NUNSU YACHISANU
✔ Mgezenge akwatira Zikani Mwambo udayamba mwachilendo ndi kuyankhula kwa makolo akuchikazi. Mawu a Gama, bambo a Zikani
∙ Zikani adamutuma zoti anene kuti iye adasangalala polowa m’banja ndipo ndi amene adapereka ganizo loti achite shazi.
∙ Ukwati wa Zikani ndi Mgezenge udalimbitsa ubale womwe udalipo kale. (Adakhala ngati nyumba yanjerwa yomwe akuyipaka pulasitala wasimenti.)
∙ Adayamika mkamwini wake Mgezenge kamba ka thandizo lomwe amapereka komanso kamba ng’ombe ziwiri zomwe adapha patsikuli zomwe nyama yake anthu ankakanika kuyitsiriza.
✔ Kumbutso: Akuchimuna sadayankhule popeza padalibepo komanso padalibe yemwe adawayimirira.
✔ Zipangizo
∙ Msemphano: Gama adauza anthu kuti Zikani adamutuma kuti anene kuti iye wakondwa polowa m’banja komanso adaonjeza kuti Zikani ndi yemwe adapereka ganizo loti achite mwambo wa shazi chonsecho Zikani sadapereke ganizoli ndipo sadakondwere nkomwe polowa m’banja.
MAPHUNZIRO
- Bodza: Gama adauza anthu kuti Zikani adamutuma kuti anene kuti iye wakondwa polowa m’banja komanso Zikani ndi yemwe adapereka ganizo loti achite mwambo wa.
- Zinthu zosalongosoka: Pamene Zikani amalowa m’banja ndi Mgezenge monga banja lachiwiri, akuchikazi padalibe komanso padalibe yemwe adawayimirira mwakuti sadayankhulepo.
NUNSU YACHISANU NDI CHIMODZI
Mkangano kunyumba kwa Mgezenge pambuyo pa ukwati
Mgezenge akanganana ndi Nagama.
∙ Mgezenge adauza Nagama kuti akatulutse katundu wake kuchipinda chachikulu chomwe amagona ndipo akalowe kuchipinda cha alendo kuti apereke danga kwa Zikani. ∙ Nagama adauza Mgezenge kuti iye ndi amene atasamukire kuchipinda chomwe azikagona ndi Zikani.
∙ Mokwiya, Nagama adatulutsa katundu wake kuchipinda chachikulu nasiya Mgezenge ndi Zikani.
Mgezenge akangana ndi Zikani.
Atatuluka Nagama zinthu izi zidachitika m’chipindamu:
∙ Mgezenge adamuyamikira Zikani ndipo adamuuza kuti amuyang’ane; asachite manyazi popeza ndi mamuna wake.
∙ Zikani adamuyankha kuti iye ndi bambo wopanda manyazi komanso iye ndi mlamu wake. ∙ Mgezenge adamuuza Zikani kuti panthawiyi sanalinso mlamu wake koma mamuna wake popeza adasinthidwa. (Chimanga akachigaya sichikhalabe chimanga.) Zikani adatsindika kuti sankafuna konse.
∙ Mgezenge adati anthu aakazi amanena zinthu zaukwati ngati sakufuna. Atamufunsira Nagama sadalole komabe adamukwatira. Zikani adakanitsitsa kuti sankamufuna Mgezenge.
∙ Pambuyo pake, Nagama adalowanso m’chipindamo nauza Mgezenge ndi Zikani kuti iye akagona m’chipinda china; Zikani akalowe m’chipinda chachikulu akayale. ∙ Zikani adatsindika kuti Mgezenge sangakhale mamuna wake pazifukwa izi:
✔ Sanayezetse magazi kuti aone ngati ali bwino kapena ayi. Mchemwali adakhala akudwala kwa nthawi yayitali koma sanali kudziwa chomwe ankadwala.
✔ Zimaonetsa kuti Mgezenge ndi Nagama amaopa kuyezetsa magazi.
∙ Zikani adauza Mgezenge kuti iye adayezetsa ndipo adamupeza ndi kachirombo koyambitsa Edzi. Apa Mgezenge adamuthamangitsa Zikani m’chipindamo.
MAPHUNZIRO M’NUNSUYI
- Kudziteteza
Zikani adatsindika kuti Mgezenge sangakhale mamuna wake pazifukwa izi: ∙ Sanayezetse magazi kuti aone ngati ali bwino kapena ayi
∙ Iye adayezetsa ndipo adamupeza ndi kachirombo koyambitsa Edzi. (Ili lidali bodza.)
2. Kusasamala
∙ Nagama adakhala akudwala kwa nthawi yayitali koma sadaganize zopita kukayezetsa magazi.
NUNSU YACHISANU NDI CHIWIRI
Zikani athawa kunyumba kwa Mgezenge
∙ Mgezenge podzuka m’mawa, sadamuone ndipo atamufunsa Nagama analinso odabwa popeza adawasiya awiriwa m’chipinda chachikulu.
∙ Mgezenge amanena kuti Zikani anakagona kuchipinda limodzi ndi Nagama pamene Nagama adawasiya awiriwa m’chipinda. Pachifukwachi, Nagama adaganiza Mgezenge adapita kukamwa mowa usikuwo.
∙ Adamusakasaka m’zipinda zonse koma sadapezeke.
∙ Anthuwo adazunguzika popeza Zikani adatuluka pamene zitseko zinali zokhoma. ∙ Nagama ndi Mgezenge adaganiza zokamuyang’ana kwa makolo ake.
∙ Mgezenge adauza Nagama kuti sangayende asanadye. Pamawu amenewa Nagama adali ndi maganizo awa:
✔ Mgezenge akudziwapo kanthu pakusowa kwa Zikani.
✔ Nkutheka kuti Mgezenge adamupha mtsikanayu ndipo ngati ndi choncho nayenso anali wokonzeka kuphedwa.
MAPHUNZIRO
- Kukwiya
✔ Nagama adakwiya pamene Mgezenge adati ayambe wadya asanapite kukamuyang‟ana Zikani kwa makolo ake mwakuti adamukalipira Mgezenge kuti ndi mfiti. Kukwiyaku kudachititsa kuti Mgezenge asinthe maganizo.
- Kusaganiza
✔ Mgezenge adauza mkazi wake Nagama kuti sangapite kukasaka Zikani asanadye. Izi Nagama adazitanthauzira kuti mamuna wakeyo amadziwapo kanthu pakuti pamene adakana zophikazo Mgezenge adalusa namuopseza kuti akadatha kumumenya.
NUNSU YACHISANU NDI CHITATU
Mkangano pakati pa makolo a Zikani ndi Mgezenge pa kusowa kwa Zikani ∙ Mgezenge ndi Nagama adapita kunyumba kwa makolo a Zikani kuti akamufufuze kumeneko komabe kunalibe.
∙ Makolo a Zikani anali odwabwa pakumva za kusowa kwa mwana wawo ndipo adatulutsa maganizo awa:
✔ Mgezenge sanayenere kukawafunsa za komwe kunali Zikani popeza anali mkazi wake, adampatsa ndipo ankakhala naye.
✔ Ngati adamupha Zikani nkutengako zizimba akadangonena.
✔ Munthu akakwatira mkazi amakhala kwa mamuna wake osati kwa makolo ake.
✔ Mgezenge sanayenere kumufunsa Nagama za Zikani pamene Zikaniyo adagona m’chipinda chimodzi ndi iyeyo.
▪ Mgezenge adauza makolo a Zikani kuti sakadakamba zoti Zikani adaphedwa pamene mtembo wake sadawuone.
▪ Mgezenge ndi apongozi ake onse awiri adagwirizana kuti akanene kupolisi za kusowa kwa Zikani.
Zipangizo
- Zifanifani
∙ Ndikamadya masamba osathira nsinjiro ndimakhala ngati mbuzi yomwe ikudya msipu. ∙ Osamangoti maso tunguluzutunguluzu ngati birimankhwe.
∙ Iwenso usangokhala ndwii ngati akukuvinira chinamwali.
- Mikuluwiko
∙ Pamudzi pakhala zitsiru mkamwini asamakulirepo mwendo: Mgezenge anayenera kupereka ulemu kwa apongozi pamene anawapeza pakhomo pawo posatengera kuti anali amphawi. ∙ Nkhuyu zodya mwana zidapota akulu: Chilichonse chomwe chidachitika pa Zikani chidakhudzanso makolo ake.
- Mvekero
∙ Tunguluzutunguluzu: kuyang’ana uku ndi uku
∙ Ndwii: kukhala osayankhula koma kumangoyang’anitsitsa
4) Msemphano
∙ Mwana akalirira fupa, muninkhe: likamuthyola dzino, ndi zake zimenezo: Zikani sadawumirire kukwatiwa ndi Mgezenge; adamuwumiriza ndi makolo ake mwakuti pamene adasowa Mgezenege ndi makolo ake anayenera kumusakasaka.
MAPHUNZIRO M’NUNSUYI
1) Kupanda ulemu
∙ Mgezenge adafika ndi ukali pakhomo pa apongozi ake komanso ankayankhula ali chilili.
2) Kusokonezeka
∙ Nagama ankakanika kuyankha mafunso atapita kwa makolo ake popeza adasokonekera ndi kusowa kwa mchemwali wake Zikani.