NUNSU YACHISANU NDI CHINAYI
Anthu akhudza maliro a Zikani ngakhale iye sadamwalire
∙ Ngakhale anthu sadaone mtembo wa Zikani, adakhulupirira kuti adamwalira. Umboni woti Zikani adamwalira
∙ Panalibe umboni weniweni woti Zikani adamwalira. Anthu adakhulupirira izi: ∙ Atsikana awiri omwe ankakhala m’nyumba yomwe alonda ankhalango adayisiya ndipo zinkamveka kuti adathawa mabanja awo ndipo m’modzi mwa iwo ankati ndi Zikani, adaphedwa ndi afisi ndipo kunali kovuta kuzindikira nkhope zawo. Matupi awo adalibe ziwalo zina.
Umboni woti atsikana omwe ankakhala m’nyumba yam’nkhalango adamwalira ∙ Patapita masiku angapo afisi adavuta m’midzi yoyandikana ndi nkhalangoyo. ∙ Sabata idatha atsikanawo asadaonekenso.
∙ Anthu adamva fungo loyipa kuchokera kunkhalango ndipo atalowa m’nkhalangomo adapeza matupi awiri ataonongeka kwambiri. Matupiwo adali a atsikana.
Umboni woti m’modzi wa atsikanawo anali Zikani
∙ Mphekesera zinamveka kuti atsikanawa ankapita ku sukulu zosiyanasiyana nkumakauza atsikana anzawo za ufulu wa maphunziro a atsikana. Izi ndi zomwe Zikani adauzanso makolo ake pamene ankamuuza zoti akwatiwe ndi mlamu wake Mgezenge. ∙ M’modzi mwa iwo ankafanana ndi Zikani.
∙ Atsikanawo atafunsidwa mayina awo, adakana kutchula powopa kuti angakawabwezere kumabanja komwe adathawa. Panthawiyi nkuti Zikani atathawa kubanja kwa Mgezenge.
Kumbutso:
∙ Malingana ndi wotsogolera mwambo wamaliro a Zikani zidali zokayikitsa ngati m’modzi mwa atsikana omwe adaphedwa ndi afisiwo anali Zikani popeza nkhope zawo zidadyedwa kotero kuti kunali kovuta kuwazindikira kuti adali yani ngakhale panali madiresi omwe anthu ankati anali a atsikanawo.
∙ Anthu adakhulupirira kuti afisiwo adali a munthu ndipo kuti mwiniyo anali Mgezenge.
∙ Mwa mwambo wake, popeza mtembo wa Zikani panalibe, amuna angapo adapita kumanda n’kukakwirira thunthu lanthochi m’dzenje lamanda poopa kuti mzimu wa malemu Zikani ungawasautse m’mudzimo.
∙ Amfumu adachitira umboni kuti Zikani anali mwana wamakhalidwe abwino.
Zikani atulukira pamaliro ake
∙ Adatulukira pamodzi ndi mzake.
∙ Mgezenge, Abiti ndi a Gama adamuona.
∙ Mgezenge adachita mantha poyesa ndi mzukwa.
∙ A Gama, bambo ake, adalimba mtima n’kumuyandikira komanso kumugwira kenako n’kuthawa.
∙ Amfumu adamuponyera dothi kuti awone ngati ndi mzukwa kapena munthu weniweni popeza mzukwa umazimirira akawuponyera dothi. Zikani sadazimirire.
∙ Atate ake, a Gama, adafuna kudziwa kuti zidatheka bwanji munthu wakufa n’kudzukanso. ∙ Iye adatsindika kuti iye simalemu ndipo pamoyo wake sadafepo; ndi mwana wa Mulungu yekha basi yemwe adadzukapo.
∙ Mgezenge adakuwa kuti mkazi wake sadafe; adali ndi moyo koma Zikani adakanitsitsa kuti sadali mkazi wake. Iye adasowa chifukwa ankamuthawa Mgezengeyo.
∙ Adanena mosaopa kuti Mgezenge ndi chidyamakanda, munthu woyipa komanso wopusa. (Adali ngati nkhuku yodzimwera mazira ake omwe popeza adamulera yekha Zikani kenako n’kumafunanso akhale mkazi wake.)
Mawu a Zikani pa nkhani ya atsikana omwe adaphedwa ndi afisi
∙ Matupi omwe adapezekawo anali a atsikana anzake omwe adathawa kumabanja okakamizidwa. Nawonso adathawa mwambo wa shazi ndi amuna adyera monga Mgezenge. ∙ Zovala zake zidapezeka ndi atsikanawo popeza sadapeze mpata wotenga zovala zawo pamene ankathawa kumabanjako mwakuti Zikaniyo ndiye adawabwereka zake. ∙ Atsikanawa, Sibongile ndi Malita, adaphedwa ndi afisi atangochapa zovala zawo. Iye ndi mnzake, Chisomo, adapulumuka popeza adathawira kutali atangomva phokoso la afisiwo. Iwo adathawira kwa mayi wina wopemphera yemwe adawalimbikitsa kupempherera mizimu ya anzawo awiriwo.
∙ Atamva kuti anthu akulira maliro ake, iye adabwera mwansanga kuti anthu adziwe zoti iye adakali moyo.
Tsoka la mnzake wa Zikani (Chisomo Mwayikale)
∙ Makolo ake ankakongola ndalama kwa munthu wina wolemera dzina lake Mwenekuchanya. ∙ Atalephera kubweza ndalamazo, makolowo adagwirizana ndi Mwenekuchanya kuti Chisomo akhale mkazi wake wachinayi ngakhale anali wachichepere kwambiri (ali ndi zaka zisanu).
∙ Makolowo adakamupereka kwa njondayi (Mwenekuchanya) ali sitandade 7. Mwambowu umenewu umatchedwa “Kupimbila” kapena “Kupawila”.
∙ Iye adathawa tsiku lomwelo ndipo adakwera basi ngakhale adalibe ndalama. Atawafotokozera anthu zomwe zidamchitikira, adamuthandiza. Iye ankati akupita kwa amalume ake kuboma ngakhale kuti komwe ankalowera sankakudziwa. Mwamwayi adakumana ndi Zikani atangotsika basi ndipo adayamba kukhalira limodzi.
Mawu a amfumu atamva nkhani ya Chisomo
∙ Atamva izi adati adachita manyazi nati sadayenere kuloleza ukwati wa Zikani kuti uchitike. ∙ Adauza anthu onse kuti miyambo yina n’kutheka idali yabwino pachiyambi koma anthu adayisokoneza. N’kuthekanso makolo ena anali adyera. Miyambo ina mwina idayamba makolo atasauka.
∙ Adalamula kuti miyambo monga hlazi ndi chimeta masisi itheretu m’mudzimo.
Mgezenge ayambitsa chisokonezo.
∙ Iye adatsindika zomutengabe Zikani kukhala mkazi wake ngakhale zikadavuta motani. ∙ Adati anthu ena adadya ndalama zake choncho adayenera kubweza.
∙ Mgezenge adati miyamboyo ikamatha, iye akhala atamutenga mkazi wake, Zikani. Kupanda kutero akadavulaza munthu wina. Iye adaopseza kuti kusintha miyambo kusayambire pa iyeyo.
MAPHUNZIRO M’NUNSUYI
- a) Ana adazunzika kamba ka umphawi wamakolo
∙ Makolo a Chisomo adamukwatitsa ali wachipere kwa mkulu yemwe adakanika kumubwezera ndalama zake atakongola. Chisomo adathawira kunyumba ina yomwe adayisiya alonda ankhalango. M’nyumba m’menemu ndi momwe anzawo ena awiri adaphedwa ndi fisi.
∙ Zikani adathawa ku banja lokakamizidwa ndipo ankakhala m’nyumba ina yomwe adayisiya alonda ankhalango.
- Chisoni
∙ Anthu omwe adamva nkhani ya Zikani adamuthandiza kuti ulendo wake upitirire. c. Chikondi
∙ Zikani adawabwereka zovala atsikana omwe adaphedwa ndi afisi popeza pobwera kwawo sadatenge zovala.
- Nkhanza
∙ Makolo a Zikani ndi Chisomo adakwatiwitsa ana awo mowakakamiza asadafike pamsinkhu woyenera kutero.
- Kudziteteza
∙ Zikani ndi Chisomo adathawa ku mabanja okakamizidwa komanso adathawa afisi olusa napita kwa mayi wina komwe ankapempherera mizimu ya anzawo awiri amene adaphedwa ndi afisiwo.
- Kulongosola/Kuwongola zinthu
∙ Amfumu adathetsa mwambo wa shazi/ mbirigha/ isakulwa/ chimeta masisi g. Kuipa mtima/Kusamva
∙ Mgezenge adalimbikira zoti amutengabe Zikani ngati mkazi chonsecho amfumu adalengeza kuti adathetsa mchitidwe wa shazi m’mudzi mwawomo.
NUNSU YAKHUMI
Sukulu ipindulira Zikani, Funsani ndi Chisomo
∙ Anthu atatuwa adaphunzira ndipo adali pantchito. Chisomo ankagwira ntchito limodzi ndi Zikani m’bungwe la “Mtetezi wa Mwana” lomwe adayambitsa Zikani. Macheza a Chisomo ndi Funsani
∙ Chisomo adafika kunyumba kwa Funsani ndi Zikani kuti akapereke lipoti lantchito yomwe adakagwira ku esiteti ina komwe zimamveka kuti mwini wake ankagwiritsa ntchito ana aang’ono.
∙ Chisomo adasankha kupatsidwa madzi m’malo mwa chakumwa chilichonse ndipo adati:
✔ Zakumwa zisamakhale ndi shuga wambiri komanso zothiramo zosadziwika.
✔ Agogo ake adawadula mwendo ndipo matenda ashuga ndiwo adali gwero.
✔ Funsani adauza Chisomo kuti kusankha madzi isakhale njira yopulumutsira makobili pozemba zakudya zabwino popeza atsikana makobili amathera m’mutu.
Macheza a Chisomo, Zikani ndi Funsani
∙ Chisomo adauza Zikani kuti adabwera kudzamuuza m’mene adayendera ku esiteti komwe kudamveka kuti mwini wake akugwiritsa ntchito ana aang’ono.
∙ Adakumbutsana zakale ndipo adakamba zotsatirazi:
∙ Akadapanda kuchita khama bwenzi panthawiyi atakalamba; sakadaphunzira monga adachitira panthawiyi.
∙ Sukulu ndi yabwino popeza idathandiza kuti ayambitse bungwe la “Mtetezi wa Mwana”. ∙ Matenanti a ku esiteti ina adakadandaula ku ofesi ya Zikani ndi Chisomo. M’modzi mwa matenantiwo adali ndi ana asanu ndi awiri. Onsewo amagwira ntchito pa esiteti pomwepo. Anawo ankavutika popeza ankagwira ntchito zolemetsa komanso sankapita kusukulu.
∙ Funsani adakumbukira m’mene ankagwirira ntchito kugolosale kwa a Mgezenge: amagwira ntchito n’kumalipidwa zovala zakale.
∙ Zikani adagwirizana ndi Funsani kuti Zikani adachita bwino kuthawa kwa a Mgezenge popeza a Mgezenge adali kudwaladwala mwakuti adaonda kwambiri ndipo Nagama adamwalira. Chuma chonse chidatha: ng’ombe zidathera malipiro asing’anga, golosale adatseka.
∙ Zikani adalakalaka akadathandiza makolo ake koma panthawiyi anali atamwalira. Zotumphuka pa macheza a Zikani, Funsani ndi Chisomo kunyumba kwa Funsani ndi Zikani
∙ Chilonda chimavuta kupola ndi matenda a shuga.
∙ Nsima yamgayiwa ndi yabwino popeza imakhala ndi madeya ofunika m’thupi komanso ili ndi sitalichi ndi faiba wambiri. Nsimayi imathandiza kupewa matenda amtima ndi khansa.
∙ Patapita nthawi Zikani adakwatiwa ndi Funsani
∙ Zikani adayambitsa bungwe la “Mtetezi wa Mwana” ndipo anali bwana wamkulu. Chisomo adali mthandizi wake.
∙ Azungu a mishoni ndi omwe adalipirira sukulu Funsani mpaka ku yunivesite ndipo adamupezeranso ntchito. Azunguwa adapita kumwambo wolandira madigiri monga makolo a Funsani. M’modzi mwa azungu amishoniwa anali Bambo Alfred.
∙ Eni esiteti akalemba bambo ntchito, ndiye kuti banja lonse limagwira ntchito yomweyo. ∙ Eni esiteti anali oyipa pazifukwa izi:
✔ Ndi iwo okha amene amagula fodya wamatenanti.
✔ Amagula fodya wamatenanti pa mtengo wozizira.
✔ Amalamula mtengo wogulira fodya wamatenanti awo.
✔ Amawapatsa matenanti zakudya zosakwanira.
∙ Makolo a Zikani komanso Funsani anali atamwalira panthawiyi.
∙ Zikani ndi mamuna wake Funsani ankacheza moserewulana.
∙ Zikani adanena moserewula za ntchito yakale ya Funsani: “Ikakhala golosale yako ija muli akangaude okhaokha.”
∙ Funsani adanena moserewula za ukwati wa Zikani ndi Mgezenge: “Amuna ako aja anali wovuta kwambiri.”
Zipangizo
- Zining’a
o Fisi asanathyole khola: asanagonane
o Anatsikira kulichete: Anamwalira
o Ali mafupa okhaokha: Adaonda kwambiri.
o Ndi bwenzi wa mphasa: Akudwaladwala.
o Onse anatsogola: Anamwalira.
o Pamtengo wozizira: Pamtengo wotsika
o Makobiri akuthera m’mutu: Makobiri akuthera kukonza tsitsi.
o Tawonjola ana ambiri: Tapulumutsa ana ambiri.
- Chifanifani
∙ Ndinkakhalira mphanthi ngati nsikidzi.
∙ Ndinkakhala movutika kwambiri.
MAPHUNZIRO M’NUNSUYI
1) Chikondi
∙ Azungu amishoni adamutenga Funsani makolo ake atamwalira n’kumakhala naye ndipo adamulipirira sukulu mpaka ku yunivesite. Atatsiriza ku yunivesite, adamupezera ntchito.
2) Nkhanza
∙ A Mgezenge ankamugwiritsa ntchito Funsani ku golosale koma ankamulipira zovala zokutha.
∙ Eni esiteti ankawachitira nkhanza zosiyanasiyana matenanti awo.
3) Kukonda/Kusamala ntchito
∙ Zikani adafuna kumva kaye m’mene Chisomo adayendera ku esiteti komwe kudamveka kuti mwini wake akugwiritsa ntchito ana aang’ono. Adachita zimenezi atangofika kuchokera kuntchito, asadapume ngakhale mwamuna wake Funsani adamuuza kuti ayambe wapuma.
4) Kudziwa zinthu
∙ Chisomo adachenjeza Funsani pa nkhani ya zakumwa zashuga wambiri komanso zothiramo zosadziwika. Adamufotokozeranso za matenda a shuga ndi momwe adachititsira kuti agogo ake adulidwe mwendo. Mtsikanayu adafotokozanso za kufunika kwa nsima yamgayiwa.
NUNSU YAKHUMI NDI CHIMODZI
Zikani ndi Chisomo ku esiteti
∙ Adafika pakhomo pa a Kamwendo atavala zitenje ndi mipango ndipo adalonjeredwa. Bambo Kamwendo anali tenanti.
∙ Ataona mwana wina wa a Kamwendo atasenza mtolo wankhuni waukulu kuposa msinkhu wake, Zikani adafunsa modabwa popeza mnyamatayo anayenera kukhala ali kusukulu panthawi monga imeneyi.
∙ Zikani adawafunsa chiwerengero cha ana omwe adali nawo komanso momwe amaliwonera tsogolo lawo ndipo a Kamwendo adayankha izi:
✔ Ali ndi ana asanu ndi awiri.
✔ Mwana amene adadutsa ndi mtolo anali wachinayi.
✔ Ana ena anali kuganyu yopalira.
✔ Mwana wawo wamkazi adapita kutauni kukagulitsa masamba.
✔ Ana awiri aang’ono adaperekeza mayi awo kuchigayo.
✔ Anawo sakadamapita kusukulu tsiku lililonse popeza sakadapezako chakudya.
✔ Amawaphunzitsa anawo momwe angadzakhalire akadzakula; amawaphunzitsa ntchito.
Zomwe Zikani adaunikira a Kamwendo koma sadazimvetse
∙ Ntchito zomwe ana aang’ono amagwira pakhomo zizifanana ndi msinkhu wawo. ∙ Kholo logwiritsa ana ntchito zoipa litha kumangidwa.
∙ Dziko lidasainira mgwirizano pa 17 June 1999 wa “Mitundu ya Ntchito Zoyipitsitsa kwa ana” “Worst Forms of Child Labour Convention” womwe gawo 3 limakamba za ntchito zomwe zingathe kuononga moyo wamwana.
∙ Zimaonetsa kuti a Kamwendo sakulera bwino ana: samawapititsa kusukulu nthawi zonse, amawagwiritsa ntchito zomwe zikadatha kuononga moyo wawo. Chitsanzo chinali cha mwana amene adadutsa ndi mtolo wankhuni yemwe amaoneka kuti adakakamizidwa kutero.
∙ A Kamwendo adawathamangitsa Zikani ndi Chisomo ponena kuti sangawalamulire za ana awo poti iwo adalibe ana komanso sankadziwa chilichonse chokhudza mwana.
MAPHUNZIRO M’NUNSUYI
- Kusazindikira
∙ A Kamwendo ankagwiritsa ntchito ana awo mobzola msinkhu wawo komanso ankawajombetsa kusukulu nthawi zambiri, kotero samadziwa kufunika kwa sukulu. 2. Kusaphunzitsika
∙ A Kamwendo sadamvetse kuti kugwiritsa ana awo ntchito mopitirira mulingo ndi kuwachitira nkhanza. M’malo mwake iwo adatanthauzira kuti Zikani ankawauza kuti anawo asamagwire ntchito mwakuti adamulalatira namuopseza kuti achoke pakhomopo asadamukhwiyitsire agalu.
- Kuteteza
∙ Zikani adayambitsa bungwe la “Mtetezi wa Mwana” kuti awonjole/apulumutse ana kumavuto a kugwiritsidwa ntchito zosagwirizana ndi msinkhu wawo komanso kusapita kusukulu.
NUNSU YAKHUMI NDI CHIWIRI
Mgezenge kunyumba kwa Zikani ndi Funsani
Adafika akudziyankhulira zinthu izi:
∙ Abale ake onse adamwalira.
∙ Adali wolemera koma zinthu zonse (mbuzi, ng’ombe, sitolo, nkhuku ndi nkhunda) zidatha.
∙ Pa esiteti yake boma lidamanga sukulu ndipo ndalama zachipukutamisozi zidatha kalekale.
∙ Msewu womwe udadutsa m’munda mwa apongozi ake umalunjika kusukulu. ∙ Anthu akamuona, ankamutcha wamisala kapenanso sing’anga.
∙ Adaganiza zopempha malo ogona panyumba ina yomwe sankadziwa kuti inali ya Funsani ndi Zikani.
∙ Adachita odi ndipo Chisomo Mwayikale ndiye adamulonjera.
∙ Adamuuza Chisomo kuti akawauze eni nyumba kuti iye ankafuna malo ogona; tsiku lotsatiralo azipita.
∙ Chisomo adauza Mgezenge kuti mnzakeyo adavomera kuti amusunga ndipo akagona kunyumba yogona anyamata. Adamutengera Mgezenge kunyumba yayikulu kuti akamuone.
∙ Funsani adawazindikira a Mgezenge ndipo Chisomo adawadziwanso koma iwo sadawazindikire.
∙ Zikani adawadziwitsa a Mgezenge kuti iyeyo ndi Zikani ndipo mamuna wake ndi Funsani.
∙ Mgezenge adapepesa.
∙ Funsani ndi Zikani adakhululukira Mgezenge pa zonse zomwe adawachitira. ∙ Zikani adauza wantchito wake kuti awasamalire a Mgezenge ku chipinda cha alendo. ∙ Chisomo adatsanzika n’kumapita kwawo.
Zipangizo Zining’a
- a) Onse kutha psiti: Onse kumwalira
- b) Ndiwone msana wanjira: Ndizipita
MAPHUNZIRO M’NUNSUYI
- Kunong’oneza bondo
∙ Mgezenge adadziyankhulira yekhayekha modandaula kuti kunja kuyanja lichero. Iye adali ndi chuma koma chidatha chonse. Abale ake onse adamwalira ndipo anthu akamuona akumunena kuti ndi wamisala komanso sing’anga.
- Chuma ndi mchira wakhoswe sukhalira kupululuka
∙ Mgezenge adali ndi chuma chambiri ndipo ankachitira anthu nkhanza. Adagwiritsa ntchito chuma chake kuti akwatire mlamu wake Zikani. Chuma chonsecho chidatha ndipo adasauka mwakuti anthu akamuona ankamuyesa wamisala.
- Kukhululuka
∙ Zikani ndi mwamuna wake Funsani adamukhulukira Mgezenge ngakhale adawachitira zoyipa. Atafika pakhomo pawo atasaukiratu komanso atadwalika kwambiri n’kupempha malo ogona, anthu awiriwa adamusamala Mgezenge.
- Kusayiwala
∙ Funsani adakumbukira zonse zomwe Mgezenge adachitira Zikani ndi iye yemwe. Iye adati Mgezenge adali katswiri pogwiritsa ana ntchito yakalavula gaga, iye adali kapolo wake, adali chidyamakanda ndipo Zikani adatsala pang’ono kufa kamba ka iye.
NUNSU YAKHUMI NDI CHITATU
Mgezenge adzikhweza pakati pa usiku
∙ Wantchito wa Funsani ndi Zikani adayimbira foni Funsani kuti anamva phokoso losonyeza kuti munthu ankaphupha mobanika ndipo atathamangira m’chipinda momwe adagona Mgezenge, adapeza atadzimangirira ndi chingwe choyanikapo zovala.
∙ Funsani ndi wantchito adathandizana kuswa chitseko ndipo adampeza Mgezenge asadafe. Adayitanitsa makiyi a galimoto kuti amutengere kuchipatala.
Chipangizo Mkuluwiko
∙ Chifundo chidapha nkhwali: Chisoni chomwe Funsani ndi Zikani adachitira Mgezenge pompatsa malo ogona chikadawabweretsera mavuto pamene Mgezenge adadzimangirira.
MAPHUNZIRO M’NUNSUYI
∙ Kudziweruza: Mgezenge adadzimangirira kuti afe popeza kudali kovuta kuti akhale m’nyumba mwa Funsani ndi Zikani poganzira nkhanza zomwe adawachitira pamene iye adali ndi chuma.
∙ Moyo ndi wozungulira: Mgezenge adakapempha chithandizo kunyumba kwa Funsani pamene m’mbuyomo Mgezenge ndi amene adalemba ntchito Funsani yogulitsa m’golosale mwake.
MAKHALIDWE A BAMBO MGEZENGE
1) Wandeu
∙ Akumuponyera chibakera Nagama chifukwa choti sakugwirizana ndi maganizo oti akahale awiri
∙ Akwenya Funsani pa khosi chifukwa chopezeka ndi cholembera mu thumba lake. Iwo amaganiza kuti waba mu golosale yawo yomwe iye akuwagulitsira ngati wantcito 2) Wosaganizira ena (wosalabadira mavuto a anzake)
∙ Mayamiko awabweretsera nkhuni ndipo ayembezera kuti apatsidwe ndalama kuti akagule sopo yochapira zovale kuti azipita bwino ku sukulu. A Mgezenge aumuuza kuti akathana ndi abambo ake osamupatsa kena kalikonse
3) Waukali
∙ Akalipira Nagama pa china chilichonse chomwe atalakwitse
∙ Tsiku lina pochapa, Nagama apempha Zikani kuti awathandize kuchapa. Koma amulangiza kuti asawauze a Mgezenge kuopa kukalipiridwa
4) Wachipongwe
∙ Amusiyitsa ntchito Funsani chifukwa chotseka shopu. Iye anatseka shopu chifukwa anapita ku chipatakla atadwala malungo
5) Wopanda ulemu
∙ Apita kwa apongozi ake (Abiti ndi Gama) nawawuza kuti abwera kudzangosiya mwana wawo. Akupanga izi asanakhale ndi pansi.
MAKHALIDWE A ZIKANI
- Wozindikira
∙ Awuza a Mgezenge kuti kuti sangakhale mkazi wawo popeza ndi mlamu wawo ∙ Awuza a Mgezenge kuti sangagonane asanakeyedzetse magazi
- Wolimba mtima
∙ Awuza makolo ake kuti iyeyo sangakhale mkazi wa Mgezenge
∙ Awuza a Mgezenge kuti iye ndi mlamu wawo osati mkazi wawo
- Wachisoni
∙ Amalira pa ukwati chifukwa chosafuna kuti akhale mkazi wa Mgezenge d. Wa chikondi
∙ Ayambitsa kalabu yotchedwa Mtetezi wa Mwana ndi cholinga choteteza ana omwe akuponderezedwa mu ma esiteti ndi malo ena
- Wokhululuka
∙ Anakhululukira a Mgezenge pa nkhanza zomwe ankanamuchitira pamene anapita kunyumba kwawo pofuna malo ogona
MFUNDO ZIKULUZIKULU
- Miyambo
∙ Mwambo wopereka ma digiri kwa ophunzira
∙ Mwambo wa ukwati wa Zikani ndi Bambo Mgezenge
∙ Mwambo wa maliro a Zikani
∙ Mwambo wa chikhalidwe chamakolo: kupereka Zikani kwa mlamu wake, Mgezenge, mbiriya
- Zikhulupiriro
∙ Mulungu: Zikani anati makolo ake anali ku mwamba ndi mulungu. Mzimayi wopemphera adamutenga Zikani pomwe anathawa a Mgezenge
∙ Ufiti: Abiti ndi Gama amakhulupirira kuti a Mgezenge amupha Zikani kuti alemere. ∙ Mizimu: pa mwambo wa maliro anati, mu dzenje akatayamo thunthu la nthochi ndi kulikwirira kuopa kuti azimu angaphe munthu wina mu mudzimo. Zikani anati mizimu wa Sibongire ndi Malita (atsikana odyedwa ndi afisi kunkhalango) ukhala mafuta onyeketsera miyambo yonunkha ya makolo awo
∙ Makhwala a zitsamba: Mlamu wa mfumu anasiya kuona chifukwa choyambana ndi mfumu. Atachira anaonanso zodabwitsa kamba koti sanamvere malangizo oti asakagone ndi mkazi wake usikuwo. Panopa akufunafuna sing’anga kuti awapatse mankhwala a zitsamba.
- Umphawi
∙ Bambo Gama adapereka Zikani kwa Mgezenge ndi cholinga choti azithandizidwa bwino ∙ Makolo a Chisomo anakongola ndalama kwa mkulu wina wolemera. Chifukwa chosowa ndalama yokabweza, anakapereka Chisomo kwa mkuluyo ngati malipiro
∙ Zikani asoweka kokatenga ndalama yopereka ku sukulu ya chitukuko ndinso yogula buku lomwe wophunzira wina anamubera.
∙ Mayamiko analibe kotenga sopo yochapira zovala zake zakusukulu. Zotsatira zake akujomba kusukulu. Akudikirira kuti akagula sopo a Mgezenge akumulipira ndalama pamene wawabweretsera nkhuni. Komabe sanamutse kena kalikonse
∙ A Mgezenge asawuka kwambiri. Chumna chawo chonse chiwathera. Mapeto ake akuyendayenda mpaka afika ku nyumba ka Funsani ndi Zikani