NUNSU YOYAMBA
Bonzo ndi Jubeki athawa kundende
Chomwe zidachititsa kuti Bonzo ndi Jubeki amangidwe
∙ Adathyola banki ndipo adaba ndalama zambiri zokwana 200 million kwacha. Zomwe zikadachititsa kuti Bonzo ndi Jubeki agwidwe
∙ Ganizo la Bonzo loti pothawa kundende avale nsapato: mdidi wawo ukadamveka ∙ Mkuwo wa Bonzo ataponda msomali: atajowa mpanda, Bonzo adakafikira kuponda msomali ndipo adalira ngati mwana wamng’ono
Kusiyana kwa Bonzo ndi Jubeki ndi Nyapala pamilandu yawo
∙ Bonzo ndi Jubeki adathyola banki naba ndalama zambiri; choncho adali akaidi abwinoko. ∙ Nyapala adagwirira kamwana kakang’ono choncho anali mkaidi wachabechabe.
Maganizo a Bonzo ndi Jubeki pa chitetezo cha ndalama zomwe adabisa ∙ Bonzo anali ndi chikaiko ngati ndalama zomwe adaba nkubisa kumanda zidalipobe popeza panali patapita zaka ziwiri chikwirireni ndalamazo choncho china chake chikadatha kuchitika.
∙ Jubeki adatsindika kuti palibe yemwe akadawadziwa malowo popeza anthu adasiya kugwiritsa ntchito mandawo.
∙ Bonzo adatsimikiza nawo mfundoyi ponena kuti palibe yemwe akadadziwa malo omwe anali pamtunda wa masitepe 77 kuchokera pamtumbira wotsiriza komanso palibe yemwe akadakumba kumanda.
∙ Jubeki adakayikira zinthu zotsatirazi:
✔ Munthu akadatha kuswa mphanje kapena kutsekula munda pamalopo. ✔ Munthu akadatha kumangapo nyumba.
∙ Ngakhale Jubeki anali ndi nkhawa zimenezi, adalinso ndi chikhulupiriro kuti zimenezi sizingachitike kumanda
Umboni woti Bonzo ndi Jubeki adali oopsa komanso adachita umbanda ndi umbava kwa nthawi yayitali
∙ Paulendo wothawa kundende, ngakhale munali mumdima, Jubeki adakwanitsa kudziwa chinthu choopsa chomwe chinali patsogolo pawo chomwe chikadatha kuwavulaza monga dzenje.
∙ Jubeki adathawapo apolisi chipolopolo chili pantchafu apolisiwo atamuwombera. ∙ Jubeki adagwira ntchitoyi (umbava ndi umbanda) kwa zaka zoposa makumi awiri. ∙ Bonzo adagwira ntchitoyi kwa zaka khumi ndi mphambu zisanu ndi ziwiri.
Zomwe Bonzo ndi Jubeki adayenera kuchita kuti asazindikiridwe komanso asagwidwe ∙ Adayenera kupeza zovala zina mwachangu popeza Malaya akundende omwe anali atavala panthawiyi akadagwidwa nawo poti ngakhale munthu wongodziyendera akadatha kuwadabwa nkuwagwira.
Kumbutso
∙ Bonzo ndi Jubeki adagwirizana zokathyola nyumba yomwe adayiona pafupi n’kulowa kuchipinda cha makolo kuti akapeze zovala zachimuna.
∙ Jubeki adauza Bonzo kuti Nyapala adali wopusa zedi popeza adagwirira mwana pamene azimayi adalipo ambirimbiri omwe akadatha kuwafunsira.
∙ Kugwirira ana ndi ufiti ndipo anthu amachita zimenezi pofuna zizimba.
Zipangizo
- Zining’a
∙ titaya bomwetamweta: titaya mwayi wopezapeza
∙ tinapakula : tinaba
∙ walasa : walunjika pa zomwe ndimaganiza
∙ kamatekenya : munthu wamatekenya
- Zifanifani
∙ Unafuula ngati mwana wamng’ono: Unafuula mokweza kwambiri kamba ka ululu. ∙ Ukuyenda ngati kamatekenya: Ukuyenda motsimphina kamba ka ululu wakuphazi. 3. Chifaniziro/Chizindikiritso
∙ Misomali ndi mayenje: Chizindikiritso cha chilango ndinso kugwidwa 4. Msemphano
∙ Bonzo ndi Jubeki ndi mbala zoopsa zomwe zathawa kundende koma zinali ndi chikhulupiriro kuti zikapulumuka monga mbala yomwe inapulumutsidwa pamtanda ndi Yesu nthawi yothaitha.
- Kalosera
∙ Jubeki adakayikira kuti munthu akadatha kuswa mphanje kapena kutsekula munda pamalo pamene adafotsera ndalama kapena munthu akadatha kumangapo nyumba. Izi zidachitikadi. Pamene anthu awiriwa adathawa kundende adakapeza pamalo pamene adakwirira ndalama patamangidwa chinyumba chachitali.
Maphunziro m’nunsuyi
- Anthu akuba saopa
∙ Bonzo ndi Jubeki atathawa kundende adaganiza zothyola nyumba ina kuti apeze zovala zina kuti asinthe.
- Kulimba mtima
∙ Bonzo ndi Jubeki adathawa kundende.
∙ Jubeki adathawa apolisi chipolopolo chili pantchafu atamuwombera.
- Kuganiza mwakuya
∙ Bonzo ndi Jubeki adaganiza zokabisa ndalama kumanda.
∙ Bonzo ndi Jubeki adaganiza zoti apeze zovala zina mwachangu poopa kugwidwa ndipo adagwirizana zothyola nyumba ina nkulowa kuchipinda chamakolo kuti akapeze zovala zachimuna popeza kuchipinda kwa ana sakadapeza zomwe amafuna.
NUNSU YACHIWIRI
Ubwenzi wa Khoswe ndi Anne
∙ Aliyense mwa awiriwa anali pabanja.
∙ Anthu awiriwa amapeza danga locheza pamene mamuna wa Anne, Goli, anali mgulu la anthu okagwira ntchito usiku komanso naye Khoswe amakagwira ntchito yake usiku (kuyang’anira akayidi).
∙ Macheza awo amachitikira kunyumba kwa Goli usiku.
∙ Khoswe amakhotera kunyumba kwa Anne akamapita kuntchito.
∙ Awiriwa ankalimba mtima nkumacheza mpaka usiku zedi popeza Goli amati akapita kuntchito ankabwerako 7koloko m’mawa ndipo kunali kovuta kuti wapolisi athawire kuntchito.
∙ Tsiku lina Anne adamuphikira Khoswe zakudya zomwe Khosweyo adaziyamikira mpaka kunyoza mkazi wake ponena kuti Anne pazophika adatha mayunivesite pamene mkazi wake anali adakali ku pulayimale.
Chipwirikiti kunyumba kwa Goli
∙ Akuba adabwera nasolola zovala zomwe zinali pafupi ndi zenera lakuchipinda komwe Khoswe anali kucheza ndi Anne. Akubawa adasololanso yunifolomu ya Khoswe ya pulizoni. ∙ Khoswe adatchayiridwa thenifolo ndi mzake wakuntchito yomudziwitsa kuti akayidi awiri, Bonzo ndi Jubeki, adathawa.
∙ Anne ndi Khoswe adakanika kufuula kuti apolisi awathandize atazindikira kuti m’chipindamo munabwera akuba poopa kuti akadawululika. Anthu awiriwa ankaopa kuyatsa getsi m’chipinda momwe ankacheza poopa kuti anthu anyumba yoyandikana ndi ya Goli komanso alonda a Goli akadakanena kwa Goli.
∙ Anne adakayikira akayidi omwe adathawa kundende kuti ndi amene adaba zovala kudzera pazenera pamene iye ndi Khoswe adatanganidwa ndi kucheza.
∙ Khoswe adavala zovala za Goli zomwe zidali zazikulu zedi ndipo adatuluka n’kumapita.
Mawu ofunika kuwaona bwino
- Khoswe analidi khoswe.
∙ Khoswe ankamuzembera Goli nkumachita ubwenzi ndi mkazi wake Anne chimodzimodzi m’mene amachitira khoswe m’nyumba pozembera mwininyumba n’kumadya katundu wake.
- Kutchena kapena kukwana kwa zovala ndi pamtendere.
∙ Khoswe adavala zovala zazikulu zedi zamamuna wake wa Anne popeza adazingwa pamene akuba adathawitsa yunifolomu yake yakuntchito m’mene iye ankacheza ndi Anne.
MFUNDO ZIKULUZIKULU
- Chimasomaso
∙ Khoswe anali pabanja koma anali kuzemberana ndi Anne mkazi wa Goli. ∙ Anne anali pabanja koma anali kuchita ubwenzi ndi Khoswe yemwe anali pabanja. 2. Mantha
∙ Khoswe ndi Anne adakanika kuyatsa getsi lam’chipinda momwe ankacheza pamene amafuna kuti ayang’ane zovala za Khoswe popeza anali kuopa kuti anthu oyandikana nyumba ndi ya Goli komanso alonda a Goli akadakamuuza bwana wawo.
∙ Khoswe ankamuopa Goli: ankati ndi wamphamvu zedi mwakuti akangomugwira ndi Anne mphamvu zonsezo zikadathera pa iyeyo.
∙ Anne adaganiza zokuwa kuti kudabwera akuba pakutuluka kwa Khoswe m’nyumbamo popeza ankaopa kuti akadaululika.
∙ Anne ankamuopa mamuna wake Goli. Pamene Khoswe adamuuza zoti adzayankhe mamuna wake akabwera pa zakusowa kwa diresi yake yovala pogona komanso zovala za mamuna wakeyo adati asunga mayankho koma adaonjeza kuti Goli monga wapolisi amafunsa mafunso akafukufuku kwambiri.
Matanthauzo amawu
∙ Uchidzete : uchitsiru
∙ Duwa, nyale, dzuwa, ngale : mkazi wokongola
NUNSU YACHITATU
Kugawana zovala zakuba
∙ Bonzo ndi Jubeki adazindikira kuti zovala zomwe adaba zinali yunifolomu ya wogwira ntchito ku pulizoni komanso diresi yovala pogona.
∙ Jubeki adauza Bonzo kuti iyeyo (Jubeki) ndi yemwe atavale yunifolomuyo popeza adaswa zenera adali iye ndipo kuti Bonzo avala diresi.
∙ Anthu awiriwa adagwirizana kuti yunifolomu yaukaidi ayitaye pobisika poopa kuti kukadakhala kosavuta kuti awalondole.
Milandu ya bonzo ndi jubeki ndi zilango zake
∙ Kuthyola banki, kuba ndalama m’banki komanso kuzimbayitsa ndalama. ∙ Bonzo ndi Jubeki adaba ndalama zokwana K200,000,000.
∙ Mlandu uliwonse unali ndi zaka zake zoti nthu awiriwa akakhale kundende komanso aliyense mwa iwo adagamulidwa kuti akakhale kundende kwa zaka khumi.
MFUNDO ZIKULUZIKULU
- Kuganiza mwakuya
∙ Jubeki adauza Bonzo kuti yunifolomu yaukaidi ayitaye pobisika popeza kuyitaya pooneka kukadachititsa kuti alondoledwe mosavuta.
Zipangizo
Mkuluwiko
∙ M’mphechepeche mwa njovu sapitamo kawiri: Bonzo ndi Jubeki sanayenera kuthyolanso nyumba kuti apeze zovala zina popeza akadatha kugwidwa.
Chining’a
∙ Makhumutcha Anthu olemera/andalama
NUNSU YACHINAYI
Mkazi wa khoswe adabwa ndi mamuna wake
∙ Anzake a Khoswe adabwera kunyumba namuuza kuti mamuna wake sanali kuntchito. Iye adadabwa nazo popeza Mwamuna wakeyo adapita kuntchito komweko atavala yunifolomu. ∙ Mwamuna wakeyo adatulukira kunyumba nthawi yomwe anayenera kukhala kuntchito. ∙ Khoswe adatulukira kunyumba atavala zovala zachilendo: chimalaya chachikulu komanso chibuluku chachikulu.
∙ Khoswe adamuuza mkaziyo kuti yunifolomu adamutsomphola akaidi omwe adathawa panthawiyi iye ali kuchimbudzi chapanja.
∙ Khoswe adaoneka odabwa pamene anzake adamuyimbira foni yomudziwitsa kuti akaidi athawa. Abwana a Khoswe ndiwo adamudziwitsa mkaziyu.
MFUNDO ZIKULUZIKULU
- Bodza
∙ Khoswe adanamiza mkazi wake kuti iye anali kuntchito, adatsekula m’mimba, anali kuchimbudzi chakunja pamane akaidi ankathawa ndipo akaidiwo adamutsomphola yunifolomu ali kuchimbudziko, chonsecho Khoswe anali kuchibwenzi (kwa Anne) komwe yunifolomu yake idabedwa ndi akaidiwo.
- Kuopseza
∙ Khoswe adaopseza mkazi wake kuti amumenya ngati sasiya kumufunsa.
Zipangizo: Zining’a
∙ Mawu oluma: mawu aukali
∙ Mvumbi wazibakera: zibakera zobwera motsatizana
NUNSU YACHISANU
Zokambirana za Goli ndi mkazi wake
Bodza la Anne kwa mamuna wake Goli
∙ Adamuuza kuti akuba adaphwanya zenera mpaka kuba iye ali mtulo ndipo akumulota iyeyo (Goli). Adaonjezanso kuti apolisi amapereka chitetezo kudziko kusiya okondedwa awo kunyumba.
∙ Adagwetsa mphwayi mamuna wake pomuuza kuti zojambula zidindo za zala za omwe adaba m’nyumbamo angozisiya popeza zipangizo zojambulira zinali zodula.
Mayankho a Goli kwa Anne mkazi wake
∙ Goli adamuyankha mkazi wakeyo, Anne, kuti kunyumbako adabwerera ntchito komanso kupereka chitetezo ndi ntchito yomwe adafunsira.
∙ Adatsimikiza zoti atenga zidindo za zala zakumanja za akubawo ndipo monga wapolisi ayesetsa kuti akubawo agwidwe. Adafotokozanso kuti ngati si akaidi omwe adathawa ku pulizoni omwe adaba kunyumbako, adayenera kupeza munthu aliyense yemwe zidindo za zala zake zikadapezeka kuchipindako.
NUNSU YACHISANU NDI CHIMODZI
Bonzo ndi Jubeki agwidwa
∙ Adafika pamanda pamene adakwirira ndalama zomwe adaba kubanki koma adadabwa ataona kuti padamangidwa chinyumba chachitali ndipo sakadakwanitsa kuchigwetsa kuti afukule ndalamazo.
∙ Mlonda wapamalopo adatchayira lamya apolisi ndipo mkulu wawo (Insipekitala Goli) adatulukira mwamsanga nawauza anthu awiriwa (Bonzo ndi Jubeki) kuti akuwamanga pa mlandu wopezeka malo olakwika usiku.
∙ Chikhothi cholembedwa “Police” chidathandizira Goli kuti azindikire zoti anthu awiriwa (Bonzo ndi Jubeki) ndi akaidi amene adathawa kundende usiku wapitawo komanso adaba kunyumba kwake.
∙ Insipekitala Goli adazindikira kuti anthu awiriwa ndi Bonzo ndi Jubeki pamene Bonzo adamunong’oneza namuuza kuti akadatha kumulemeretsa usiku womwewo ndi ndalama zomwe zidali pa chinyumba chachitalipo.
Kumbutso:
▪ Jubeki adagonana ndi bwenzi lake (mkazi wapamalo wogulitsa mowa) mosadziteteza mwakuti anali kukayikira kuti akadatha kumupatsa matenda amakono. Chomwe Jubeki ankadandaula panthawiyi si matenda amakonowo ayi koma kuwululidwa ndi mkaziyo.
▪ Jubeki adauza Bonzo kuti akafukula ndalama zomwe adabisa akazisungitsa kwa mkazi wapamalo ogulitsa mowayo.
▪ Jubeki adamulonjeza mkaziyo kuti amupatsa ndalama zoti atsegulire malo akeake ogulitsira mowa.
MFUNDO ZIKULUZIKULU
- Kusasamala
∙ Jubeki adagonana ndi bwenzi lake (mkazi wapamalo ogulitsirapo mowa) mosadziteteza. b. Zinthu zazing’ono zimawululitsa zazikulu
✔ Chikhothi cholemba mawu oti “Police” chidawululitsa Jubeki ndi Bonzo kuti ndi omwe adakaba kunyumba kwa Insipekitala Goli.
- Chinyengo
∙ Bonzo ndi Jubeki adanyengerera Insipekitala Goli kuti ampatsa 50 miliyoni Kwacha ngati angawasiye osawamanga.
- Kukonda ntchito
∙ Insipekitala Goli adakana kuchita zachinyengo.
∙ Ngakhale mkazi wake wa Goli adamugwetsa mphwayi kuti zojambula zidindo za zala za omwe adaba kunyumba kwawo angozisiya iye adamutsimikizira mkaziyo kuti iye adabwerera ntchito kunyumbako ndipo ayesetsa kuti okubawa agwidwe.
Zipangizo
- Chining’a
∙ Akuthirani machaka: Akuwomberani ndi mfuni
- Msemphano
∙ Anne adauza Goli mamuna wake kuti akuba adaswa zenera iye ali mtulo akumulota mamuna wakeyo chonsecho kuba kudachitika iye atatanganidwa ndi kucheza ndi bwenzi lake Khoswe m’chipinda chomwecho.
NUNSU YACHISANU NDI CHIWIRI
Khoswe apanikizidwa ndi Goli kupolisi
Umboni woti kuthawa kwa akaidi kumamukhudza Khoswe
∙ Adamizira kuti adadwala mwadzidzidzi panthawi yomwe akaidiwo adathawa koma atafunsidwa ngati adawadziwitsa abwana ake monga mwa dongosolo la pantchito, iye adakana.
∙ Yunifolomu yake yakuntchito idapezeka kunyumba kwa mzimayi woyendayenda yemwe adapereka zovala kwa Bonzo ndi Jubeki atathawa kundende ndipo chiphaso chake chinali m’thumba lamalaya.
∙ Diresi yovala pogona ya mkazi wa Goli yomwe idabedwa kunyumba kwa Goli idapezeka pamodzi ndi yunifolomu yake ya Khoswe.
∙ Zovala zomwe zidabedwa kunyumba kwa Goli pamodzi ndi diresi yovala pogona ya mkazi wake Anne, idapezeka kunyumba ya Khoswe.
Milandu yomwe Khoswe komanso mkazi wake ankaganiziridwa
Khoswe:
∙ Kuthandiza akaidi kuthawa kundende
∙ Kuthyola nyumba komanso kuba
Mkazi wa Khoswe:
∙ Kuthandizira kuba (kubisa zovala zobedwa m’nyumba)
∙ Kulephera kukanena kupolisi zakatundu wobedwa yemwe adali m’nyumba mwake.
MFUNDO ZIKULUZIKULU
- a) Bodza
∙ Khoswe adanama kuti adadwala mwadzidzidzi pamene akaidi awiri ankathawa, chonsecho anali akucheza kuchibwenzi kunyumba ya Goli.
- b) Chipwirikiti
∙ Yunifolomu ya Khoswe idapezeka kunyumba kwa mtsikana wapamalo wogulitsa mowa komanso chiphaso chake chidali m’thumba lamalaya.
∙ Yunifolomu ya Khoswe idapezeka ndi akaidi othawa kundende.
∙ Diresi la Anne lovala pogona lomwe lidabedwa kunyumba kwa Goli lidapezeka kunyumba kwa mtsikana wapamalo ogulitsa mowa.
∙ Zovala za Goli zomwe zidabedwa kunyumba kwake, zidapezeka kunyumba kwa Khoswe.
Zipangizo
- a) Msemphano
∙ Goli adauza Khoswe kuti chitsimikizo choti iye (Khoswe) adali ndi akaidi ndi choti atavula yunifolomu yake n’kuwapatsa akaidiwo, iwo adamupatsa malaya ake (a Goli) omwe adaba kunyumba kwake kuti iye asayende maliseche. Zoona zake n’zakuti akaidi adaba yunifolomu ya Khoswe pamene iye adatanganidwa ndi kucheza ndi Anne m’chipinda chomwe mudabedwamo ndipo Anne ndi yemwe adampatsa Khoswe zovala za Goli kuti avale.
∙ Mkazi wa Khoswe adaganiziridwa mlandu wobisa katundu wobedwa komanso kulephera kukanena kupolisi zakatundu wobedwa yemwe adali m’nyumba mwake. Zoona zake n’zakuti zovala za Goli zomwe zidapezeka m’nyumba mwake sizidabedwe; mamuna
wake Khoswe adabwera atavala zovala za Golizo usiku tsono kunali kovuta kuti mkazi wa Khoswe akanene kupolisi.
- b) Chining’a
∙ Ndikuchotsa chimbenene: Ndikukhaulitsa zedi.
NUNSU YACHISANU NDI CHITATU
Kubwalo lamilandu: chilungamo chidziwika
∙ Mkazi wa Goli, Anne, adauza woweruza kuti adali ali mtulo pomwe akuba adaswa zenera ndipo adazindikira kutacha kuti magalasi anali ataphwanyidwa komanso zovala za mamuna wake zidabedwa pamodzi ndi diresi lake lovala pogona.
∙ Bonzo adavomereza mlandu wothawa kundende osati wolanda Khoswe yunifolomu. Iye adafotokoza kuti atathawa kundende adaphwanya zenera pa nyumba ina momwe adabamo zovala ndipo adazindikira kuti panali yunifolomu ya msirikali wandende ndi diresi lovala pogona. Pamene ankaba zinthuzi n’kuti bambo ndi mayi a m’nyumbamo akucheza mwachikondi pa kama. Yunifolomu yomwe adatengayo adakasungitsa kwa bwenzi lake ku bala.
∙ Jubeki nayenso adavomera mlandu wothawa kundende osati wolanda Khoswe yunifolomu. Iye adafotokoza kuti ntchito yake inali yoonetsetsa ngati sikumabwera anthu panthawi yomwe Bonzo amaswa zenera. Nayenso adanena kuti eni nyumbayo anali akucheza pa kama m’mene iwo ankaba. Iye adati adamuzindikira mkazi wa Goli koma mamuna yemwe annkacheza naye sadamuzindikire.
∙ Khoswe adauza woweruza kuti akudziwa Bonzo ndi Jubeki osati mkazi wa Goli. Jubeki ndi Bonzo adathawa kundende ndipo adamulanda yunifolomu iye akudzithandiza atadwala m’mimba mwadzidzidzi. Iye adadzikola ponena kuti sadamuone Bonzo pamene amaswa zenera kunyumba ya Goli komanso adakanika kumuyankha Bonzoyo pamene adamufunsa ngati adayamba wajambulitsapo ndi mkazi wa Goli. Khoswe adanenetsa kuti Mayi Goli sanali kuwadziwa.
∙ Jubeki adawulula kuti sadamutsomphole Khoswe yunifolomu. Iye ndi Bonzo adaba yunifolomu kunyumba ya Goli ndipo m’thumba la yunifolomuyo dapeza chithunzi. Adapereka chithunzicho kwa woweruza milandu. (Khoswe ndi Anne adakumbaturana mwachikondi pachithunzipo.)
∙ Kumbutso: Goli sankadziwa kuti kunyumba kwake kudalowa mamuna wina yemwe ankazemberana ndi mkazi wake Anne koma zoyankhula za Bonzo ndi Jubeki zidawulula za mamunayu.
Zipangizo
- a) Chining’a: Mumakadzithandiza
- b) M’malere/M’biso: Mlembi sadafotokoze zomwe Goli adachitira mkazi pamene adazindikira kuti anali ndi mamuna wina iye ali kuntchito.
Makhalidwe oipa mu seweroli ndi zotsatira zake
∙ Khoswe athawa kuchokera ku ntchito yoyang’anira akaidi napita ku chibwenzi chake, Anne, mkazi wa Inspector Goli, zotsatira zake Bonzo ndi Jubeki apezerapo mpata nathawa ku ndende kuja
∙ Khoswe ali kwa Anne, Bonzo ndi Jubeki amubera shati ndi buluku lake (uniforomu ya pulizoni), mapeto ake ayenda atamvala Malaya a Inspetor Goli.
∙ Bonzo ndi Jubeki athyola banki nabamo ndalama zokwana k200 miliyoni ndipo azibisa ku ku manda, masitepe 77 kapena malipande makumi asanu kuchokera pa mtumbira womaliza. Pothawa kuchokera ku ndende apeza anthu atamangapo kale nyumba, komanso apolisi awagwiranso.
∙ Bonzo ndi Jubeki athawa kuchokera ku ndende ndipo apita kumanda kuja kuti akafukule ndalama zawo. Koma mlonda wa ku nyumba yomwe inamangidwa pomwe anabisa ndalama zawo ayimbira foni apolisi omwe abwera nawakwizinganso kachikena
∙ Akuthawa ku ndende Bonzo ndi Jubeki, Bonzo anaponda msomali nafuula ndi ululu, mapeto ake amayenda motsimphina. Komanso, akuyenda ayandikira nyumba ina naganiza kuti abemo zovala, Jubeki nayenso aponda msomali koma azulidwa ndi mnzake.
∙ Pothawa, Jubeki anati mkaidi wina (nyapala) anali mu ndende chifukwa chogwirira ka mwana kakang’ono.
Padziko la pansi palibe chinsinsi (Chilichonse chimaululika)
∙ Khoswe anathawa ku ntchito napita kwa Anne. Bonzo ndi Jubeki atathawa, Goli apita kunyumba kwa mkazi wa Khoswe kukamufunafuna. Khoswe nayenso afika atavala malaya ena. Izi zidabwitsa mkazi wake pa za komwe anali.
∙ Bonzo ndi Jubeki aba ndalama ku banki nazibisa ku manda, malipande 50 kuchokera pa mtumbira womaliza. Palibe amene anauziwa za idzi. Koma pokazitenga agwidwa ndipo amuuza Goli za izi.
∙ Pothawa ku ndende, Bonzo ndi Jubeki asungitsa zovala zomwe adakaba kwa Goli kwa msungwana wina wogwira ntchito ku malo ogulitsira mowa. Koma mzimayiyo amugwira apolisi ali ndi uniforomu ya pulizoni
∙ Zovala za goli zipezeka kunyumba kwa khoswe. Ndipo uniforomu ya Khoswe ipezeka ku nyumba kwa msungwana woyendayendayu yemwe amagwira ntchito ku malo ogululitsira mowa
∙ Pa tsiku la mlandu, Bonzo ndi Jubeki akana kuti sanawatsomphole zovala Bambo Khoswe koma awuza khoti kuti anaziba ku nyumba ina komwe banja (khoswe ndi Anne) limacheza pa bedi.
∙ Jubeki awonetsa khoti chithunzi chomwe pali mayi Goli ndi bambo Khoswe. Jubeki awuza khotilo kuti chithunzicho chinapezeka mu thumba la thalauza la Khoswe