NUNSU YOYAMBA
Kunyumba kwa Ndileya
▪ Ndileya akufika kumene kunyumba kuchokera kodula nsungwi adapeza mkazi wake Nadzonzi kulibe ali kuchitsime kotunga madzi. M’kudziyanhulira kwake, Ndileya adaulula kuti pakhomo sipanali bwino:
✔ Nkhuku zinali balala.
✔ Mbuzi zinali kunja pachingwe.
✔ M’yumba munali mosasesa.
✔ Mabulangeti anali okuda kwambiri.
Makhalidwe a Nadzonzi
▪ Kumwa mowa
▪ Kuchita miseche
▪ Ulesi
▪ Kusasamala zinthu ndi ana
Umboni woti Nadzonzi anali mlesi komanso mtchisi
▪ Adakhala zaka zitatu osachapa mabulangeti.
▪ Mamuna wake adampatsa sopo koma samachapa zovala.
▪ Chilundu chomwe adavala panthawiyi chinali nakanaka.
▪ Adakhala kwa mwezi wathunthu osasesa m’nyumba.
▪ Sadaphikire ana mpaka adachoka pakhomo.
Umboni woti Ndileya ankamumenya Nadzonzi
∙ Pamene Nadzonzi adamuuza Ndileya kuti adachedwa kuchitsime popeza chidayamba kuphwa mwakuti ankachita kudikira kuti madzi adzadze, Ndileya sadakhutire ndipo adamuuza Nadzonzi kuti ichi ndi chifukwa chomwe adapeza.
∙ Nadzonzi adapepesa nati m’mene anamumenyera sabata yapitayo sanali kupeza bwino mwakuti sakadatha kuyenda mwachangu.
Kumbutso:
∙ Ndileya adauza Nadzonzi kuti utchisi wake wamukwana ndipo m’kuyankhula kwake adasonyeza kuti ankalakalaka atapeza mkazi wina.
Zomwe zidasonyeza kuti Ndileya ankafunadi mkazi wina
▪ Adamuyerekeza mkazi wake ndi duwa lofota ndi dzuwa ndipo adamuuza kuti ankafuna kaduwa katsopano kosiyana ndi Nadzonziyo.
▪ Adati mkazi watsopano akadatha kusamala m’nyumba ndi zinthu mwaukhondo. ▪ Adatsindika kuti adatopa ndi moyo wankhumba (wauve).
▪ Adanenanso kuti m’nyumba mwake mumafanana ndi m’khola poti munali mwanyansi: zinthu zinali mbwee.
Chipanda chamowa chidzetsa mkangano pakati pa Nadzonzi ndi mamuna wake Ndileya ∙ Ndileya adakayikira kuti Nadzonzi adamuyikiramo mankhwala m’chipandamo popeza chidagwa n’kusweka iye atangoyamba kumwa komanso mumaoneka tinthu takuda. ∙ Ndileya adafunsa Nadzonzi ngati sadamuyikire chiphe m’mowawo koma Nadzonzi adakanitsitsa.
∙ Nadzonzi adauza mamuna wakeyo kuti mowawo adapatsidwa ndi Nasiwelo. Ndileya adakwiya kwambiri ndi nkhaniyi popeza Nasiwelo ankatchuka ndi mchitidwe wopeperetsa amuna okwatira.
∙ Ndileya adamuopseza mkazi wake Nadzonzi ndi mpeni mpaka adaulula kuti adamuyikira mankhwala m’mowawo. Iye adati adachita zimenezi kuti Ndileya abwerere kwa iye kuchoka Nanzunga.
Kumbutso:
∙ Ndileya adayitanitsa Nachuma (mchemwali wake wamkulu wa Nadzonzi) kuti adzamve zomwe adachita mchemwali wake.
∙ Nachuma ataona kuti sayikwanitsa yekha nkhaniyo, adapempha Ndileya kuti apite akawafotokozere atsibweni ake a Nadzonzi a Chidazi.
∙ Nadzonzi adayankhula kuti Ndileya anali ndi chikondi chabodza: analonjeza zomukonda Nadzonzi pachisoni ndi pachimwemwe koma panthawiyi anali kuzemberana ndi Nanzunga mwakuti sanali kumulabadiranso iye monga mkazi wake.
Zipangizo
- Voko : Mtolo wansungwi uli panjapo wandiphadi.
- Zining’a
▪ Pali kangaude pam’mero panga: Ndili ndi chipemba kwambiri
▪ Inetu sindipindira iwe manja anga: Inetu sindigwirira iwe ntchito.
▪ Moyo wankhumbawu: Moyo wauvewu/ moyo wautchisiwu
∙ Moti mutha kundigeya?: Moti mutha kundisiya banja?
MFUNDO ZIKULUZIKULU
- Utchisi
▪ Nadzonzi adakhala zaka zitatu osachapa mabulangeti.
▪ Ndiliya adampatsa sopo Nadzonzi koma samachapa zovala.
▪ Chilundu chomwe adavala Nadzonzi panthawiyi chinali nakanaka.
▪ Nadzonzi adakhala kwa mwezi wathunthu osasesa m’nyumba.
- Zikhulupiriro
▪ Ndileya adakhulupirira kuti mkazi wapabanja akamacheza ndi mbeta ndiye kuti akukhalira miseche.
▪ Ndileya adakhulupirira kuti Nadzonzi anamuyikira mankhwala (mkala wamchira wabuluzi) m’mowa pamene chipanda chidagwa n’kusweka iye atangoyamba kumene kumwa mowa.
- Kunyoza
∙ Ndileya ankamutcha Nadzonzi mlesi, chidzete komanso mtchisi.
- Nkhanza
∙ Ndileya adamenya mkazi ndipo mkaziyo adavutikabe kwa masiku angapo kuti akwanitse kuyenda mwachangu.
NUNSU YACHIWIRI
Kunyumba kwa a Chidazi
∙ Ndileya adafikako mwaukali akumunyoza Nadzonzi kuti ndi chidzete komanso adadumpha malire. Iye adauza a Chidazi kuti mdzukulu wawo adamuthirira mkala wamchira wabuluzi m’mowa.
Zotumphuka m’nunsuyi
∙ A Chidazi ankadziwa kuti Ndileya amamumenya mkazi wake.
∙ Ndileya sanali kuwawopa a Chidazi.
Matanthauzo a mawu
∙ Chidzete : chitsiru
∙ Wadumpha malire : waonjeza
NUNSU YACHITATU
Kunyumba kwa Ndileya
A Chidazi adziwa chilungamo
▪ Adafunsa mdzukulu wawo Nadzonzi kuti afotokoze chomwe chidamuchititsa kuti athirire mamuna wake mkala wamchira wabuluzi m’mowa.
▪ Poyamba Nadzonzi adanama kuti ndi Nasiwelo yemwe adamunyenga zoti athirire Ndileya mankhwala m’mowa.
▪ Nadzonzi adauza atsibweni akewo kuti adamuthirira Ndileya mkala wamchira wabuluzi m’mowa popeza amafuna kuti abwerere kwa iye; achoke kwa Nanzunga komwe ankagona usiku uliwonse.
▪ Nadzonzi adafotokozera atsibweni akewo kuti mwezi udatha mwamuna wake asakugona m’nyumba mwake koma ankakagona kwa Nanzunga ndipo Nasiwelo adamulangiza kuti atha kukhwimitsa chikondi chake ndi Ndileya mamuna wake pomupatsa mankhwala achikondi.
Pamfundozi a Chidazi adayankha zotsatirazi:
▪ Nasiwelo adamunamiza Nadzonzi (adamunyenga kudya nyama yagalu) mwakuti adakwiyitsa mamuna wake (adaponya muvi mumtima mwa mwamuna wake.)
▪ Nadzonzi akadawadziwitsa ndipo akadapeza njira yabwino yothetsera vutoli.
∙ Pamene Ndileya adamva mawu a Nadzonzi (kuti iye adamupempha mankhwala Nasiwelo) adamuthamangitsa ndipo adamunyoza kuti ndi mdyerekezi komanso ndi wodetsedwa. Iye adati sadagwiritse ntchito mankhwala kuti Nadzonzi amulole.
Zotumphuka m’gawoli
∙ Akazi ndi ogona popeza amatsatira zilizonse zomwe amawanong’oneza anthu amene amati ndi anzawo; makamaka amene amasangalatsidwa ndi mjedo. (mawu a a Chidazi komanso Ndileya)
NUNSU YACHINAYI
Ku bwalo lamilandu
∙ Mfumu idathokoza anthu kamba kobwera kumilandu m’malo mopita kukakolola. Madandu a Ndileya pabwalo lamilandu
∙ Akuzunzika kwambiri ndi Nadzonzi.
∙ Nadzonzi sasesa m’nyumba (wakhala mwezi wathunthu osasesa m’nyumba) ∙ Nadzonzi sadalotche zipupa kuchokera tsiku lomwe adakwatirana.
∙ Nadzonzi sachapa zovala ngakhale amamugulira sopo.
∙ Nadzonzi saphikira ana.
∙ Nadzonzi amachoka pakhomo m’mawa nkumakabwera madzulo.
∙ Nadzonzi sasiya madzi panyumba/pakhomo.
∙ Nadzonzi adamuthirira mkala wamchira wabuluzi m’mowa.
Mawu a Nachuma, mboni ya Ndileya
▪ Adauza bwalo kuti padalibe aliyense pamene Nadzonzi ankapereka mowa kwa mamuna wake.
▪ Adavomereza kuti Nadzonzi adathirira mamuna wake mankhwala m’mowa. ▪ Iye adauza bwalo kuti ngakhale iye kudalibe, koma Nadzonzi mwini wake adavomereza kuti adayika mankhwala m’mowa womwe adapereka kwa mamuna wake Ndileya. ▪ Adatsimikizira bwalo kuti mkala womwe unathiridwa m’mowa sunali mwaye popeza unali ndi mphumphu zazikuluzikulu kuposa mwaye.
Madandu a Nadzonzi
▪ Mamuna wake Ndileya amamumenya sabata iliyonse pofuna kumuchititsa kuti amusiye. ▪ Ndileya amafuna kukwatira Nanzunga; adamugulira nyama yang’ombe kambirimbiri pamene iye ndi ana ake ankadyera mnkhwani.
▪ Akaphika nsima, Ndileya amangodya mwapatalipatali.
▪ Ndileya wakhala akugona kwa Nanzunga kwa sabata zambiri.
▪ Ndileya amamunyoza komanso amamukwiyira kawirikawiri.
Mawu a Chidazi mboni ya Nadzonzi
▪ Ndileya ndi wankhanza komanso wautambwali.
▪ Ndileya amamumenya mkazi wake mwakuti mkaziyo wakhala akudandaula. ▪ Nadzonzi sadamuuze zoti mamuna wake Ndileya akuyenda ndi Nanzunga. ▪ Nadzonzi akutayirira pankhani yogwira ntchito pakhomo monga kusesa m’nyumba popeza akukhumudwitsidwa ndi khalidwe la Ndileya.
Umboni woti Nadzonzi ankamenyedwa ndi mamuna wake Ndileya
∙ Mkono wake wamanja unali wosupuka.
∙ Anali ndi zipsera pachipumi chake.
∙ Anali ndi bala pamsana pake.
Mayankho a Ndileya kwa mfumu pankhani yomenya Nadzonzi komanso kuchita ubwenzi ndi Nanzunga
Adavomera nkhanizi ndipo adati:
▪ Nandzonzi ndi amene amamuchititsa kuti azimumenya.
▪ Nadzonzi ndi cholengedwa chopusa komanso chamtima wapachala (wosachedwa kukwiya).
Malangizo amfumu asanapereke chigamulo
Kwa Nadzonzi
▪ Aziuza atsibweni ake mamuna wake akamulakwira ndipo ngati sakuyanjana kwa atsibweni ake azikagwada kubwalo lamilandu.
▪ Sakuyenera kupereka yekha chigamulo monga adachitira pothirira mamuna wake mankhwala m’mowa.
▪ Asamagwiritse ntchito mankhwala pofuna kuti mamuna wake amukonde. ▪ Chikondi sagula, sakakamiza komanso sapanga ngati zidole.
▪ Chikondi ndi mphatso yachilengedwe yochokera kwa Chiuta.
Kwa Ndileya
▪ Azidziwitsa atsibweni ake a mkazi wake ngati mkaziyo walakwitsa kanthu. ▪ Adachita zachibwana pozemberana ndi Nanzunga.
▪ Akhale wokhulupirika kwa mkazi wake ndipo ndi wake mpaka muyaya.
Chigamulo chamfumu
▪ Sadapeze zifukwa zokwanira zothetsera banja la Ndileya ndi Ndzonzi. ▪ Ndileya ayanjane ndi mkazi wake Nadzonzi.
▪ Nandzonzi apereke dipo la mbuzi kubwao la mfumu kamba kophwanya malamulo amudzi pomuthirira mankhwala mamuna wake m’mowa.
▪ Ndileya salandira kanthu kuchokera kwa mkazi wake m’malo mwake abwerere kunyumba azikakhala naye.
▪ Ndileya azikumbukira kuti kumenya sikumasandutsa chinthu choyipa kukhala chabwino. Zipangizo
26
- Mkuluwiko
∙ Wamva m’mimba ndiye atsekula chitseko: Amene ali ndi vuto ndi yemwe amasaka thandizo.
- Zining’a
∙ Bwalo ndilo liphwanye mutu wanyani: Bwalo ndilo lipereke chigamulo kapena chilango. ∙ Chamtima wapachala: Chosachedwa kukwiya kapena kunyanyala
∙ Ziphaliwali: Ukali kapena kulalata
∙ Igwa apa: Lipira
MFUNDO ZIKULUZIKULU
- Nkhanza
∙ Ndileya ankamumenya mkazi wake Nadzonzi mwakuti adasupuka pamkono, adali ndi zipsera pachipumi komanso anali ndi bala kumsana. Kumenyedwaku kudachititsa Nadzonzi kuti akanike kuyenda mwachangu pochokera kuchitsime kotunga madzi.
2. Kupirira
∙ Ngakhale Nadzonzi ankachitidwa nkhanza ndi mamuna wake (kumumenya komanso kuzemberana ndi Nanzunga) iye sadathetse banja ndi mamuna wake Ndileya. Iye adauza bwalo kuti amamukondabe Ndileya.
- Chilungamo
∙ Amfumu adagamula kuti Ndileya ayanjane ndi Nadzonzi mkazi wake ndipo kuti iwo sadapeze zifukwa zokwanira kuthetsa banja la anthu awiriwa.
∙ Nadzonzi adavomera kuti adathira mankhwala m’mowa womwe adapereka kwa mwamuna wake Ndileya pofuna kuti Ndileya asiye kupita kwa Nanzunga. ∙ Ndileya adamuuza Nadzonzi kuti adatopa ndi utchisi komanso ulesi wake mwakuti anali kufuna kukwatira mkazi wina yemwe angathe kusunga m’nyumba ndi katundu mwaukhondo.
∙ Nachuma adauza bwalo kuti padalibe munthu wina aliyense pamene Nadzonzi ankapereka mowa kwa mamuna wake Ndileya. Zoti anathira mkala wamchira wa buluzi m’mowa womwe adapereka kwa mamuna wake adadziwa popeza adawona mkalawo komanso mwini wakeyo, Nadzonzi adavomera kuti adathiramo mankhwalawo.
∙ Amalume ake a Nadzonzi, a Chidazi adauza bwalo kuti Ndileya amamumenya mkazi wake ndipo adaonetsa zipsera zomwe zinali pachipumi pa Nadzonzi, bala lomwe linali pamkono wake komanso kumsana kwake.
- Banja si mankhwala
∙ Mankhwala omwe Nadzonzi adakatenga kwa Nasiwelo nathirira Ndileya m’mowa kuti Ndileyayo achoke kwa Nanzunga n’kubwerera kwa iye sadagwire ntchito m’malo; mwake Ndileya adakasuma kubwalo lamilandu kwa amfumu kupempha kuti amusiye Nadzonzi.
- Kulephera udindo
▪ A Chidazi ankadziwa ndipo anali ndi umboni woti Ndileya ankamuchitira nkhanza mdzukulu wawo Nadzonzi koma palibe chomwe adachitapo monga kukasuma kubwalo lamilandu. M’malo mwake adakapereka umboniwu pamene Ndileya adakadandaula kubwalo lamfumu kuti akufuna kumusiya banja Nadzonzi ndipo akufuna kukwatira mkazi wina.
▪ A Chidazi adakanika kuganiza mwakuya kuti aweruze nkhani ya mdzukulu wawo Nadzonzi ndi mamuna wake Ndileya. Iwo adangokhulupirira kuti Nadzonzi adalakwa koma sadafune kuunika bwinobwino chomwe chidachititsa Nadzonzi kuti amuyikire Ndileya mankhwala m’mowa. Adayankhula kuti akazi ndi ogona popeza amatsatira zilizonse zomwe amanong’onezedwa ndi anthu omwe amati ndi anzawo. Bambowa adakanika kumuuza Ndileya kuti nayenso anali olakwa m’malo mwake adauza Ndileya kuti iwo amusunga Nadzonzi mpaka tsiku lamilandu.
▪ Nadzonzi amakanika kuwaphikira ana asanachoke pakhomo. Monga mkazi wapabanja komanso mayi wa ana, Nadzonzi anayenera kuonetsetsa kuti ana adya asanapite kosewera komanso anayenera kudziwa komwe ana ake akupita. Ana a Nadzonzi adachoka osadya popita kukacheza ndipo amayi awo samadziwa komwe adalowera mpaka dzuwa lidalowa.
Mawu ena ofunika kuwawunikira
- Umanena chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga
∙ Ulesi ndi utchisi wa Nadzonzi udachititsa kuti Ndileya ayambe kuyenda ndi Nanzunga ndipo adakhulupirira kuti mkazi watsopanoyu angathe kusamala m’nyumba komanso zinthu mwaukhondo.
∙ Mayendedwe a Ndileya ndi omwe adachititsa Nadzonzi kuti asakesake mankhwala n’kumuthirira mamuna wakeyo m’mowa ngati njira imodzi yolimbitsira chikondi chawo.
2. Mfumu idagamula bwino mlanduwu
∙ Adafufuza bwinobwino mlandu womwe Ndileya adasumira mkazi wake Nadzonzi ndipo adapereka chigamulo choyenera.
∙ Sadathetse banja la Ndileya ndi Nadzonzi monga amafunira Ndileya. ∙ Adapereka malangizo abwino kwa anthu onse awiriwa (Ndileya ndi Nadzonzi) nawauza kuti ayanjane.
- Zivumbulutso: Zinthu zomwe zidachititsa kuti zinthu zina zobisika zibwere poyera.
- a. Kugwa ndi kusweka kwa chipanda chamowa
∙ Kupulumuka m’manja kwa chipangizochi, Ndileya atangoyamba kumwa mowa, komanso kusweka kwake kudachititsa kuti Ndileya akayikire zoti Nadzonzi adamuyikira mankhwala m’mowa.
∙ Kusweka kwa chipangizochi kudachititsa kuti mkala wamchira wabuluzi womwe Nadzonzi adathira m’mowa uwoneke ndipo Ndileya adakwiya kwambiri.
b. Mpeni
∙ Ndileya atamufunsa Nadzonzi kuti awulule yemwe adathira mankhwala m’mowa, iye adakanitsitsa kuti sakudziwa. Pamene Ndileya adatenga mpeni n’kumuuza mkazi wakeyu kuti amupha nawo akapanda kuwulula yemwe anathira mankhwala m’mowa, iye (Nadzonzi) adawulula kuti adathira ndi iyeyo
- Kupempha chisudzulo
∙ Pamene Ndileya adayala madandaulo ake kubwalo lamilandu n’kupempha kuti amusiye Nadzonzi makamaka chifukwa adamuthirira mankhwala m’mowa, Nadzonzi adaulula kuti adamuthirira mankhwala achikondi popeza ankayenda ndi mkazi wina, sankagona pakhomo komanso samamusamala pamodzi ndi ana ake omwe.
∙ Nadzonzi adaululanso kuti Ndileya amamumenya sabata iliyonse. Mboni ya Nadzonzi idaonetsa mkono wosupuka wa Nadzonzi, zipsera pachipumi pake komanso bala kumsana kwake.
∙ Kusumaku kudaululitsanso kuti Ndileya adamugulira Nanzunga nyama yang’ombe kambirimbiri pamene iye ndi ana ake ankadyera nkhwani.
- Mtsiriko womwe Ndileya adapatsidwa ndi malemu bambo ake
∙ Mtsiriko umenewu udathandizira kuti Ndileya adabwe ndipo azindikire kuti china chake chinayikidwa m’mowa womwe adapatsidwa kuti amwe.
Makhalidwe a Nadzonzi
- Waulesi
∙ Mu khitchini mumakhala mopanda madzi. Mu nyuma mumakhala mosasesa ∙ Mabulangete ndi akuda kwambiri ndipo osachapidwa kwa zaka zitatu
∙ Amalephera kuchotsa mbuzi pa zingwe
- Wosasamala banja: Akamachoka pa khomo sasiya chakudya kuti mwamuna wake akabwera azichipeza
- Wogonjera: Mwamuna wake amukalipira chifukwa chofika mochedwa ku chokera ku madzi. Iye apempha Ndileya kuti amukhululukire. Ati akukanika kuyenda msanga chifukwa chomenyedwa ndi mwamuna wake
- Wachikondi: Athira mankhwala a mchira wabuluzi mu mowa kuti mwina mwamuna wake azimukonda kwambiri. Asiye kupita kwa Nanzunga
- Wopusitsidwa: Apusitsidwa ndi nasiwero kuti atenge mchgira wa buluzi kuti athire mu mowa. Akatero mwamuna wake azimukonda kwambiri
- Wa chilungamo: Avomera pa bwalo la mfumu kuti anathiradi mchira wa buliuzi mu mowa ndi chiolinga choti Ndileya azimukonda kwambiri, asiye kumumneya komanso amusiye Nanzunga
Makhalidwe a Ndileya
- Wa ndeu
∙ Amenya mkazi wake chifukwa chothira mchira wa buluzi mu mowa
∙ Amenya ndikusupula mkono wakumanja wa Nadzonzi
∙ Apatsa mkazi wake zipsera pamphumi chifukwa chomumenya
- Wachimasomaso: Nthawi zambiri amachoka usiku kunyumba kwake napita kwa Nanzunga, chibwenzi chake. Ananena izi ndi Nadzinzi ku bwalo la milandu
- Wopanda ulemu
∙ Sakuwapatsa ulemu atsibweni ake pamene anapita kuti akawawuze zomwe mkazi wake anachita pothira mchira wa buluzi mu mowa
∙ Achita kunjenjemera ndi mantha komanso ukali pamaso pa atsibweni ake nawauza kuti mudzaone zochita za chidzete chanu
- Wosakhululuka mnsanga: Awuza Nadzonzi pamaso pa atsibweni ake azipita chifukwa chothira mchira wa buluzi mu mowa
- Wolimbikira: Agwira ntchito molimbika mu minda yachimanga kuti adyeste ana ake. Sopo amagulanso. Ananena izi pabwalo la mfumu. Koma mkazi wake amalephera kudzigwiritsira ntchito bwino