MAFUNSO OYANKHA MWACHIMANGIRIZO
- Kodi chisudzo cha Mchira wa buluzi ndi Zikani zikufanana bwanji? Fotokozani mfundo zinayi.
- Fotokozani zochitika zomwe zikutsimikizira kuti mlembi adagwiritsa ntchito msemphano m’zisudzo izi:
∙ Chamdothe, Khoswe wapadenga ndi Zikani
Chamdothe
- Tsimikizani polemba mfundo zinayi kuti atengambali ena anali ankhanza 2. Fotokozani mfundo zinayi zotsimikiza kuti ampangankhani ena anali a makhalidwe abwino
Mchira wa buluzi
- Tsimikizani polemba mfundo zinayi kuti atengambali ena adali odekha pochita zinthu
- Fotokozani mfundo zinayi zotsimikiza kuti ampangankhani ena anali a makhalidwe oipa
- Tsimikizani popereka mfundo zinayi zowonetsa kuti mkazi wopusa amapasula banja ndi manja ake.
- Fotokozani mfundo zinayi zosonyeza kufunika kwa zivumbulutso m’chisudzochi.
- Fotokozani mfundo zinayi zotsimikiza kuti Ndileya adali wachikondi pa mkazi wake Nadzonzi.
Khoswe wa padenga
- Tsimikizani polemba mfundo zinayi kuti amapangankhani ena anali osakhulupirika
- Tsimikizani pofotokoza mfundo zinayi kuti choipa chitsata mwina
- Tsimikizani mawu oti atambwali sametana polemba mfundo zinayi
- Fotokozani mfundo zikuluzikulu zinayi zopezeka mu chisuzochi
Zikani
- Fotokozani mfundo zinayi zosonyeza kuti aliyense amakolola zomwe wafesa
- Tsimikizani pofotokoza mfundo zinayi kuti choipa chitsata mwini.
- Fotokozani mavuto anayi omwe bambo Mgezenge adakumana nawo kamba ka makhalidwe awo oipa
- Ndi zochitika zinayi ziti zomwe zikusonyeza kuti Mgezenge anali wankhanza? Fotokozani.
Mudzi wa Mfumu Tandwe
- Tsimikizani polemba mfundo zinayi kuti mu nkhaniyi munali nkhanza
- Fotokozani makhalidwe anayi oipa ma mu chisudzochi
- Fotokozani mfundo zikuluzikulu zinayi zopezeka mu chisudzochi
- Ndi zinthu zinayi ziti zomwe zikusonyeza kuti zinthu sizimayenda bwino m’mudzi mwa Mfumu Tandwe ngakhale munali dongosolo? Fotokozani.