KUBWALO LA MFUMU TANDWE
∙ Chiphaliwali adaletsa phokoso ndipo adauza anthu kuti msonkhano udayenera kuyambika.
Cholinga chamsonkhano
∙ Kukambirana/kuunikira mfundo zofunika kwambiri m’mudzimo
Mawu amfumu potsekulira msonkhano
∙ Adayamikira anthu kuti zomwe adagwirizana pamsonkhano ngati womwewu chaka chapitacho zinali kuchitika ndipo anthu andayambapo kuona zipatso zake. ∙ M’chaka chatsopanochi, anali ndi mitu ingapo yoti akambirane.
∙ Idayitana nduna zake kuti zifotokoze mitu yomwe idalipo motere:
MAYI CHIBWE
Adayankhula zinthu zokhuza kuonongeka kwa chilengedwe zotsatirazi:
∙ Mvula yayambanso kugwa mwa njomba
∙ Mudzi wawo unali wochita bwino (wa mwanaalirenji)
∙ Anthu ochokera kumadera ena monga ku Chombo, ku Linga, kwa Kalimanjira, ku Chithiba ndi ku Benga ndi ena ochokera kumapiri ankadzachita nsuma. Anthuwa ankatsata zakudya monga chimanga, mpunga ndi chinangwa.
∙ Nthaka inali yachonde pano yaguga. Kumboyoku anthu amalima osagwiritsira ntchito fetereza koma panopa sakuteronso.
∙ Mu Nyanja ya Mthambithabi munali nsomba zokoma monga nthachi, nkhututu, mbununu, chitemera ndi nkhalala koma panopa kulibe
∙ Kudambo la Mthabithabi kunkamera therere la kazirira.
∙ Mu nkhalango munali zipatso zokoma ndinso zopatsa thanzi monga kapwati, masuku, nziru, kankhande, maye, nthudza, bwemba, mapoza ndi kasokolowe.
∙ Nthawi yadzinja m’nkhalangomu ankazula bowa wokoma kwambiri monga chifisi, manyame, katerera, mnofuwankhuku ndi nkhwayukwayu.
∙ M’mudzimo munali mitengo yamankhwala amakolo monga mvunguti, msolo, kamphoni, msambamfumu, mwavi ndi thundu. Mitengo ina ndi monga m’bawa, mlombwa, mng’wenya, mgwalangwa, msopa, mkongomwa ndi mkalati. Anthu maliza chifukwa chotcha makala ndi kusema ziboliboli
∙ M’nkhalango yam’mudzimo munalinso nyama monga akalulu, agwape ndi ntchenzi.
Zinthu zonse zidatha pazifukwa izi:
✔ Nkhuli (kukonda kudya zankhuli)
✔ Kuotcha makala
✔ Kucheka matabwa ndi kusema ziboliboli
∙ Zotsatira zamchitidwewu ndi izi:
✔ Kusintha kwa nyengo
✔ Mvula ikugwa mwanjomba
✔ Ngozi zachilengedwe zidachuluka m’mudzimo
∙ Mlangizi wamkulu, Gogo Tsinde, adakumbutsa anthu onse kuti mfundo pa zoyenera kuchita zikakambidwa m’malimana ndipo adzakumananso Loweruka pakatha sabata ziwiri ndipo kuti limana lililonse lidzafotokozera bwalo mfundo zake.
∙ Asanadzutse Bambo Lungu, amfumu adayitanitsa gulu lovina la amayi ndi atsikana kuti ayimbe komanso avine nyimbo imodzi yokamba za kuonongeka kwa chilengedwe komanso kusintha kwa nyengo.
BAMBO LUNGU
Nkhanza kwa amayi ndi ana aakazi: Ndunayi idayankhula motere:
∙ Nkhani zokhudza nkhanza zomwe ankangomva ngati nkhambakamwa chabe zidayamba kuchitika m’mudzimo.
∙ A Chiphiri amenya mkazi wawo koma ali woyembekezera chifukwa chobwera mochedwa kuchokera ku nkhuni. Mapeto ake mkazi wake apita pa dera. Panopa a Chiphiri akugwira ntchito ya kalavulagaga ku ndende. Bwanji iwo kuti azikatheba okha nkhuni!
∙ Amuna ambiri akagulitsa tsabola amalowerera ku Dwangwa. Amakaononga ndalama ndi akazi oyendayenda. Zikatha ndalamazo mpamene amabwerako. Ku Dwangwa amabwerako alibe kalikonse komanso atatenga matenda opatsirana pogonana.
∙ Akazi akuvutistidwa kuti azilima koma odyerera ndi ena. Akatenga mnatenda amavutitsa akazi awo powasamala komanso umasiye
∙ Anthu ambiri ofunikira m’mudzimu, anali atamwalira ndi matenda a edzi. ∙ Bambo Pedegu adamangidwa kamba ka kugwirira mwana wawo wompeza wazaka khumi. ∙ Pasukulu yomwe adayandikana nayo padali aphunzitsi ena aamuna omwe ankafunsira tiana tatikazi.
∙ Adapempha malimana kuti akaunikire mozama zedi nkhani ya amayi ndi atsikana ∙ Adatsindika kuti mchitidwe wankhanza utha chaka chimenecho.
∙ Pasanalowe mayi Amuli ndi nkhani zina ziwiri, amfumu adayitanitsa gulu lovina la abambo komanso la anyamata la Kanada kuti avine nyimbo imodzi yomwe imakamba za kuipa kwa nkhanza kwa amayi ndi ana.
MAYI AMULI
Ndunayi idayankhula nkhani zitatu zokhuza achinyamata motere:
- a) Makhalidwe a anyamata ndi atsikana
∙ Kale anthu ankati achinyamata ndi atsogoleri amawa.
∙ Makono amati achinyamata ndi atsogoleri alero komanso amawa popeza:
✔ Makono ali m’maudindo ndipo akutsogolera pa zochitika zosiyanasiyana.
✔ Adakali anthete ndipo ali ndi zaka zingapo kutsogolo; dziko lidzakhalabe m’manja mwawo. Makolo monga iwowo adatsala pang’ono kumwalira.
✔ Akadzamwalira, achinyamata adzasunge mawu awo.
∙ Anyamata ambiri m’mudzimo adalowerera komanso adasochera:
✔ Amangokhalira kumwa mowa ndi mankhwala ozunguza bongo. Ambiri mitu yawo sinkayenda bwino.
✔ Ena akumakhwewa chamba. Mapeto ake akumapenga nanamizira nkhalamba kuti zawaloza.
✔ Atsikana sankavala bwino m’mudzimu: Ankavala kazimoto/ndekesha (zovala zazifupi kwambiri) pamaliro nkumakanika kukhala pansi.
✔ Atsikana amayenda bere lili pamtunda ngati logulitsa.
∙ Achinyamata analibe chidwi ndi makhalidwe abwino amakolo
∙ Miyambo yakale yoipa idathetsedwa.
- b) Achinyamata ndi ndale
∙ Achinyamata amatengeka ndi zandale, makamaka nthawi yamisonkhano yokopa anthu. ∙ Akasuta chamba komanso akamwa kachasu, amayambitsa chipolowe. ∙ Zipolowe zomwe adachita tsiku lina zidaphetsa anzawo ophunzira bwino ndipo makolo awo anali kusowa mtengo wogwira kamba ka imfa yawo.
∙ Ana a atsogoleri azipani sachita nawo zipolowe ndipo amakhla otanganidwa ndi maphunziro kuti nawonso adzawalamulire.
- c) Kusalana
∙ Anthu ena anali kusalidwa pazochitika za m’mudzimo kamba ka kuti ndi amtundu wina kapena chimbedzo china.
∙ Anthu ankasalidwa pantchito monga kulima msewu, zomwe amalandirapo ndalama komanso pa zinthu zaulere monga kulandira chakudya chomwe mabungwe apereka kwa anthu ovutika.
∙ Mayiwa adafotokoza ndi chitsanzo kuti mwana akabadwa kuchipatala onena uthenga samati kwabadwa Mkhirisitu, Msilamu, Mkunja Kapena Mchewa, Myawo ndi Mlomwe kapena Mtumbuka. Chimodzi wopereka uthenga wamaliro sasiyanitsa.
∙ Sukulu yamm’udzimo inali yampingo koma ophunzira ake anali amipingo yosiyanasiyana osati mpingo wa eni sukuluwo. Aphunzitsinso anali amipingo yosiyanasiyana. Chimodzimodzi, chipatala cham’mudzimo chinali champingo koma ogwira ntchito ndi olandira thandizo anali amipingo yosiyanasiyana.
∙ Anthu amipingo ndi mitundu yosiyana amadalirana; n’chifukwa chake akuyenera kukhalira limodzi komanso kugwira ntchito limodzi.
∙ Anthu amene amalimbikitsa za sankho ndi opanda nzeru komanso osaganiza mozama.
MAWU A MFUMU
∙ Amfumu adauza gulu lonse kuti mfundo zomwe zinalipo zinali zokhazo ndipo adapempha Gogo Tsinde kuti awakumbutse anthu mfundo zomwe zidakambidwa pamsonkhanowo. Gogo Tsinde adawuza Mayi Mwenda omwe adafotokoza mwachidule mfundo zamsonkhano. Pambuyo pa zonse panali chidyerano.
∙ Aliyense amadya chakudya chomwe adatenga pamodzi ndi anthu ena osati abale ndi anansi ake. Gogo Tsinde adakumbutsa anthu kuti akatsiriza kudya apite m’malumana mwawo kuti agwirizane tsiku loti akumane ndipo akambirane zomwe adamva pamsonkhanowo.
∙ Pavuto lililonse apeze magwero osachepera atatu komanso akambirane momwe angalithetsere vutolo. Nduna zamfumu zidzayendera malimana kuti zione m’mene zinthu zikuyendera. Mfumu Tandwe idatseka zonse pokumbutsa anthu kuti adzakumananso Loweruka pakapita sabata ziwiri ndipo lumana lomwe silidzapezeka lidzapereka mbuzi imodzi.
ZIPANGIZO
- Zining’a
∙ Kuchita kaliunji: Kukumana
∙ Tigundane mitu: Kukambirana mokuya
∙ Waziwala m’maso: Wamisala
∙ Amvula zakale: Akale
∙ Anagonera dzanja: adamwalira
∙ Anadula phazi: Anasiya kubwera pamalo
∙ Zooneka ndi maso: Zodziwika bwino
∙ Ikugwa mwanjomba: Ikugwa yochepa komanso mwa apo ndi apo ∙ Taima mitu: Tadabwa kwambiri
∙ Anapita padera: Adabereka mwana wakufa.
∙ Kukhalira m’mphanthi: Kukhala movutika komanso mwamantha kwambiri ∙ Mwabwerako manja ali m’khosi: Mwabwerako opanda chilichonse ∙ Adatsikira kumsitu: Adamwalira
∙ Dzuwa latsala pang’ono kutilowera: Tatsala pang’ono kumwalira. ∙ Kumbiya zodooka: Kumanda
∙ Kukhwewa: Kusuta
∙ Zikutidulitsa mutu wazizwa: Zikutidabwitsa
∙ Kuzitengera pamgong’o: Kuchita zinthu mosazimvetsa bwino komanso mopitiriza muyeso
∙ Zoyika moyo pachiswe: Zoti zikhoza kuononga moyo
∙ Ukadziwotche: Kulimba mtima kololera ngakhale kufa
∙ Mutayabwidwa ndi chitedze: Mutatenga matenda opatsirana pogonana.
2. Mikuluwiko
∙ Chala chimodzi sichiswa nsabwe./Mutu umodzi susenza denga: Munthu sangachite zinthu yekha; amathandizana ndi ena.
∙ Mawu a akulu akoma akagonera: Mawu a akulu amadzapherezera pakapita nthawi.
3. Mvekero
∙ Mbalambanda: kuonekera
∙ Mbwandawumbwandawu: kuyenda motopa
MAPHUNZIRO
- Nkhanza
∙ A Chiphiri adalekerera mkazi wawo woyembekezera ndipo ali wolema kuti akatole nkhuni kudondo.
∙ A Chiphiri adamenya mkazi wawoyu pamene adabwera mochedwa kuchokera kunkhuniku.
∙ Bambo Pedegu adagwirira mwana womupeza wazaka khumi.
∙ Azibambo akagulitsa tsabola, amapita ku Dwangwa kukasakaza ndalama ndi akazi oyendayenda chonsecho ankalima ndi akazi awo
∙ Mamuna wina adafuna kugwirira mayi ake omubereka.
- Mudzi wa mfumu Tandwe unali wadongosolo
∙ Mfumu Tandwe simagwira ntchito yokha. Idagawira nduna zake zochita ndipo nduna iliyonse imagwira ntchito yake molumikizana ndi akuluakulu a m’malimana. Pamsonkhano, aliyense amatsatira ndondomeko yamalonje poyankhula.
- Chikondi
∙ Mayi Pedegu adapita kukawazonda amuna awo kundende ngakhale adamangidwa kamba kogwirira mwana wawo womupeza.
∙ Atsogoleri m’mudzi mwa Mfumu Tandwe adathetsa miyambo yakale yamokolo yoyipa monga kulowa kufa, chokolo komanso kupondereza azimayi.
- Kusunga chinsinsi
∙ Azimayi ena amabisa amuna awo akagwirira ana aakazi.
- Mchitidwe wosasiyanitsa amuna ndi akazi (gender)
∙ Mfumu Tandwe idali ndi nduna zazimuna komanso zazikazi ndipo mlangizi wamkulu ndi ena oyendetsa zinthu panthawi yamsonkhano adali akazi.
- Kuganiza molakwika
∙ Makolo a anyamata omwe adapenga ndi chamba ankati anyamatawo adalodzedwa ndi nkhalamba.
- Kusasalana
∙ Anthu a m’mudzi mwa Tandwe, omwe anali osiyana zipembedzo ndi mitundu yomwe ankapita ku sukulu ndi chipatala cha mpingo ngakhale kuti zinthu ziwirizi zinali za mpingo wosiyana ndi anthuwo.
- Kulowerera
∙ Achinyamata a m’mudzi mwa mfumu Tandwe anali osokonekera m’njira zosiyanasiyana.
9. Kusasamala
∙ Anthu a m’mudzi mwa Tandwe adadula mitengo pocheka matabwa, kuotcha makala komanso kusema ziboliboli. Mitengo yambiri idatha. Izi zinadzetsa mavuto a zachilengedwe mu mudzimo
∙ Anthu ankawedza nsomba mwadyera choncho zambiri zidatha
- Kuganiza mwakuya
∙ Amfumu amayitanitsa gulu la ovina monga amayi ndi atsikana komanso abambo ndi anyamata a Kanada pambuyo pa zoyankhula za nduna. Izi zimathandizira kuti anthu asatope komanso asanyinyirike kutalika kwa msonkhano. Izinso zimapereka mpata kwa woyankhula kuti akonzekere.