Course Content
Kufunika kwa Zisudzo
Chisudzo ndi nkhani yochitika kapena yopeka yomwe imafotokoza zinthu mokhala ngati zikuchitika kumene.
0/2
MITU YONSE MNKHANIYI
0/1
Khoswe Wa Padenga
Kukamba za Bonzo, Goli, Khoswe, Anne ndi Jubeki
0/2
Mudzi Wa Mfumu Tandwe
Kuonongeka kwa zachilengedwe ndi mavuto ena
0/3
CHAMDOTHE NDI ZISUDZO ZINA

NUNSU YOYAMBA  

Ku bwalo la masewero: Kaziputa anyoza Chamdothe  

Kaziputa adakumana ndi Chamdothe pabwalo lazamasewero ndipo adamunyoza kuti ndi  opusa ndi anzake onse popeza  

ankachita masewero omvetsa chisoni.  

amayimba nyimbo zomvetsa chisoni pamene anthu ena onse anali kusangala.  amadziyerekeza ndi birimankhwe wobwretsa imfa.  

anthu ochenjera sachita masewero okamba za imfa.  

Kaziputa adapeperetsa Chamdothe pomuuza kuti atafune khala n’kunena kuti ngochenjera  ndipo akatero adzasiya kumunena kuti chidzete. Chamdothe adatsomphola khalalo  n’kulitafuna koma adatsamwa nalo. Kaziputa adaonjezera mnyozo wake pomunyodola  Chamdothe kuti anthu ochenjera sadya makala. Chamdothi adakwiya mwakuti pamene  Kaziputa amachoka pabwalo adamutsatira ngakhale Dama ankamuletsa.  

Kumbutso: Chamdothe adauza Kaziputa kuti gulu lawo limaonetsa chisangalalo poyimba  nyimbo zachisoni choncho kuyimba nyimbo zachisoni sikudali kupusa.  

Kunja kudayamba mabingu ndi ziphaliwali ndipo Dama adauza anzake kuti mvula  idayenera kugwa panthawiyi. Chamdothe, pozindikira mavuto ake monga mwana wadongo,  adayamba kuthawira kwawo. Panthawiyi, mayi ake a Chamdothi ankamuyitana ndi nyimbo  ya “Chamdothe thawa mvula.” Zione adamunyengerera Chamdothe kuti asapite kwawo  popeza anali kusewerabe.  

Chamdothe atafika kunyumba adafuna kudziwa kuchokera kwa amayi ake kuopsa kwa  kuvumbidwa ndi mvula. Ndatopa, mayi ake, adamufotokozera kuti iye anali wosiyana ndi  anthu enawo popeza adachita kuombedwa ndi dongo choncho sakuyenera kukhudzidwa ndi  dontho lamvula: angadzabwerere ku dongo komwe iye adachokera. Iye adali ndithu mdani  wamvula yomwe idali imfa yake.  

MFUNDO ZIKULUZIKULU  

  1. Chikondi/Chilungamo/Kuteteza  

Ndatopa adamuuza mwana wake Chamdothi kuti adapangidwa kuchokera ku dongo  choncho adayenera kumathawa mvula yomwe ikadatha kumupha. 

Mayiyu adafotokozera mwana wake momveka bwino za umoyo wake ndipo tsiku lina  ataona kuti kunja kwayamba mabingu ndi ziphaliwali adayamba kumuyimbira kanyimbo  komuyitanira kunyumba kuti tsoka lisampeze popeza mwana adali yekhayo. 

2. Chidwi  

Chamdothe adafuna kudziwa chomwe mayi ake ankaopa pomuyitana ndi nyimbo kuti  athawe mvula.  

  1. Kunyoza  

Kaziputa adanyoza Chamdothe ndi anzake kuti anali opusa poeza amayimba nyimbo  zomvetsa chisoni pamene ena onse ankasangalala.  

  1. Ulemu  

Chamdothe adavomera kuyitana kwa amayi ake ndipo adapita mwachangu ngakhale  Zione ankamunyengerera kuti anali kusewerabe.  

  1. Nkhanza 

Kaziputa auza Chamdothe kuti adye khala kuti awonetse kuti ndi wochenjera. Chamdothe  adya ndipo atsamwa. Kaziputa amuseka 

Kaziputa akankhira Chamdothe pansi nagwa pomwe iye amayerekeza kuyenda  kayendedwe ka birimankhwe. Pamene akuyesera kuti adzuke, gulu la Kaziputa  limukanikizira pansi ndipo Kaziputa amuopseza Chamdothe. 

NUNSU YACHIWIRI 

Kunyumba kwa Ndatopa: Kubadwa kwa Chamdothe  

Ndatopa adaloleza Chamdothe kuti apite akasewere ndi anzake. Ndipo pambuyo pake  Mayi Lunda adabwera kudzacheza ndi mayi a Chamdothe. Mayiwa adampeza mnzawoyo  ali m’malingaliro ndipo atamufunsa adati ankakumbukira ubwana wawo.  

Azimayi awiriwa adavinira limodzi gule wa bongololo ndipo Mayi Lunda adanyamuka  n’kumapita. Ndatopa adakumbukira mkangano womwe udachitika ndi mamuna wake  Angozo pankhani yakusowa mwana ndipo udachititsa kuti mamunayo asamuke  pakhomo. Ndatopa adakumbukira zinthu zotsatirazi:  

Angozo adamutcha Ndatopa buthu popeza adalibe mwana.  

Abale a Angozo ankamufunsa mafunso ambirimbiri ndipo asuweni ake aakazi  ankamunena kuti adangodzivutitsa kupeza mkazi.  

Angozo ankati anzake ankamunena kuti Kalulu adamudutsa m’mphechepeche.  Ndatopa adauza Angozo mamuna wake kuti ankamwabe mankhwala omwe awiriwa  adakatenga kwa ng’anga ina.  

Angozo ankafuna kutenga mkazi wina kuti amuberekere ana.  

Angozo adamulowola Ndatopa kwa Asena.  

Mkangano umenewu udachititsa Ndatopa kuganiza zongoomba chidole ndi dongo ndipo  adakatapadi dongolo nadzitsekera mnyumba mwakuti pamene Mayi Lunda adabwera  kudzacheza, sadatsekule chitseko. Adamunamiza mnzawoyo kuti anali kumva mutu koma pomumvetsa Ndatopa, Mayi Lunda adamuuza kuti amuna amalemekeza mkazi  akawaberekera ana ndipo kuti ngati mkazi satero amakhala wopanda pake.  Ngakhale mayiyu adayesetsa kunyengerera Ndatopa kuti amutsekulire aone mbiya yomwe  amaomba, iye sadatsekule. Ndatopa adauza Mayi Lunda kuti awayitana akatsiriza kuomba  mbiyayo popeza anali atangoyamba kumene ntchitoyo. 

Panthawiyi Ndatopa akusisima adaomba chidole ndipo adapempha Chiuta kuti ampatse  mwana. Adatsinzina nakweza manja kumwamba kwa Mulungu ndipo chidolecho chidakhala  ndi moyo. Mayi Lunda ankadikirabe panja panyumbayo koma Ndatopa adawauza kuti anali  asadatsirizebe kuomba ngakhale mphika umodzi.  

Chamdothe, mwana yemwe anali atangoombedwa chakumene ndipo adapatsidwa moyo,  adayamba kuyankhula pofunsa za mayi yemwe anali kunja kwa nyumbayo koma mayi ake  adamphimba pakamwa kuti Mayi Lunda asamumve. Pambuyo pake Ndatopa adauza Mayi  Lunda kuti awapititsira kwawo miphika yomwe anali atangotsiriza kumene kuomba ndipo  ayinyamula mosamala.  

Kumbutso: Mayi Lunda ndi omwe adaphunzitsa Ndatopa kulotcha mimphika.  

Chamdothe pabwalo tsiku loyamba  

Kaziputa adafuna kuti amudziwe Chamdothe ndipo adazizwa atamva kuti ndi mwana wa  Ndatopa popeza adauzidwa kuti Ndatopa sakadakhala ndi mwana ndiponso analibe  mwamuna.  

Puna adaonjeza kuti Ndatopa akadakhala ndi mwana sakadakula anthu osadziwa. 

Chamdothe adauza Kaziputa kuti amake adamtenga kubanja lina m’mudzi wa  Kuserikumvenji.  

Puna ndi Kaziputa sadakhulupirire ndipo adayamba kumukankha Chamdothe kuti anene  zoona koma Lunda ndi Zione adaleretsa. Lunda adaopseza Kaziputa ndipo Chamdothe  adapeza mwayi wothawira kwa amayi ake.  

Chamdothe ndi amayi ake 

Chamdothe adafotokozera mayi ake zomwe ankanena Kaziputa ndi Puna kuti iwo alibe  mwana komanso mudzi wa Kuserikumvenji kulibe.  

Ndatopa adachenjeza Chamdothe kuti asamawayandikire anthu awiriwa angadzamuphetse.  Adamuuzanso kuti asamale ndi Kaziputa popeza anali ndi mavuvu ndipo Ndatopa sakadatha  kumuteteza kumavuvuwo.  

Ngakhale Chamdothi adanena kuti ankafuna kukhala ngati mnyamata wina aliyense  pophunzira mavuvu n’kuwagonjetsa popeza mamuna aliyense amatero kuti akule, Ndatopa  adamuuza kuti sanayenera kuchita masewero onyansawo kuti akule.  

Chamdothe adauza amakewo kuti Zione, Dama ndi Lunda adamulandira kale ngati mnzawo  kubwalo. Ndatopa adamuchenjeza kuti anzakewo asamupititse koopsa.  

Chamdothe agwa m’chikondi ndi Zione 

Adakangana ndi Kaziputa popeza ankati Zione ndi wake (mkazi wa Kaziputa) ndipo  adamutsimikizira kuti tsopano ndi mkazi wake (wa Chamdotheyo).  

Adalandira chibangiri kuchokera kwa Zione.  

Matanthauzo amawu  

  1. a) Mavuvu : Khalidwe lochita zinthu mosaugwira mtima, modzionetsera komanso moonjeza. b) Gwetseranani mumchenga: Siyani kukangana ndipo yanjanani. 
  2. c) Chibangiri: Khoza lachitsulo lovala kumanja 
  3. d) Chamdothi: Mwana wochita kuumbidwa kuchokera ku dongo 
  4. e) Kaziputa: Mnyamata wokonda kuputa dala ndikunyoza Chamdothe. 
  5. f) Ndatopa: Mayi wolema chifukwa chosakhala ndi mwana nkumavutana ndi mamuna wake,  g) Zione: Ona zinthu monga zabwino ndi zoyipa zomwe  

MFUNDO ZIKULUZIKULU 

  1. Nkhanza 

Kaziputa ndi Puna adayamba kumukankhizirana Chamdothe pamene ankamutsutsa zoti  sadatengedwe ku banja lina ndipo mudzi wotchedwa Kuserikumvenji kudalibe.

2. Kuteteza 

Zione ndi Dama komanso Lunda adamuleretsa Chamdothe pomuuza Kaziputa kuti iye  amangodana ndi Chamdothe ndipo adaonjezanso kuti asayerekeze kumuvutitsa  Chamdothe. 

Adamuopsezanso kuti mavuvu akewo asachitire munthu wam’mudzimo popeza akatero  adzathesemulidwa. 

  1. Chikondi 

Chamdothe ndi Zione adagwa mchikondi moti Zione adapereka chibangiri kwa  Chamdothe. 

Chamdothe adauza Kaziputa, ngakhale anali wamavuvu, kuti Zione ndi mkazi wake.  4. Kukanika kulongosola 

Kaziputa adakanika kumufotokozera Chamdothe pamene adafuna kudziwa ngati iyeyo  (Kaziputa) anali kuonetsera chikondi chake pa Zione pamene adanena kuti ndi mkazi  wake.  

  1. Bodza.  

Chamdothe anamiza Kaziputa kuti iye anachokera ku mudzi wa Kuserikumvenji.  Ndatopa anamiza anzawo, Mayi Lunda kuti akuumba mbiya pomwe akuumba  Chamdothe 

NUNSU YACHITATU 

Chamdothe kumtsinje  

Chamdothe adaomba mbuzi yadongo n’kumasewera nayo. Kaziputa adamulanda  mbuziyo ndipo adapita nayo pamwala womwe unali pakati pa dziwe. Kaziputa adauza 

Chamdothe kuti ankafuna kuona ngati Chamdothe angapulumutse mbuziyo.  Adayigumula nayiponyera m’madzi.  

Zione ndi anzake ena adamuthamangira Chamdothe yemwe panthawiyi ankayenda  m’mbali mwa mtsinje posafuna kuti alumphire m’madzi. Zione adauza Chamdothe kuti  Kaziputa adachitira dala kugumula komanso kuponya m’madzi mbuzi yake pofuna  kulipsira zomwe Chamdothe adachitira Puna usiku wina.  

Zione adakumbutsa Chamdothe kuti Kaziputa amachitira anzake zoipa ngakhale  asadamuyambe. Kaziputa adakana Puna ku Mnjiri. Pochoka kumtsinjeku, Zione  adampatsa Chamdothe nkhanu kuti akapereke kwa amayi ake popeza adakhala nthawi  asadazilawe.  

Pochoka pamalopa Chamdothe adaganizira zinthu ziwiri zotsatirazi:  

Chomwe chinkamuchititsa Kaziputa kuti azimusungira nkhwidzi nthawi zonse

  Adalakalaka Zione atadzakhala mkazi wake  

Chamdothe Kumunda 

Chamdothe adauza amake kuti adaganiza zopita nawo kumunda popeza sankafunanso  kusewera panthawiyi. Ndatopa adafuna kudziwa kuchokera Chamdothe chomwe Zione  adalinga popereka nkhanu kwa Chamdothe.  

Mwanayu adayankha amakewo kuti Zione adati nkhanuzo ndi zawo (za amakewo) osati za  iyeyo. Mafunso omwe Chamdothe adaponyera Ndatopa adasonyeza kuti iye (Chamdothe)  adagwa m’chikondi ndi Zione ngakhale kuti sadam’tchule dzina.  

Adakacheza choncho, Ndatopa adagwira nkhumbu yomwe panthawiyi inkapereka zinthu  ziwiri: chakudya chokoma komanso macherechete.  

Pamundapa, Chamdothi ndi mayi ake, Ndatopa adacheza motere:  

Ndatopa adakana kumuuza Chamdothi nyimbo ya macherechete komanso ya nkhumbu. 

Ndatopa adauza Chamdothe kuti akadatha kugonetsa nkhumbu m’kakhola ndi kuyimba  nyimbo yekha.  

Chamdothe adayankha kuti kutero ndi kuchitira nkhanza tizilombo monga nkhumbuzo. 

 Ndatopa adatsimikizira Chamdothe kuti nkhumbu zidalengedwa kuti zizidyedwa.  Ndatopa adadziwitsa mwana wakeyo kuti anthunso adzafa ndipo uthenga wa imfa  

udabwera ndi namzikambe kuchokera kwa Chiuta kupita kwa Mchewa kapena Mmaravi  wamamuna ndi wamkazi pa Kapirimtiwa koma Chamdothe adayankha kuti  nkhumbu/chilule siziyenera kuphedwa kamba ka uthenga wa imfa womwe udabwera ndi  namzikambe popeza ndi tizilombo tating’ono ndipo imfa yake njopanda pake.  

Ndatopa adauza Chamdothe kuti imfa zisankha ndipo sifotokoza chifukwa chake.  Asanatsirize macheza pamundapa kudamveka mkokomo wamvula kotero Ndatopa  adamutenga Chamdothe nkuthawira naye kunyumba kuti asanyowe. Adasiya makasu ndi  dengu.  

 

MFUNDO ZIKULUZIKULU  

  1. Chikondi 

Ndatopa adacheza ndi mwana wake ndipo adamufotokozera chiyambi cha imfa komanso  adamuuzako za nkhumbu nampangira macherechete.  

Zione adapereka nkhanu kwa Chamdothe kuti akawapatse mayi ake popeza adakhala nthawi  yayitali asadazilawe.  

Zione adamuthamangira Chamdothe, pamene adamuona akuyenda m’mbali mwa mtsinje,  kuti asagwere m’madzi.  

  1. Kuteteza  

Zione adamuthamangira Chamdothe, pamene adamuona akuyenda m’mbali mwa mtsinje,  kuti asagwere m’madzi.  

Ndatopa adalolera kusiya makasu ndi dengu pamunda pofuna kupulumutsa Chamdothe ku  mvula yomwe ikadamupha.  

  1. Nkhanza 

Kaziputa abonthola mbuzi yomwe Chamdothe anaiumba. Apa anali ku mtsinje pomwe  amasewera. 

  1. Luso 

Luso loimba: Ndatopa ayimba nyimbo mpaka nkhumbu yomwe ikuluka kutera. Ndatopa  aimbira nyima chelule mpaka kumugonetsa. Kenako amugwira 

Luso loumba: Chamdothe aumba mbuzi ku mtsinje. Ndatopa aumba Chamdothe. 

Matanthauzo a mawu  

Nkhumbu: Kachirombo kooneka moyerera komwe kamakhala ndi mapiko olimba ndipo  anthu amapangira mangwere.  

Macherechete: Choyimbira chopangidwa ndi chingwe chachitali chomwe anthu  amatungirako mapiko a nkhumbu akunja navala m’khosi mokupatira, kenaka namayimba  ndi zala.  

NUNSU YACHISANU  

Imfa ya Chamdothe  

Zione adapita kwa mayi a Chamdothe ndipo adawapempha kuti amutenge akasewere naye.  Mayi a Chamdothe adamukaniza pomuuza kuti samafuna zoti mwana wawo Chamdothe  akasewere kutali popeza nyengo yamvula inali itafika. Zione adalonjeza kuti akamudyetsa  komanso akamusamalira bwino Chamdothe. Ndatopa adamuloleza Zione kuti amutenge  Chamdothe.  

Zione ndi Chamdothe atafika pabwalo posewerera, Kaziputa adasiya Puna nanyamuka kuti  akamukankhe Chamdothe koma Dama ndi Lunda adaleretsa. Mkangano wolimbirana Zione  udabukanso pakati pa Chamdothe ndi Kaziputa motere:  

Chamdothe adauza Kaziputa kuti adali kale ndi Puna choncho anayenera kukhala ndi  Punayo basi.  

Chamdothe adaonjezanso kuti n’kutheka kuti Kaziputa anali woyipa n’chifukwa chake  Zione adasankha Chamdotheyo. 

Kaziputa adamuuza Chamdothe kuti sakhalitsa naye Zione. 

Kaziputa adamuuzanso mnzakeyu kuti Zione ndi mtsikana wokongola choncho  sangakhale mkazi wa Chamdothe. 

Dama adalowerera mkanganowu ndipo adauza Chamdothe ndi Kaziputa kuti sadayenera  kukanganirana Zione popeza awa adali masewera chabe (zamasanje). Zikadakhala zenizeni,  makolo sakadawaloleza kuti azisowa kwa kanthawi.  

Kaziputa adamuyankha Dama kuti mudali zambiri m’masanje zoposa kungosewera za amayi  ndi abambo.  

Macheza otsiriza a Chamdothe ndi Zione 

Zione adafuna kudziwa chomwe chidamuchititsa Chamdothe kuti amusankhe kukhala  mkazi wake. Chamdothe adamuyankha kuti mwina ndi maphikidwe ake abwino abowa  komanso adalawa nkhanu zake. 

Zione adatsutsa ganizoli ponena kuti nkhanuzo adaphika sanali iyeyo.

Zione adafuna kudziwa ngati Chamdothe adawauza mayi ake za chibangiri chomwe  Zioneyo adamupatsa koma Chamdothi adati sadwauze amake popeza ankasowa  poyambira. Nkhaniyi idakwiririka ndi nkhani inzake yokhudza kaliyoliyo yomwe Zione  ankati amuuzabe Chamdothe panthawi yopuma. 

Kunja kudamveka mabingu ndipo Chamdothe adatsanzika Zione kuti azipita koma Zione  adamuuza kuti anali asadayimbe chimbo yotsekera masanje . 

Zione adamuuza Chamdothe kuti abisala m’nyumba yamasamba koma iye adamuyankha  kuti nyumba yamasambayo singamuteteze. 

Mayi a Chamdothe, Ndatopa, adayamba kumuyitana kudzera m’nyimbo ya “Chamdothe  thawa mvula.” Zione adathamanga ndi Chamdothe kuti akamusiye kwawo koma mnyamatayu adayamba kuwolowa nkumachoka chiwalo chimodzichimodzi mpaka udatsala  mutu wokha womwe udagwera pansi pamene Zione amawupereka kwa Ndatopa.  

MFUNDO ZIKULUZIKULU 

1) Kusasamala: Zione ankadziwa kuti Chamdothe sayenera kukhudza madzi kuopa kufa nawo  koma adalolera kumuchedwetsa mpaka kumunywesa ndi mvula ndipo imfa yake idali  yomweyo. 

2) Kudziyenereza: Kaziputa adauza Chamdothe kuti Zione anali mkazi wokongola wosayenera  kukhala mkazi wa Chamdothe koma iyeyo. 

3) Kudziteteza: Chamdothe atamva mabingu adadziwa kuti mdani wake, mvula, wayandikira  ndipo adatsanzika Zione kuti azipita kwawo ndipo pamene Zione adamuuza kuti akabisala  panyumba yamasamba, Chamdothe adamuyankha kuti nyumba yamasamba singamuteteze  ku mvula. 

4) Kukwaniritsa lonjezo: Zione atenge mutu Chamdothe pomwe anasungunuka ndi mvula  nakaupereka kwa amayi ake, Ndatopo. Umu ndi momwe adawalonjezera 

Mawu ena ofunika kuwaunikira 

  1. Chamdothe ankakhala moyo wosasangalala kwenikweni  

Nthawi zambiri ankavutitsidwa komanso kunyozedwa ndi Kaziputa.  Iye ankakhala mwa mantha makamaka poganizira kuti mdani wake wamkulu ndi madzi.  Kaziputa atamutengera mbuzi yake yadongo n’kupita nayo pamwala pakati pa mtsinje  

iye adamulondola koma ankayenda m’mbali mwa mtsinje poopa kuti anganyowe ndipo  anzake adamuthamangira nkumugwira kuti asalumphire m’madzi.  

Kunja kukaonetsa zizindikiro zoti mvula igwa iye amathawira kwawo mvulayo  isanayambe poopa kuti anganyowe n’kugumuka.  

  1. Fisi ali ndi bwenzi  

Kaziputa anali munthu woyamba dala anzake komabe anali ndi bwenzi lake Puna amene  amachita naye zinthu nthawi zambiri ndipo kumasewero amasanje anali mkazi wake.  Ndatopa adanyozedwa ndi mamuna wake Angozo pamene sankabereka komabe Mayi a  Lunda ankamumvetsa ndipo ankayesetsa kuti asamakhale ndi nkhawa. 

error: Content is protected !!
Scroll to Top