NUNSU YOYAMBA
Mgezenge ndi Nagama kunyumba kwawo
Mgezenge akudziyankhulira yekha ndipo adandaula zinthu izi:
▪ Miyendo inkamuphwanya ndipo inkatero kamba kakuti iye adakalamba.
▪ Miyendo yake imafunika kukhala m’mwamba.
▪ Akazi ena akamakula amavuta kwambiri. (Adayankhula izi popeza mkazi wake Nagama adachedwetsa kubweretsa mpando woti apachikepo miyendo.)
Madandaulo a Mgezenge pamene amakambirana ndi mkazi wake
▪ Mkazi wake, Nagama, adachedwetsa mpando woti ayikepo miyendo.
▪ Iye ankadwala kusowa chisamaliro.
▪ Kusowa chikondi ndi chisamaliro ndi matenda ndithu.
▪ Ulemu wochokera kwa mkazi wake umaperewera. (Amamutchula “amuna anga” m’malo mwa dzina lake “Mgezenge” pomuyitana ngakhale amalidziwa bwino dzinali.) ▪ Mkazi wakeyo amamuyankhula ali chilili.
Madandaulo a Nagama mkazi wa Mgezenge
▪ Adakumbutsa mamuna wake kuti iye anali kudwala mwakuti sankachitira dala kuchedwetsa kampando kopachikapo miyendo.
▪ Mgezenge, mamuna wake, sankamulabadira.
▪ Kumutchula mwamuna wake “Mgezenge” ndi ulemu
Zotumphuka pa zokambirana za Mgezenge ndi mkazi wake
▪ Mgezenge ankamuyankhula mkazi wake moopseza komanso mwaukali.
▪ Mgezenge ankanyinyirika ndi kudwala kwa mkazi wake mwakuti adamuopseza kuti akwatira mkazi wina popeza iye (mkaziyo) sanali kugwira ntchito zambiri.
▪ Ku mayiko ena monga ku Napal, Tibet, Sri Lanka ndi mbali zina za China, mkazi amatha kukwatiwa ndi amuna angapo. Mitala yochita mkaziyi imatchedwa Poliyandire.
▪ Banja la Mgezenge linali ndi zifuyo zambiri: ng’ombe zopitirira makumi asanu ndi awiri (70) komanso mbuzi zana limodzi ndi makumi awiri kudza mphambu zisanu ndi zinayi (129).
Umboni woti pamafunika munthu wothandiza ntchito pakhomo pa mgezenge ▪ Zifuyo zinalibe mbusa choncho zinkaononga m’minda ya wanthu.
▪ Zifuyo zimafunika munthu woti apite nazo ku dipi.
▪ Golosale imafunika dongosolo labwino.
Kumbutso
▪ Ngakhale pamafunika munthu woti athandize kugwira ntchito, monga kusamala ziweto pakhomo pa Mgezenge, yankho la vutoli silinali kukwatira mkazi wina monga amanenera Mgezenge.
▪ Pamene Nagama adauza mamuna wake Mgezenge kuti anali kuyankhula m’zining’a, Mgezengeyo adalusa nakunga chibakera n’kumuponyera mkazi wakeyo koma iye adzinda mwakuti Mgezenge adagwa pansi ndipo amaoneka kuti ankamva ululu kwambiri.
Mgezenge ndi Zikani
▪ Zikani adautukira naodira kunyumba kwa Mgezenge panthawi yomwe Nagama adazinda chibakera cha Mgezenge kachiwiri ndipo Mgezenge adagwa ngati chithumba.
▪ Zikani adathandiza Mgezenge kuti adzuke ndipo Mgezenge adamukumbatira mosonyeza chikondi. Izi zidachititsa Zikani kuti amukankhe Mgezenge ndipo adatsala pang’ono kugwanso.
▪ Zikani atawafunsa alamu ake a Mgezenge kuti afotokoze chomwe chinachitika kuti apezeke atagwa, Mgezenge adamuyankha kuti adaterereka pamene ankafuna kuti akhale pampando.
▪ Mgezenge asirira momufuna Zikani Pamene Zikani adatsanzika nayamba kuyenda kuti alondole mkulu wake Nagama kukhitchini, Mgezenge adadziyankhulira mawu otsatirawa akumuyang’ana: “Mulungu sungamumvetse. Adalenga munthu wamkazi kuti akhale wothangatira mamuna. Atamulenga mkaziyo, anapitiriza ndipo akupitiriza kumukongoletsa munthu wamkazi. Atsikana akubadwa masiku ano akuposa amawo kukongola. Ndipo Mulungu amati akalenga mwana wamkazi chaka chino, chaka chamawa amadzalenga njole yozunguza mutu. Atsikana amakono akamayenda amakhala ngati akuvina ndipo akamayankhula amakhala ngati akuimba nyimbo zanthetemya.”
Zotumphuka pa mkumano wa Mgezenge ndi Mayamiko
▪ Mayamiko adali mwana wa a Mackson Chikoya ndipo anali ndi zaka khumi ndi ziwiri (12). ▪ Mgezenge adagwirizana ndi bambo a Mayamiko kuti awapititsire nkhuni koma mtengo weniweni ndi kuchuluka kwa nkhuni (kukula kwa mtolo) sadagwirizane. Mayamiko adadziwa kuti mtolowo wakwanira pamene bambo ake adavomera ndi mutu pamene iye ankadutsa panyumba akupita kwa Mgezenge.
▪ Mayamiko ankachita malonda amakala.
▪ Mayamiko sadapite kusukulu popeza atate ake adamujombetsa kuti akasake nkhuni zomwe adakapereka kwa Mgezenge komanso zovala zake zinali zokuda mwakuti ankayembekezera kuti Mgezenge akampatsa ndalama zankhuni zomwe adapititsazo, akagule sopo wochapira pobwerera kwawo.
▪ Golosale ya Mgezenge idali yotseka ndipo Mgezenge adapsa mtima nati amuchotsa ntchito Funsani, mnyamata yemwe amagulitsa m’golosaleyi.
▪ Mgezenge amamukhulupirira Funsani.
Zipangizo m’gawoli
- Zifanifani
▪ Kumangoti amuna anga amuna anga muli pholi ngati mlongoti.
▪ Agwanso ngati chithumba.
▪ Osamathamangira kufunsa mafunso ngati aphunzitsi.
▪ Atsikana amakono akamayenda amakhala ngati akuvina
▪ Akamayankhula amakhala ngati akuimba nyimbo zanthetemya.
- Msemphano
▪ Zikani atawafunsa alamu ake a Mgezenge kuti afotokoze chomwe chinachitika kuti apezeke atagwa, Mgezenge adamuyankha kuti adaterereka pamene ankafuna kuti akhale pampando. Zoona zake n’zakuti Mgezenge adagwa pamene mkazi wake Nagama adazinda chibakera chomwe adamuponyera.
- Mvekero
∙ Pholi: chiimirire
MFUNDO ZIKULUZIKULU
- a) Bodza
∙ Zikani atawafunsa alamu ake a Mgezenge kuti afotokoze chomwe chinachitika kuti apezeke atagwa, Mgezenge adamuyankha kuti adaterereka pamene ankafuna kuti akhale pampando.
- b) Kusirira
∙ Mgezenge ankamusirira kwambiri Zikani mwakuti pamene ankamudzutsa atagwa pamene Nagama adazinda chibakera chomwe adamuponyera, adamukumbatira mosonyeza chikondi.
- c) Kuyipa kwa kuononga chilengedwe
∙ M’mudzi m’mene ankakhala Mgezenge ndi anthu ena mitengo idatha ndipo idayamba kusowa kamba ka m’chitidwe wootcha ndi kugulitsa makala.
- d) Nkhanza
∙ Mgezenge adafuna kumenya mkazi wake pazifukwa zosakwanira.
- e) Kukhulipirira wantchito
∙ Mgezenge adamusiyira Funsani makiyi akugolosale.
- f) Kumvera makolo
∙ Bambo Chikoya adamujombetsa mwana wawo Mayamiko kuti akasake nkhuni ndipo akazitule kwa Mgezenge. Mayamiko adajombadi nachita zomwe adauzidwa ndi atate ake.
- g) Kuganiza mosiyana
∙ Nagama ankamuyitana mamuna wake Mgezenge pomutchula kuti “amuna anga” ndipo adaona kuti ankachita ulemu poteropo.
∙ Mgezenge sankasangalatsidwa ndi mchitidwewu ndipo adauza mkazi wakeyo kuti ndi mwano kuti azimutchula “amuna anga” chonsecho dzina lake anali kulidziwa.
NUNSU YACHIWIRI
Zotumphuka pamacheza a Nagama ndi Zikani
▪ Nagama adadabwa kuti Zikani adafika kunyumba kwake panthawi yomwe anayenera kupezeka m’kalasi kusukulu.
▪ Zikani adathangitsidwa kusukulu popeza sadapereke ndalama zochitira chitukuko pasukulu (monga kumanga zimbudzi) komanso zogulira bukhu lomwe adataya.
▪ Bukhu lomwe Zikani anayenera kulipira lidasowa pamene iye adapita kukadzithandiza kuchimbudzi.
▪ Pasukulu pomwe Zikani ankaphunzira pamafunikadi zimbudzi zoonjezera popeza ophunzira ankakhala pamzere wautali nkumadikirana kuti alowe ku zimbudzi zomwe zinalipo.
▪ Nagama adandaula zinthu zotsatirazi malingana ndi kubedwa kwa bukhu la Zikani:
✔ Kuba ndi koipa m’dziko popeza kumachititsa kuti mwini katundu avutike.
✔ Anthu amene amakhala akuba pasukulu sasiya mwansanga.
✔ Anthu amene akuba makonowa adayamba m’chitidwewu adakali ana.
∙ Makolo a Zikani ankadalira banja la Nagama pankhani zachuma.
∙ Mkazi akalowa m’banja kamba ka umphawi, amakhalira kumulambira mamunayo. ∙ Mgezenge akakwiya ndi chinthu, mkwiyo umathera pa mkazi wake Nagama. ∙ Nagama amakhala mwamantha ndi mamuna wake koma ankamumasukira mchemwali wake Zikani.
MAPHUNZIRO M’NUNSUYI
- Kuba ndi koipa m’dziko popeza kumachititsa kuti mwini katundu avutike. ∙ Wophunzira wina adaba bukhu la Zikani kotero kuti Zikani anayenera kulipira. 5. Kudalira
∙ Zikani adadalira makolo ake kuti amupatsa ndalama zochitira chitukuko pasukulu komanso zolipirira bukhu lomwe adataya.
∙ Makolo a Zikani ankadalira kwambiri banja la Mgezenge ndi Nagama pankhani zachuma.
∙ Zikani adadalira mnzake kuti amuyang’anira bukhu pamene iye adapita kukadzithandiza.
6. Nkhanza
∙ Mgezenge chilichonse chikamuvuta, mkwiyo umadzathera pa mkazi wake.
5. Kuba
∙ Zikani aberedwa buku lake kusukulu pomwe analisiya atapita ku chimbuzi kukazithandiza
Zipangizo
- Mikuluwiko
∙ Wamva m’mimba ndiye atsekula kukhomo: Amene ali ndi vuto ndipo akufuna chithandizo mwansanga, akuyenera kuchitapo kanthu.
∙ Wopempha safulumira: Wopempha amayendera maganizo a wopereka chithandizoyo.
2. Msemphano
∙ Azimayi am’mudzi ankachitira nsanje Nagama ponena kuti adakwatiwa ndi mamuna wolemera (adakwatiwa n’kumbuyo komwe). Azimayiwa sankadziwa kuti Mgezenge anali mamuna wovuta mwakuti Nagama ankavutika ndipo amakhala moyo womulambira. Chilichonse chikamuvuta, mkwiyo umadzathera pa mkazi wake.
NUNSU YACHITATU
Mgezenge ndi Funsani ku golosale
∙ Mgezenge adakwiya kwambiri popeza Funsani sanatsekule golosale ndipo pamene adatulukira adamutchula kuti ndi wopusa.
∙ Funsani sadatsekule golosale chifukwa ankadwala ndipo adapita kukalandira thandizo lamankhwala kuchipatala. Mgezenge sadamve izi: adangoti Funsani ndi wopusa komanso waulesi.
∙ Mgezenge adauza Funsani kuti achite sitoko patsikulo ngakhale kuti Funsaniyo sankadziwa tanthauzo lake.
∙ Mgezenge adayankhula kuti makolo a Funsani ankagwira ntchito pa esiteti ya Mgezenge koma adapititsidwa ku esiteti ya mnzake wa Mgezenge kutali. Pochoka iwo adavomereza kuti Funsani atsale azigwira ntchito mgolosale ya Mgezenge.
∙ Ngakhale Funsani adamuuza Mgezenge kuti cholembera chomwe adachipeza m’thumba mwake adachita kugula kuti azilembera, Mgezenge sadamumvere ndipo adamuchotsa ntchito namuuza kuti malipiro ake ndi cholembera chomwe adatengacho.
MAPHUNZIRO M’NUNSUYI
- Nkhanza
∙ Mgezenge adamulemba ntchito Funsani ngakhale adali mwana wazaka khumi ndi ziwiri (12).
∙ Mgezenge adamunyoza Funsani pamene sadatsegule golosale kamba koti adapita kuchipatala kukalandira thandizo lamankhwala pamene adadwala malungo. ∙ Mgezenge adachotsa ntchito Funsani popanda zifukwa zokwanira.
∙ Mgezenge adamukwenya pakhosi Funsani ndipo sadampatse malipiro pamene adamuchotsa ntchito ponena kuti malipiro ake ndi cholembera chomwe chidapezeka m’thumba lake.
- Kukayikira/Kuganiza molakwika
∙ Mgezenge adauza Funsani kuti makolo ake povomereza zomusiya kuti azigwira ntchito mugolosale ya Mgezenge adagwirizana zoti amubere.
- Umphawi umachititsa munthu kuti aganize moperewera.
∙ Makolo a Funsani adavomereza zomusiya mwana wawo wazaka khumi ndi ziwiri kuti azigwira ntchito m’golosale ya Mgezenge pamene iwo amatumizidwa kukagwira ntchito kutali ku esiteti ya mnzake wa Mgezenge, zotsatira zake Mgezenge adamuchita nkhanza mwanayo. Zipangizo
Matanthauzo a mawu
∙ Malungo adandithyola mafupa: Malungo anandivuta zedi
∙ Ndipsi: wakuba
∙ Sitoko: Kuwerengera katundu yemwe watsala m’shopu pofuna kupeza katundu amene watuluka ndi kufananitsa ndi ndalama zomwe zilipo katunduyo atagulitsidwa.
NUNSU YACHINAYI
Zotumphuka pa kucheza kwa Abiti ndi Gama kunyumba kwawo pambuyo pa msonkhano wa kwa Agulupu
∙ Monga Mgezenge, naye Gama anali wosachedwa kupsa mtima ndipo mkazi akamamuyankhula ali chilili amatanthauzira kuti ndi mwano.
∙ Mkazi wake, Abiti, atayankha kuti si amfumu amene adapereka chigamulo cha nkhani yamunda iye adapinda chibakera namuloza nacho nkumuuzanso kuti safuna zopusa. ∙ Chitukuko chamsewu ndi chomwe chidautsa mapiri pachigwa.
∙ Amfumu (Agulupu Watison Kajiyanike Jere) adauza Gama kuti msewu udutsa m’munda mwake ndipo “Road Reserve Boundary” imadyanso gawo lalikulu zedi lamundawo. ∙ A Gulupu Watison Kajiyanike Jere ankaopedwa m’mudzi kamba ka zamatsenga zomwe
adamuchita mlamu wawo (atawalakwira nkukana kupepesa, adangomutchula dzina ndipo iye adachita khungu ali kutauni).
∙ Anthu m’mudzimu adaononga mitengo ndi malonda amakala.
∙ Agulupu adayankhula anthu mwamwano komabe adayankhula chilungamo.
Mgezenge akumutula Nagama kwa makolo ake
∙ Adatulukira atamugwira padzanja ndipo adayankhula mwamwano ndi makolo a Nagamayo kuti akudzamusiya koma a Gama adamuyankha mwaukali namuuza kuti akhale pansi popeza sakadagona usiku ngati sakadathana naye masana atsikulo.
∙ Nagama adandaula kuti Mgezenge adamumenya usiku wonse.
∙ Mgezenge adapereka dandaulo lake kudzera m’zining’a ziwiri: mpando ndi mbalame. (Munthu amene ali ndi mpando koma nkumagona pansi, mutu wake ndi wosakoka. Mbalame yomwe ili ndi chisa koma ikuopa kugona poti muli njoka, singalimbe mtima kuti ilowemo m’chisamo.) Apa Mgezenge amafuna kutanthauza kuti sakukhala pamodzi ndi mkazi wake monga banja kamba ka zovuta zina zomwe kwa iye zinali zosakwanira.
Zotumphuka pazokambiranazi
∙ Mgezenge ndi Gama anali amuna osachedwa kupsa mtima.
∙ Mkazi wa Gama, Abiti, amatsatira nkhani ndipo amamvetsa zinthu.
∙ Abiti ndi mamuna wake Gama ankakomedwa ndi chuma cha Mgezenge mwakuti sanali kukonza mavuto a banja la mwana wawo Nagama moyenera. Iwo amalimbikira kumuuza Nagama kuti sakufuna kuti awathawitsire mkamwini wabwinobwinoyo.
∙ Mgezenge ankamufuna kwambiri Zikani.
∙ Abiti ndi mamuna wake anali wokonzeka kumupereka mwana wawo Zikani kwa Mgezenge kuti akhale mkazi wake wachiwiri n’cholinga choti apitirize kulandira ndalama zake.
Zomwe zidachititsa Makolo a Nagama kuti achite Shazi/Mbirigha/Isakulwa/Nthena ∙ Nagama adakhala pafupifupi chaka chathunthu asakupeza bwino mwakuti Mgezenge sanali kulowa m’nyumba.
∙ Samafuna kuti Mgezenge ayambe kuzemberana ndi akazi adera.
Matenda a Nagama
∙ Amatsegula m’mimba, ankangomva thupi kuphwanya komanso amadwala malungo pafupipafupi.
Umboni woti Abiti ndi Gama amafuna Mgezenge akwatirenso Zikani Pamene Mgezenge adadzamutula Nagama kunyumba kwawo, makolowa adamuuza Nagama zinthu zotsatirazi:
∙ Munthu akaweta galu amayenera kumupatsa chakudya zonse chifukwa akapanda kutero amagwira nkhuku za eni.
∙ Mlimi wang’ombe yamkaka amayenera kuyipatsa msipu ndi chakudya china choyenera ngati akufuna izimupatsa mkaka wambiri ndipo ayenera kuonetsetsa kuti ng’ombeyo sikuchoka m’khola.
∙ Akatswiri ankhondo amene amadumpha m’ndege yatombolombo; amene amadumpha ndi chipangizo chokhala ngati chiambulera sangabwerere m’ndege adadumphamo kale. ∙ Adamuuza Zikani kuti akufuna kuchita mwambo wa “Shazi” ndipo adamufotokozera momveka bwino zifukwa zomwe iwo amafunira kuchita mwambowo.
Zipangizo
- Zifanifani
∙ Mukungoberekana ngati makoswe: Mukuberekana kwambiri
- Zining’a
∙ Chiunda (kankhunda kakang’ono): Zikani
∙ Nkhunda yayikulu: Nagama, mkazi wa Mgezenge
∙ Akuthandize kusenza mtolo: Azigona ndi mamuna wako kuti aleke kudandaula ∙ Mwamuna azingoyang’ana kudenga: Azingokhala osagona ndi mkazi wake. ∙ Mgodi: Popezera ndalama ndi thandizo lina lofunikira
∙ Kuwedza chambo chonona kenako n’kuchitayira m’madzi momwemo: Kupeza mamuna wachuma ndi kumusiyanso
∙ Sakulowa m’nyumba: Sakugona ndi mkazi wake monga banja.
∙ Kutaya bomwetamweta: Kutaya mamuna wopezapeza
∙ Zidzete: Zitsiru/Opusa/Opepera
- Mikuluwiko
∙ Zengerezu adalinda kwawukwawu: Chidodo chimabweretsa mavuto.
∙ Munthu akaweta galu amayenera kumupatsa zakudya nthawi zonse chifukwa akapanda kutero amagwira nkhuku za eni: Mgezenge, pamene adakwatira Nagama, anayenera kupatsidwanso Zikani ngati Nagamayo samakwanitsa zinthu zoyenera m’banjamo poopetsa kuti angatenge mkazi wadera osati m’bale wake wa Nagamayo.
∙ Mlimi wang’ombe yamkaka amayenera kuyipatsa msipu ndi chakudya china choyenera ngati akufuna izimupatsa mkaka wambiri ndipo ayenera kuonetsetsa kuti ng’ombeyo sikuchoka m’khola: Kuti Mgezenge apitirize kupereka ndalama zambiri kwa apongozi ake, apongoziwo anayenera kumupatsanso Zikani ngati mkazi wabasera/wabanyira.
∙ Akatswiri ankhondo amene amadumpha m’ndege yatombolombo; amene amadumpha ndi chipangizo chokhala ngati chiambulera sangabwerere m’ndege adadumphamo kale:
Makolo a Zikani adachita chisankho chochita mwambo wa Shazi mwakuti sakadathanso kubwerera m’mbuyo n’kusintha maganizo kamba ka maganizo a Zikaniyo.
MAPHUNZIRO M’NUNSUYI
- Mwano
∙ A gulupu adayankhula mwamwano kuti iwo sangakulitse dziko, pamene anthu ankawadandaulira kuti asowa malo olima malingana ndi kubwera kwa msewu.
2. Ndalama ikayankhula, chilungamo chimakhala chete.
∙ Mgezenge amapereka ndalama zambiri kwa apongozi ake ndipo patsiku limene adapita ndi madandaulo ake nkukamusiya Nagama, adatenganso ndalama zambiri nawapatsa amayi ake. Ndalama zimenezi zidachititsa kuti makolo asaganizire bwino mavuto omwe mwana wawo amakumana nawo kubanja. Iwo adaganiza zopereka Zikani, mng’ono wake wa Nagama kwa Mgezenge kuti akhale mkazi wake wachiwiri n’cholinga choti azilandirabe ndalama.
- Nkhanza
∙ Makolo a Zikani adamusiyitsa sukulu mtsikanayu kuti akwatiwe ndi mlamu wake Mgezenge.
∙ Mayi a Nagama adamuuza kuti alibe mphamvu zowatsutsa pamene iwo ankamuuza za ganizo loti Zikani alowe m’nyumba mwake ngati mkazi wachiwiri wa Mgezenge. ∙ Mgezenge amafuna adzilowa m’nyumba ngakhale mkazi wake anali akudwala.
4. Dyera
∙ Abiti adauza Nagama kuti sankafuna zoti Mgezenge akwatire kwina; akhalebe m’banja lawo kuti ateteze chuma.
- Ufulu
∙ Zikani adauza bambo ake kuti anali ndi ufulu wopitiriza maphunziro mwakuti atate akewo sangamukakamize zokalowa m’nyumba mwa Mgezenge mlamu wake ngati mkazi wake wachiwiri.
- Kusamva maganizo a ena
∙ Makolo a Zikani sadafune kumva maganizo a mwana wawo pamene ankamupereka ngati shazi kwa Mgezenge. Kuonjezera apo, a Gama adatsindika pomuuza Zikani kuti zimene iwo alamula, alamula basi; palibe alandulepo.
Matanthauzo amawu
∙ Mbirigha: Mkazi wabasera/wabanyira kwa mamuna pomuthokoza mamunayo kamba ka mtima wake wabwino kapena wothandiza.