AGWIRIZANITSI
Mgwirizanitsi: Phatikizo limene limasonyeza mgwirizano pakati pa dzina kapena mlowam’amalo ndi mawu ena m’chiganizo.
Chitsanzo: Malani wataya mchere wathu.
MITUNDU YA AGWIRIZANITSI
-
Wamwininkhani:
-
: Mphatikiram’mbuyo wamneni yemwe amasonyeza mgwirizano pakati pa yemwe wachita ntchito (mwininkhani) ndi mneniyo.
-
Zitsanzo:
-
Ntchentche zimafalitsa matenda akamwazi.
-
Agalu amawuwa zedi usiku.
-
-
-
Wapamtherankhani:
-
: Mphatikiramkati wamneni yemwe amasonyeza mgwirizano pakati pa yemwe akuchitidwa/akuchitiridwa ntchito (pamtherankhani) ndi mneniyo m’chiganizo.
-
Zitsanzo:
-
Amayi adatifunsa mafunso ovuta zedi.
-
Tawona amandikonda ndithu.
-
-
Kumbutso: Mgwirizanitsiyu amatha kukhala mphatikiram’mbuyo ngati mneni ali m’kachitidwe kawochitidwa.
-
Chitsanzo: Mitengo yadulidwa ndi Akimu.
-
-
Waumwini:
-
: Mphatikiram’mbuyo kutsinde la umwini yemwe amaonetsa mgwirizano pakati pa dzina ndi mawu amene akusonyeza umwini wachinthu chomwe chikutchulidwa ndi dzinalo.
-
Zitsanzo:
-
Mwana wanu wavuula nyama yathu.
-
Chovala chanu chilibe lamba.
-
-
-
Wowerengera:
-
: Mphatikiram’mbuyo kutsinde lowerengera yemwe amagwirizanitsa mawu owerengerawo ndi dzina lomwe likutchula zinthu zomwe zikuwerengedwazo.
-
Zitsanzo:
-
Ana atatu athawa sabata yatha.
-
Mundipatseko mphangala ziwiri.
-
-
-
Woloza:
-
: Mphatikiram’mbuyo kutsinde loloza amene amasonyeza ubale pakati pa mawu olozawo ndi dzina la chinthu chomwe chikulozedwa m’chiganizomo.
-
Zitsanzo:
-
Mtsikana uyu ndi chilandamoyo.
-
Kamwana aka kamandisautsa.
-
Mutiphere nkhuku iyo.
-
-
-
Waubale / wamgwirizano:
-
: Mphatikiram’mbuyo kutsinde lamgwirizano/ubale ndipo amadalira gulu ladzina pofuna kugwirizana ndi dzinalo.
-
Zitsanzo:
-
Mandala ndiye asankhe zipokolo zomwe ndikuzifuna.
-
Sukulu imene ndidaphunzira ndi yabwino.
-
-
-
Wamfotokozi:
-
: Uyu ndi mphatikiram’mbuyo ku tsinde la mfotokozi ndi mawu ena, timapangira afotokozi kuchokera kumasinde a afotokozi ndi mawu ena ndipo amagwirizanitsa mfotokozi ndi dzina lomwe akulikamba.
-
Zitsanzo:
-
Usavale buluku lofiira.
-
Ndikwatira mkazi wokuda.
-
Watenga choko chachifupi.
-
-
-
Wodzichitira:
-
Mphatikiramkati wamneni yemwe amasonyeza kuti ntchito yabwerera kwa yemwe akuyichita.
-
Zitsanzo:
-
Zuze wadziphunzitsa.
-
Kazimire adadzikhapa.
-
-
MAFUNSO
-
Kodi agwirizanitsi angagwiritsidwe ntchito bwanji mu masinda?
-
Chimodzi mwa zitsanzo zomwe mungapereke pa wamwininkhani?
-
Ndi mawu otani amene angagwirizane pa wapamtherankhani?
-
Ndi mtundu wotani wa agwirizanitsi umene umakhalapo mu mawu owerengera?
-
Kodi zimenezi zimathandiza bwanji mukamalankhula?