AKAPANDAMNENI
Kapandamneni ndi gulu la mawu lomwe silikhala ndi mneni wosintha nthawi ndipo nthawi zina limagwira ntchito ngati mtundu wamawu.
Zitsanzo:
- Tikupita ku Zomba.
- Samakonda kudya mbatata.
- Adabwera usiku zedi.
- Ankatafuna ngati nkhumba.
- Mwana wa abusa athu amatukwana zedi.
MITUNDU YA AKAPANDAMNENI
Kuti tidziwe mtundu wakapandamneni, tiyenera kuyeza mawu omwe ali paphata la kapandamneniyo.
- Wadzina: Amayamba ndi dzina ndipo amagwira ntchito ngati dzina.
- Zitsanzo: Mwana osamvera malangizo amachititsa manyazi makolo.
- Wamfotokozi: Mawu apaphata pake ndi mfotokozi ndipo amagwira ntchito ngati mfotokozi.
- Zitsanzo: Nkhuku yosayikira pakhomo imadyedwa ndi zilombo.
- Wamuonjezi: Amagwira ntchito ngati muonjezi, ngakhale kuti sinthawi zonse amayamba ndi muonjezi.
- Zitsanzo: Amayenda ngati chitsiru.
- Wamperekezi: Ili ndi gulu lamawu lomwe limayamba ndi mperekezi.
- Zitsanzo: M’chiuno mwa mwana simufa nkhuku.
- Wamfuwu: Amayamba ndi mfuwu ndipo amagwira ntchito ya mfuwu.
- Zitsanzo: Kalanga ine! Ndavulala.
- Wamneni wosasintha nthawi: Mawu apaphata pake amakhala mneni wosasintha nthawi.
- Zitsanzo: Ndidalephera kupita kusukulu.