ALUMIKIZI
Awa ndi mawu amene amalunzanitsa mawu ndi mawu anzake, kapandamneni ndi kapandamneni, chiganizo ndi chiganizo komanso nthambi za chiganizo ndi nthambi zinzake. Mawu omwe akulumikizidwawo amakhala amitundu yofanana monga dzina ndi dzina, mneni ndi mneni, mfotokozi ndi mfotokozi, muonjezi ndi muonjezi, mlowam’malo ndi mlowam’malo.
Zitsanzo:
- Wavala malaya ong’ambika komanso okuda.
- Amayi ndi abambo apita kudimba.
MITUNDU YA ALUMIKIZI
- Olumikiza mawu: Amalumikiza mawu ofanana mtundu komanso mphamvu monga dzina ndi dzina kapena mfotokozi ndi mfotokozi mnzake.
Zitsanzo:
- Ankadya mwachangu komanso mwauve.
- Mukandigulire zovala ndi zakudya.
- Olumikiza akapandamneni: Amalumikiza akapandamneni ku ziganizo ndi mawu ena.
Zitsanzo:
- Tikaimbe nyimbo zabwino ndiponso zogwira mtima.
- Adatitumizira maungu okoma ndi mphonda zowawasa.
- Olumikiza ziganizo: Amalumikiza ziganizo ku ziganizo zina.
Zitsanzo:
- Mudye ndipo mukhute.
- Tinasewera komanso tinamwa.
- Mukamutenge osati mukam’menye.
NTCHITO ZA ALUMIKIZI
- Kupatula/kulekanitsa
Zitsanzo:
- Ukanditengere therere osati masamba amaungu.
- Muyenera kumulangiza osati kumuchotseratu.
- Kuonkhetsa/kuphatikiza
Zitsanzo:
- Aphunzitsi awa ndi aulemu komanso akhama.
- Ndidalima ndiponso ndidakolola zambiri.
- Kusiyanitsa:
Zitsanzo:
- Katoleni ndi wachibwana koma ndi wanzeru.
- Mwanayu ndi wamwano komabe ali ndi chikondi.
- Ngwangwa ndi wamfupi pamene Timve ndi wamtali.
- Amamva koma alibe chidwi.
- Kusonyeza kupeneka
Zitsanzo:
- Timugulire Malaya kapena buluku.
- Nyembazi zitha kukwanira anthu asanu kapena anayi.
- Kusonyeza zotsatira
Zitsanzo:
- Sankawerenga choncho mayeso amuvuta.
- Mvula idagwa mwakuti tidakolola chimanga ndi mtedza wambiri.
- Kusonyeza chifukwa
Zitsanzo:
- Sindibwera kuphwandoko chifukwa ndadwala.
- Popeza ukuchita mtudzu, sudya nawo mondokwayu.
- Kusonyeza cholinga
Zitsanzo:
- Tikulandira mbewu kuti tikadzale kudimba.
- Timapereka msonkho kuti tithandize boma lathu.
- Kusonyeza pokhapokha
Zitsanzo:
- Mudzalandira ngati mungapemphe ndi mtima wonse.
- Ndimupatsa ngati atabwere kuno.
Kumbutso: Nthawi zina mtundu wa mulumikizi umatengera ntchito yomwe akugwira.
Zitsanzo:
- Adandiyitanira kunyumba kwake kuti akandifotokozere bwino. (mulumikizi “kuti” ndi wosonyeza cholinga)