Aonjezi
-
Definition: Aonjezi ndi mawu omwe amawonjezera kuchuluka kapena mawu ena, komanso akufotokoza momwe, malo, nthawi, kapena kuchuluka kwa zomwe zikuchitika.
Mitundu ya Aonjezi
-
Amalo (Malo): Amasonyeza malo komwe ntchito ikuchitika.
-
Zitsanzo:
-
Upite kumudzi ukapereke ndalama.
-
Adabisala pachitsamba.
-
-
-
Amakhalidwe/amchitidwe (Chitidwe): Amakamba za momwe ntchito ikuchitikira, akuyankha funso loti “bwanji?” kapena “motani?”
-
Zitsanzo:
-
Ife tafika bwino.
-
Ankawerenga mofulumira.
-
-
-
Anthawi (Nthawi): Amasonyeza nthawi yomwe ikuchitika, akuyankha funso loti “liti?” kapena “nthawi yanji?”
-
Zitsanzo:
-
Tinkatafuna mondokwa powerenga.
-
Chiyanjano adamwalira usiku.
-
-
-
Ofunsa (Ofunsa): Amafunsa zamalo, mchitidwe, nthawi, ndi kuchuluka.
-
Zitsanzo:
-
Ukupita kuti?
-
Wafera pati?
-
-
-
Amuyeso (Kuchuluka): Amapima (amayesa) kuchuluka kapena kuchepa kwa momwe ntchito ikuchitikira.
-
Wowerenga (Kuwonjezera):
-
Ndagogoda kawiri koma sananditsegulire.
-
Titadya katatu, tidakhuta ndithu.
-
-
Wochulutsa (Kuchepetsa):
-
Amapita kawirikawiri.
-
Mudye pang’ono nsimayo.
-
-
-
Otsimikiza/otsindika (Chitsimikizo): Amatsimikiza kuchitika kwa ntchito.
-
Zitsanzo:
-
Tibwera ndithu, musakayike.
-
Adavala malaya okongola ndithu.
-
-
-
Okayika/openeka (Kuyika mu nkhawa): Amakayika kapena kupeneka zakuchitika.
-
Zitsanzo:
-
Mwina, abwera.
-
Iye kapena apita yekha.
-
-
-
Ovomera kapena kukana (Vomera/Kana): Amavomera kapena kukana zakuchitika.
-
Zitsanzo:
-
Zoonadi, Salamanda ndi ineyo.
-
Ayi, sitingagwade kwa milungu yakufa.
-
-
Kapangidwe ka Aonjezi
-
Kuchokera kumayina: Poyika aphatikiram’mbuyo “mwa-,” “ku-,” “pa-,” ndi “mu-” ku mayina.
-
Zitsanzo:
-
Chombo amayankhula mwanzeru.
-
Tiyeni tikachezere kumbali.
-
-
-
Kuchokera ku masinde a afotokozi: Aonjezi amapanga poyika aphatikiram’mbuyo “ku-,” “pa-,” ndi “mwachi-.”
-
Zitsanzo:
-
Ku- → -tali: Kutali.
-
Pa- → -ng’ono: Pang’ono.
-
Mwachi- → -kulu: Mwachikulu.
-
-
-
Kuchokera ku aneni: Amapangidwa poyika aphatikiram’mbuyo “mo-,” “po-,” ndi “cho-.”
-
Zitsanzo:
-
Mo- → -yenda: Moyenda.
-
Po- → -gona: Pogona.
-
Cho- → -thamanga: Chothamanga.
-
-
-
Kuchokera ku aonjezi ena: Poyika “mwa-” ku aonjezi ena.
-
Zitsanzo:
-
Mwa- → -chabe: Mwachabe.
-
Mwa- → -udyo: Mwaudyo.
-
Mwa- → -dala: Mwadala.
-
-
-
Kuchokera kumasinde osiyanasiyana:
-
Osonyeza malo: Kuyika aphatikiram’mbuyo “ku-,” “pa-,” ndi “mu-” kumasinde amalo.
-
Zitsanzo:
-
Ku- → -no: Kuno.
-
Pa- → -no: Pano.
-
Mu- → -no: Muno.
-
-
-
-
Owerengera: Kuyika aphatikiram’mbuyo “ka-” ndi “kachi-” ku masinde owerengera.
-
Zitsanzo:
-
Ka- → -modzi: Kamodzi.
-
Kachi- → -wiri: Kachiwiri.
-
-