MSCE Chichewa Galamala Form 3 and 4

DZINA

Mawu otchulira kapena kuyitanira chinthu chilichonse: chamoyo kapena chopanda moyo, chowoneka kapena chosaoneka, chokhudzika ngakhale chosakhudzika.
Zitsanzo: Zomba, nyenyezi, mzeru, munthu, Mangochi, nsomba, tsabola.

MITUNDU YAMAYINA

  1. Dzina lamwinimwini:

  • Dzina lotchulira munthu, chinthu kapena malo ndipo limayamba ndi chilembo chachikulu.

  • Zitsanzo: Zomba, Malosa, Shire, Chikumbutso, Zambia.

  1. Dzina lopanda mwinimwini:

  • Dzina lotchulira munthu aliyense kapena chinthu chilichonse molingana ndi mayina agulu lake kapena mtundu wake.

  • Mayina awa sayamba ndi lembo lalikulu pokhapokha ngati akutsekulira chiganizo.

  • Zitsanzo: thabwa, buluzi, namwali, mamuna, nkhuku, dothi, mtengo, galimoto.

  1. Dzina lachinthu chokhudzika:

  • Limayimira chinthu chomwe tithe kuchiona komanso kuchikhudza (chamoyo kapena chopanda moyo).

  • Zitsanzo: nyama, phiri, munthu, agogo, udzu, masamba, khoma, chingwe.

  1. Dzina lachinthu chosakhudzika:

  • Limayimira chinthu chomwe sitingathe kuchiona kapena kuchikhudza.

  • Zitsanzo: nzeru, chisoni, ulesi, uve, chidani, umunthu, uchitsiru.

  1. Dzina launyinji:

  • Limayimira zinthu zapagulu osati chimodzichimodzi ayi.

  • Zitsanzo: mkoko, phava, mpingo, msambi, mtolo, mzukutu, khwimbi, namtindi, khamu.

NTCHITO ZAMAYINA

  1. Kukhala mwininkhani:

  • Dzina limakhala mwininkhani ngati likuchita ntchito m’chiganizo.

  • Chitsanzo: Chisomo wapha nkhuku.

  1. Kukhala pamtherankhani:

  • i) Wachindunji: Dzina lomwe likuchitidwa ntchito m’chiganizo (dzina lomwe ntchito yamneni yachitikira molunjika).

    • Chitsanzo: Chisomo wapha nkhuku.

  • ii) Wopanda chindunji: Dzina lomwe likuchitiridwa ntchito m’chiganizo (mlandirakanthu).

    • Zitsanzo: Bengo waphera Thokozani ziwala.

    • Amayi agulira mwana chiboolamoyo.

  • iii) Wamperekezi: Amatsatana ndi mperekeziyo.

    • Zitsanzo: Tidamgwaza ndi chisongole.

    • Adabisala kuseri kwa mpanda.

  1. Kuyitanira:

  • Zitsanzo: Khama, tabwera ndikutume.

  • Atate, ndipatseniko mtedzawo.

  1. Kusonyeza umwini wachinthu:

  • Zitsanzo: Adatenga mazira a nkhanga.

  • Wadya phala la mwana.

  1. Kusonyeza malo:

  • Zitsanzo: Kumudzi kwathu kulibe ufiti.

  • Pasukulupa pali mbava zambiri.

  1. Kukhala mtsirizitsi (mtsirizo/mtsiriza tanthauzo lamneni):

  • Zitsanzo: Alinafe adali chiphadzuwa.

  • Mayilosi ndi mnyamata wabwino zedi.

  • M’khola muli ng’ombe ziwiri.

MAFUNSO

  1. Chimodzi mwa zitsanzo zoti zingagwirizane ndi dzina lamwinimwini ndi chiyani?

  2. Ndi mawu otani amene angawoneke mu dzina lachinthu chokhudzika?

  3. Kodi ndi mawu otani omwe angachitidwe ntchito monga wopanda chindunji?

  4. Mungapereke zitsanzo ziti pa kukhala mtsirizitsi?

  5. Kodi dzina lopanda mwinimwini lili ndi tanthauzo lotani pa ntchito yamene limagwiritsidwa ntchito?

MAYINA AZINTHU ZAZIMUNA NDI ZAZIKAZI

  • Bambo – Mayi

  • Mchimwene – Mchemwali

  • Mkwati – Mkwatibwi

  • Mfumu – Mfumukazi

  • Muphwa – Mfumakazi

  • Tonde – Mkota

  • Chipsolopsolo – Msoti

  • Tambala – Thadzi

  • Muna – Mbombe

  • Mtsibweni/malume/mjomba – Zakhali

  • Gojo/gocho – Chumba

  • Bwana – Dona

  • Tatavyala – Mpongozi

  • Mkamwini – Mtengwa/mkamwana

  • Wakunjira – Namkungwi

  • Mwamuna – Mkazi

  • Mnyamata – Mtsikana

  • Tate – Mayi

  • Ndoda – Ntchembere

  • Kapolo – Mdzakazi

  • Mntheno/mfule – Mzidzi

  • Mzambwe – Nkhunda

MAYINA OYIMIRA CHACHIMUNA KAPENA CHACHIKAZI

  • Mlamu

  • Nkhalamba

  • Munthu

  • Msuwani

  • Gogo

  • Mdzukulu

  • Mwana

  • Mphunzitsi

  • Dotolo

MAGULU AMAYINA

a. Mu-, a- (Wa-)

  • Chimodzi / Zambiri

    • Mkulu / Akulu

    • Mkwatibwi / Akwatibwi

    • Mwana / Ana

    • Mlimi / Alimi

    • Mphunzitsi / Aphunzitsi

    • Mlendo / Alendo

b. Mu-, Mi-

  • Chimodzi / Zambiri

    • Mkate / Mikate

    • Mkute / Mikute

    • Mleme / Mileme

    • Mkeka / Mikeka

    • Mulungu / Milungu

Note: Pali mayina ena m’gululi omwe saonetsa kuti ali m’chimodzi kapena m’zambiri ngakhale kuti amachulukitsidwa molakwika ndi “ma”.

  • Zitsanzo: mwano, mchenga, mkodzo, moto, mpweya, mtedza, mwavi, msuzi, mpunga, mchere

c. U-, Ma-

  • Chimodzi / Zambiri

    • Udindo / Maudindo

    • Uta / Mauta

    • Una / Mauna

Note: Pali mayina ena am’gululi amene saonetsa chimodzi kapena zambiri ndipo sachulukitsidwa.

  • Zitsanzo: udzu, umunthu, ufa, udzudzu, uchitsiru, ukadaulo

d. I-, Zi

  • Chimodzi / Zambiri

    • Mbale / Mbale

    • Nyemba / Nyemba

    • Mfuti / Mfuti

    • Mvula / Mvula

    • Nyumba / Nyumba

    • Njinga / Njinga

    • Mbala / Mbala

    • Nyerere / Nyerere

e. Chi-, Zi-

  • Chimodzi / Zambiri

    • Chulu / Zulu

    • Chola / Zola

    • Chiguduli / Ziguduli

    • Chaka / Zaka

    • Chala / Zala

    • Chigoli / Zigoli

Note: Pali mayina ena m’gululi omwe sachulukitsidwa.

  • Zitsanzo: chimanga, chajira, Chichewa, Chitonga, Chifalansa, changu, chisoni, chikondi

f. Li-, Ma-

  • Chimodzi / Zambiri

    • Dalitso / Madalitso

    • Dimba / Madimba

    • Lamba / Malamba

    • Khasu / Makasu

    • Khola / Makola

    • Khonde / Makonde

    • Khumbi / Makumbi

Note: Mayina otsatirawa, mgululi, sachulukitsidwa: mawu, malovu, malonda, mamba, malungo, mafuta, madzi, mafinya

g. Ka-, Ti-

  • Chimodzi / Zambiri

    • Kabanga / Timawanga

    • Kamwana / Tiwana

    • Kamphunzitsi / Tiaphunzitsi

    • Kamunda / Timinda

    • Kamwendo / Timiyendo

    • Kakhutu / Timakutu

    • Kamkwaso / Timikwaso

    • Kanyumba / Tinyumba

    • Kamwala / Timiyala

h. Ku-, malo; Pa-, malo; mu-, malo

  • Chimodzi / Zambiri

    • Kumudzi / Pamudzi / M’mudzi

    • Kunyumba / Panyumba / M’nyumba

    • Kutsinde / Patsinde / M’tsinde

    • Kumbuyo / Pambuyo / M’mbuyo

    • Kuseri / Paseri / M’seri

    • Kudzala / Padzala / M’dzala

Kumbutso

Mayina amayikidwa m’magulu potsata njira ziwiri:

  1. Kuyang’ana aphatikira m’mbuyo osonyeza chinthu chimodzi ndi zinthu zambiri

    • Zitsanzo: una…………………mauna (U-, Ma-)

    • Chipika……………..zipika (Chi-, Zi-)

  2. Kugwiritsa ntchito agwirizanitsi osonyeza chinthu chimodzi ndi zinthu zambiri

    • Zitsanzo: Nyumba iyi………………..nyumba izi (I-, Zi-)

    • Kamunthu aka…………….tianthu iti (Ka-, Ti-)

 

KAPANGIDWE KA MAYINA

a. Kuchokera ku Aneni

i. Kuyika mphatikiram’mbuyo ku tsinde lamneni

  • Zitsanzo:

    • Mphatikiram’mbuyo | mneni | dzina

    • Chi- | Yenda | Chiyenda

    • Chi- | Kumba | Chikumba

    • m- | Londa | Mlonda

    • m- | Phika | Mphika

    • m- | Busa | Mbusa

    • ma- | Lemba | Malemba

    • ma- | Taya | Mataya

    • chi- | lasa | Chilasa

ii. Kuchotsa lembo lotsiriza lamneni la “a” ndikuyikapo “o”

  • Zitsanzo:

    • mneni | dzina

    • Lemba | Lembo

    • Yankha | Yankho

    • Phunzira | Phunziro

    • Funsa | Funso

    • Langiza | Langizo

    • Lamula | Lamulo

    • Tsogola | Tsogolo

iii. Kuyika mphatikiram’mbuyo kumneni komanso kuchotsa lembo lotsiriza lamneni la “a” ndikuyikapo “o”, “i” kapena “e”

  • Zitsanzo:

    • Mphatikiram’mbuyo | mneni | dzina

    • m- | Phunzitsa | Mphunzitsi

    • ma- | Phunzira | Maphunziro

    • chi- | Weruza | Chiweruzo

    • ma- | Yankha | Mayankho

    • chi- | Khulupirira | Chikhulupiriro

    • m- | Lemba | Mlembi

    • chi- | Pera | Chipere

    • chi- | Kwereta | Chikwerete

    • m- | Sodza | Msodzi

    • u- | langiza | Ulangizi

iv. Kusinthiratu mneni

  • Zitsanzo:

    • Tsinde lamneni | Mayina osiyanasiyana opangidwa

    • Yenda

    • -gwa kodza | Ulendo, mlendo, mwendo, chilendo

    • Gwero, chigwa, mgwetsa

    • Likodzo, nkhodzo, mkodzo, chikhodzodzo

v. Kuphatikiza mneni ndi muonjezi

  • Zitsanzo:

    • Mphatikiram’mbuyo | mneni | muonjezi | dzina

    • Ka- | Chi- | Chi- | Ka-

    • Ka- | Chi- | |

    • -lima | Ponda | Gona | Lima

    • -da | yenda | |

    • Padzala | M’thengo | M’bwalo | M’chinena | Msana usiku

    • Kalimapadzala | Chipondam’thengo | Chigonam’bwalo | Kalimam’chinena | Kadamsana chiyendausiku

vi. Kuphatikiza mneni ndi dzina

  • Zitsanzo:

    • Mphatikiram’mbuyo | mneni | dzina | dzina

    • Chi- | Chi- | Ka- | Chi- | Chi-

    • Womba

    • -dya | Liza

    • -dya | lima

    • Nkhanga | Makanda | Mbeta | Onga mpunga

    • Chiombankhanga | Chidyamakanda | Kalizambeta | Chidyaonga | Chilimampunga

vii. Kuphatikiza mneni ndi mlowam’malo

  • Zitsanzo:

    • mneni | Mlowam’malo | dzina

    • Kwata |

    • Ine |

    • Kwataine |

    • Konda | Ine | Kondaine

    • Simba | Zako | Simbazako

    • leka | zawo | Lekazawo

b. Kuchokera ku Mayina: Kuyika Mphatikiram’mbuyo ku Mayina

i. Zitsanzo:

  • Mphatikiram’mbuyo | dzina | dzina

    • Ka- | Litsiro | Kalitsiro

    • Na- | Banda | Nabanda

    • u- | Kalaliki | Ukalaliki

    • ka- | Manu | Kamanu

    • u- | Chitsiru | Uchitsiru

    • u- | namwino | Unamwino

ii. Kuphatikiza dzina ndi dzina

  • Zitsanzo:

    • dzina | dzina | dzina

    • Njoka | Luzi | Njokaluzi

    • Mwana | Bere | Mwanabere

    • Mwana | Mphepo | Mwanamphepo

    • Mkanda | nkhuku | Mkandankhuku

c. Kuchokera ku Masinde Amawu Osiyanasiyana

i. Kuyika mphatikiram’mbuyo ku masinde amayina

  • Zitsanzo:

    • Mphatikiram’mbuyo | tsinde | dzina

    • Zi- | -nthu | Zinthu

    • Mu- | -nthu | Munthu

    • m- | -tengo | Mtengo

    • chi- | -nthu | Chinthu

    • chi- | -nyamata | Chinyamata

    • a- | -nyamata | Anyamata

ii. Kuyika mphatikiram’mbuyo kutsinde lamfotokozi

  • Zitsanzo:

    • Mphatikiram’mbuyo | tsinde | dzina

    • Chi- | -wisi | Chiwisi

    • u- | -tali | Utali

    • chi- | -kulu | Chikulu

    • u- | -kulu | Ukulu

    • m- | -kazi | Mkazi

    • li- | -tali | Litali

iii. Kuyika mphatikiram’mbuyo kumasinde a mawerengo

  • Zitsanzo:

    • Mphatikiram’mbuyo | tsinde | dzina

    • Chi- | U- |

    • u- | -wiri |

    • -tatu |

    • -modzi | Chiwiri | Utatu | Umodzi

d. Kuchokera ku Aonjezi: Kuyika Mphatikiram’mbuyo ku Aonjezi

  • Zitsanzo:

    • Mphatikiram’mbuyo | muonjezi | dzina

    • u- |

    • u- |

    • u- |

    • -bwino | -kale | -chabe | Ubwino | Ukale | uchabe

MAYINA OBWEREKERA

a. Mushe (Chiwemba)

  • Mphatikiram’mbuyo: Mu- (kuwonjezera mmeneyi)

  • Dzina: Muthera (kuwonjezera Muthera wa Mushe)

b. Zakhali (Chisutu)

  • Mphatikiram’mbuyo: Za- (kuwonjezera mmeneyi)

  • Dzina: Zakhali (kuwonjezera Zakhali wa Zakhali)

c. Sabata, aleluya, ame (Chiheberi)

  • Mphatikiram’mbuyo: Sa- (kuwonjezera mmeneyi)

  • Dzina: Sabatasa (kuwonjezera Sabata wa Sabata)

d. Kavalo, malinyero, dona, kapitawo, zenera, nsapato, mbatata, fodya, bulu (Chipwitikizi)

  • Mphatikiram’mbuyo: Ka- (kuwonjezera mmeneyi)

  • Dzina: Kavalokapita (kuwonjezera Kavalo wa Kavalo)

e. Chipewa, boo (Chifalansa)

  • Mphatikiram’mbuyo: Chi- (kuwonjezera mmeneyi)

  • Dzina: Chipanji (kuwonjezera Chipewa wa Chipewa)

f. Malume, zaithwa, zimatha, mkosi (Chingoni)

  • Mphatikiram’mbuyo: Ma- (kuwonjezera mmeneyi)

  • Dzina: Malumikosi (kuwonjezera Malume wa Malume)

g. Sofa, sadaka (Chiluya/Chiarabu)

  • Mphatikiram’mbuyo: So- (kuwonjezera mmeneyi)

  • Dzina: Sofadaka (kuwonjezera Sofa wa Sofa)

h. Boma, mmwenye, bwana, ndege, shula (Chiswahili)

  • Mphatikiram’mbuyo: Bo- (kuwonjezera mmeneyi)

  • Dzina: Bomwenye (kuwonjezera Boma wa Boma)

i. Gomo, chingwa, malasha, dondo, muti, ambwana, bota (Chishona)

  • Mphatikiram’mbuyo: Go- (kuwonjezera mmeneyi)

  • Dzina: Gomwandu (kuwonjezera Gomo wa Gomo)

j. Kalilore, mjomba, mlingo, kakasi (Chiyawo)

  • Mphatikiram’mbuyo: Ka- (kuwonjezera mmeneyi)

  • Dzina: Kalilorkakasi (kuwonjezera Kalilore wa Kalilore)

Chidule:

  • Mayina obwerekera ali ndi mphatikiram’mbuyo okhala ndi mawu a mmeneyi.

  • Mphatikiram’mbuyo zimaonjezera ndi kuonjezera mzimu kapena kudzikumbutsa.

error: Content is protected !!
Scroll to Top