MSCE Chichewa Galamala Form 3 and 4

MALAMULO ACHIYANKHULO MITUNDU YAMAWU M’CHICHEWA

M’chichewa, pali mitundu isanu ndi inayi yamawu, yomwe ndi:

  1. Mayina

  2. Alowam’malo

  3. Afotokozi

  4. Aonjezi

  5. Aneni

  6. Aperekezi

  7. Alumikizi

  8. Mifuwu

  9. Mvekero

MITUNDU INA YAMAWU M’CHICHEWA

  1. a) A phatikizo limodzi
    Zitsanzo: ndi, za, kwa, pa, cha, la, mwa, wa, ku, mu

  2. b) A maphatikizo awiri
    Zitsanzo: munthu, bala, mwala, ntchito, gwira, komba, pita

  3. c) A maphatikizo atatu
    Zitsanzo: lalata, wakunda, chinangwa, monyada, ngakhale

  4. d) A maphatikizo anayi kapena kupitirira apo
    Zitsanzo: khululuka, mpulumutsi, malimidwe, bongololo, muyang’anadzuwa, chilimampunga, chigwirizano

NTCHITO ZA MAWU APHATIKIZO LIMODZI

  1. a) Kukhala aperekezi
    Zitsanzo: Amayi apita ndi atate. Adadya phala la mwana. Tikupita ku Masasa.

  2. b) Kukhala aneni
    Zitsanzo: Kapoloma ndi mphunzitsi. Akoma Akagonera si bukhu lovuta.

  3. c) Kukhala alumikizi
    Zitsanzo: Mukagule masache ndi makungwa.

  4. d) Kukhala mvekero
    Zitsanzo: Tikufuna kansima ka ndi. Adali mbu. Chitsulo chidali psu pamoto.

MAGWERO A MAWU

M’Chichewa, magwero aakulu amawu ndi tsinde ndi muzu. Tsinde ndi gawo lamawu lomwe silisintha, ndipo ili ndi phata lomwe timatha kupangira mawu. Kusiyana kwa tsinde ndi muzu ndi uku:

  1. a) Tsinde limamalizira ndi lembo laliwu, ndipo limatchulika palokha.
    Zitsanzo: -nthu, -dya, -pita, -fa

  2. b) Muzu umamalizira ndi lembo lopanda liwu, ndipo sumatchulika pawokha makamaka chifukwa cha mathero ake.
    Zitsanzo: -nth, -dy, -mw ndi bwer

MITUNDU YA MASINDE

  1. Tsinde la dzina: Limathandiza popanga mayina.
    Zitsanzo: anthu, munthu, chinthu

  2. Tsinde lamfotokozi: Timaligwiritsa ntchito popangira afotokozi ndi mawu ena.
    Zitsanzo: -tali, -fupi, -kulu, -ng’ono, -muna, -kazi, -wisi

  3. Tsinde lamneni: Timapanga nalo aneni osiyanasiyana.
    Zitsanzo: wadya, tadya, akutola, mutola, kumwa, timwa, walemera, tilemera

  4. Tsinde lolozera: Timapangira alozi (mawu olozera).
    Zitsanzo: uja, kaja, zija, ilo, icho, aka, ako, uyu

  5. Tsinde lofunsira: Timaligwiritsa ntchito popanga mawu ofunsira.
    Zitsanzo: otani, zotani, anji, yanji, zayani, kayani, tingati, zingati

  6. Tsinde losonyeza kuchuluka kwa zinthu:
    Zitsanzo: ambiri, zambiri, zingapo, angapo, zingapo, ochepa, zochepa

  7. Tsinde laumwini: Timapangira mawu osonyeza umwini.
    Zitsanzo: anga, panga, kwathu, zathu, pawo, chawo, tanu, kanu, wake, zake

  8. Tsinde losonyeza malo: Timaligwiritsa ntchito popanga mawu osonyeza malo.
    Zitsanzo: kuno, pano, muno, paseri, kuseri, mseri, kunsi, pansi, m’munsi

  9. Tsinde lamgwirizano:
    Zitsanzo: amene, kumene, pamene, komwe, yemwe, zomwe

Mawu m’Chichewa amapangidwa pophatikiza aphatikiram’mbuyo ndi masinde komanso maphatikizo molondola.

MAPHATIKIZO

Phatikizo ndi gawo lamawu lomwe limapangidwa pophatikiza zilembo zaliwu ndi zopanda liwu. Phatikizo timalitchula kamodzi ndi kamodzi.
Zitsanzo: ba, ka, kwa, nkhwa, mphwe, chu, the, psu, tswa, mwe, nyo.

KUMBUTSO: Zilembo za liwu zimayima pazokha ngati phatikizo.
Zitsanzo: a, e, i, o ndi u

MITUNDU YA MAPHATIKIZO

  1. a) A lembo laliwu
    Zitsanzo: ana, ena, ina, ona, una

  2. b) A lembo limodzi lopanda liwu ndi limodzi laliwu
    Zitsanzo: longa, to, sa, menya, te, ma, ka, li, pa, la, manga

  3. c) A malembo awiri opanda liwu ndi limodzi laliwu
    Zitsanzo: phala, dyera, khasu, pwayi, thawa, bwato

  4. d) A malembo atatu opanda liwu ndi limodzi laliwu
    Zitsanzo: nthawi, nkhanu, tchire, khwerero, phwera

  5. e) A malembo anayi opanda liwu ndi limodzi laliwu
    Zitsanzo: nkhwere, ntchito, nthyamba, mphwayi

MPHATIKIRI

Mphatikiri ili ndi phatikizo limene limayikidwa (limaphatikizidwa) kutsinde la mawu.

MITUNDU YA APHATIKIRI

  1. MPHATIKIRAM’MBUYO: Amakhala / amayikidwa kumbuyo kwa tsinde lamawu.
    Zitsanzo: mu- (munthu), chi- (chinthu)

NTCHITO ZA APHATIKIRAM’MBUYO

  1. a) Kupangira mayina.
    Zitsanzo: u- (Ukapolo), chi- (Chimunthu)

  2. b) Kukulitsa kapena kunyoza
    Zitsanzo: chi- (chinyumba), chi- (chimphunzitsi)

  3. c) Kuchepetsa kapena kunyozetsa
    Zitsanzo: ka- (kamphunzitsi), ka- (kanyumba)

  4. d) Kulamula
    Zitsanzo: u- (Upite msanga), zi- (Zitenge zimenezi)

  5. e) Kutsutsa kapena kukana
    Zitsanzo: si- (sindipita), su- (sudya), sa- (sapita)

  6. f) Kusonyeza malo
    Zitsanzo: ku- (kumudzi), pa- (pamudzi), mu- (muno)

  7. g) Kukhala mgwirizanitsi wamwininkhani
    Zitsanzo: Aphunzitsi abweretsa mabukhu asanu.
    Chiswamphika chapana kangaude.

  8. h) Kuchulukitsa
    Zitsanzo: anthu, mitengo, zingwe, minda, matabwa

  9. i) Kusonyeza nthawi za aneni
    Zitsanzo: -ku- (akupita), -dza- (adzapita), -zidza- (ndizidzakudyetsa), -nka- (tinkamuuza)

  10. j) Kulamula
    Zitsanzo: -zi- (kazipita, kwada), -zi- (uzidya mwachangu)

  11. k) Kusonyeza kuti ntchito yachitika popanda chifukwa
    Zitsanzo: -ngo- (wangobwera sadayitanidwe), (angolira)

  12. l) Kusonyeza kuti ntchito ichitika ina ikakwaniritsidwa
    Zitsanzo: -ka- (Ndidzakondwa ukandivomera), -ta- (Ndingapite utandiuza)

  13. m) Kusonyeza kutheka kwa ntchito
    Zitsanzo: -ka- (kanakhozolo), -ku- (kwathu), -zi- (zomwezo), -pa- (panthawiyi)

  14. n) Kusonyeza kuzama
    Zitsanzo: -ndu- (pofika), -muna- (pokhuzanamo)

 

MPHATIKIRAMTSOGOLO

Amalembedwa kutsogolo kwa tsinde lamawu

  • Zitsanzo: -li, -nso, -di, -ku, -yu, -ti, -nji, -ka, -wa, -wo, -wu

NTCHITO ZA APHATIKIRAMTSOGOLO

  1. a) Kuloza

  • Zitsanzo: -chi(chimangachi)-yu (mwanayu), -li (phalali)

  1. b) Kufunsa

  • Zitsanzo: -nji (Mwatenganji lero?), (Kodi kulinji kunjako?)

  1. c) Kusonyeza malo

  • Zitsanzo: -ku (Kusukuluku kuli uve.), -mu (M’chitinimu muli kudya.)

  1. d) Kusonyeza chipangizo chomwe chagwiritsidwa ntchito

  • Zitsanzo: -ira (Aphikira mthikowu.), -era (Agendera mwala wolimba.)

  1. e) Kupangira misintho ya aneni / Kusinthira aneni

  • Zitsanzo: -ula (matula), -idwa (matidwa), -itsa (matitsa), -ana (matana)

  1. f) Kusonyeza kuphatikiza chinthu

  • Zitsanzo: -nso (Kapitonso wasewera kwambiri.), (Iwenso undisamale.)

  1. g) Kusonyeza kubwereza ntchito

  • Zitsanzo: -nso (Abwenzi adyanso lero.), -nso (Mukabenso mabuku.)

  1. h) Kuchenjeza

  • Zitsanzo: -tu (Akubweratu Matakoakanapansi), (Kulitu Edzi kunja kuno.)

  1. i) Kusonyeza kuchitiratu ntchito ina isanachitike

  • Zitsanzo: -tu (Mulimiretu mvula isanagwe.), (Anayankhuliratu tisanadye.)

  1. j) Kusonyeza kuchita ntchito kwathunthu

  • Zitsanzo: -tu (Wadyeratu ndi kwamawa komwe), (Utengeretu ndithu katunduyu.)

  1. k) Kusonyeza kuchita ntchito mopitirira muyeso

  • Zitsanzo: -tu (Aledzeleratu sangayankhulenso.), (Wagoneratu sangadzukenso.)

  1. l) Kutsimikiza kuchitika kwa ntchito

  • Zitsanzo: -di (Ife tachimwadi), (Kodi unapitadi kuchipatala?)

  1. m) Kusonyeza kupitirira kwa ntchito

  • Zitsanzo: -be (Akulirabe), (Tikusambabe.)

  1. n) Kusonyeza kuti ntchito ichitika mtsogolo

  • Zitsanzo: -be (Tibwerabe tikadya.), (Ndigonabe ndikamaliza kuwerenga.)

  1. o) Kusonyeza kukakamira kuchita ntchito

  • Zitsanzo: -be (Ngakhale ndife ndidyabe nsimayi), (Ndikwatirabe Malitayu ngakhale ndi chindalandala.)

  1. p) Kuchulukitsa kapena kulemekeza

  • Zitsanzo: -ni (Gonani apa, agogo), (Khalani pansi ana nonsenu.)

error: Content is protected !!
Scroll to Top