MSCE Chichewa Galamala Form 3 and 4

MLOWAM’MALO

Mlowam’malo ndi mawu amene amagwira ntchito m’malo mwa dzina. Awa ndi mitundu ya mlowam’malo ndi zitsanzo zake:

A. Wadzina lakelake

Wam’mawa ukugwira ntchito m’malo mwa dzina la munthu, ndipo alipo wamitundu itatu:

  1. Wakalozamwini

    • Amalowa m’malo mwa dzina la munthu yemwe akuyankhulayo.

    • Zitsanzo:

      • Ine ndikwatira mwana wa a Phiri.

      • Ife sitikufuna kudya masambawo.

  2. Wakalozamzako

    • Amaloza mzako amene ukumuona panthawi yoyankhulayo.

    • Zitsanzo:

      • Akufuna iwe mtsikanayu.

      • Inu mulibe chilungamo.

  3. Wakalozawina

    • Amaloza munthu amene panthawi yoyankhulayo palibe.

    • Zitsanzo:

      • Iye anali mphunzitsi wathu.

      • Iwo ankapita kutheba.

B. Woloza

  • Amathandiza poloza, amagwiritsa ntchito masinde oloza.

  • Zitsanzo:

    • Uyu ndi mnzanga.

    • Adamupha ndi ichi.

C. Wofunsa

  • Amathandiza pofunsa, amagwiritsa ntchito masinde ofunsira.

  • Zitsanzo:

    • Zingati mwazionazo?

    • Wotani wabera mayeso?

D. Wamgwirizano

  • Amagwiritsa ntchito masinde amgwirizano monga -tere, -mene, ndi -mwe.

  • Zitsanzo:

    • Zotere zimayambitsa chinyengo.

    • Amene wabwera adye.

E. Wogawa

  • Amagwiritsa ntchito masinde ogawa monga –li ndi –nse.

  • Zitsanzo:

    • Aliyense wadwala.

    • Tidya chilichonse.

F. Waumwini

  • Amasonyeza umwini, amagwiritsa ntchito masinde aumwini.

  • Zitsanzo:

    • Zako zili m’khola lino.

    • Wathu siwochita naye masewera.

G. Wowerenga

  • Amathandiza kusonyeza chiwerengero cha zinthu, amagwiritsa ntchito masinde owerengera.

  • Zitsanzo:

    • Mutipatse zisanu zokha.

    • Adatitengera zitatu.

H. Wopatula

  • Amasonyeza kuti zinthu zikupatulidwa kuchokera pazinzake.

  • Zitsanzo:

    • Ochepa apita ku Zambo.

    • Ena athawa.

I. Wotsimikiza/Otsindika

  • Amatsindika kapena kutsimikiza.

  • Zitsanzo:

    • Iye yemwe adandipereka kwa adani anga.

    • Inu nomwe mwatentha nyumba.

J. Wodzichitira

  • Amasonyeza kuti ntchito yabwerera kwa yemwe amayichita.

  • Zitsanzo:

    • Wadzikola wekha.

    • Adadzibaya yekha.

NTCHITO ZA ALOWAM’MALO

A. Kukhala mwininkhani

  • Apa ndi pamene mlowam’malo amachita ntchito m’chiganizo.

  • Zitsanzo:

    • Zitatu zadya mfutso wathu.

    • Wanu wapha mbuzi.

B. Kukhala pamtherankhani

  1. Wachindunji

    • Amachitidwa ntchito m’chiganizo.

    • Zitsanzo:

      • Alinafe waba chochepa.

      • Mbalangwe wapha zonse.

  2. Wopanda chindunji

    • Amachitiridwa ntchito m’chiganizo.

    • Zitsanzo:

      • Kachitsa wagulira awirife mtedza.

      • Gamaliyele wachapira ife zovala.

  3. Wamperekezi

    • Amatsana ndi mperekeziyo.

    • Zitsanzo:

      • Amauluka pa aka.

      • Adabwera ndi zinayi.

C. Kuyitanira

  • Zitsanzo:

    • Inu, thawani moto.

    • Tenga njingayi, iwe.

D. Kukhala mtsirizitsi

  • Amatsirizitsa ganizo la aneni odalira monga –li, si, komanso ndi.

  • Zitsanzo:

    • Chapha nkhuku ndi ichi.

    • Amadwala adali wathu. Makokoto si iwe.

Chidule

  • Mlowam’malo umagwira ntchito m’malo mwa dzina, kugwira ntchito zosiyanasiyana monga kulankhulana, kupempha, ndikuwonetsa umwini.

error: Content is protected !!
Scroll to Top