MSCE Chichewa Galamala Form 3 and 4

ZIGANIZO

Chiganizo ndi gulu lamawu lokhala ndi mneni ndipo limapereka ganizo lomveka bwino.

Zitsanzo:

  • Ali kulandira mankhwala otalikitsa moyo.
  • Timakhala ku Blantyre.

MITUNDU YA ZIGANIZO

  1. Chiganizo chopanda nthambi: Chimakhala ndi mneni m’modzi ndiponso chimakhala ndi ganizo limodzi.
  • Zitsanzo: Timadya bwino.
  1. Chiganizo chanthambi: Chimakhala ndi nthambi yoyima payokha komanso ina yosaima payokha.
  • Zitsanzo: Ndizoona kuti ndili ndi pakati.
  1. Chiganizo chaziganizo: Chimakhala ndi ziganizo zopanda nthambi zingapo zomwe zimalumikizidwa ndi mlumikizi m’modzi.
  • Zitsanzo: Adasewera, adavina komanso adachitako ndewu.
  1. Chiganizo chaziganizo zanthambi: Chimapangidwa ndi ziganizo zanthambi zingapo.
  • Zitsanzo: Tagwirizana kuti tikwatirane ngakhale tilibe podalira.

NTHAMBI ZA CHIGANIZO

Nthambi ndi gulu la mawu lomwe limakhala ndi mneni wakewake.

Zitsanzo:

  • Popeza ukuchita mwano.
  • Tipitako madzulo.

MITUNDU YA NTHAMBI ZACHIGANIZO

  1. Nthambi yoima payokha: Imapereka ganizo lomveka bwino.
  • Zitsanzo: Tipitako madzulo.
  1. Nthambi yosaima payokha: Simapereka ganizo lomveka ndipo imadalira nthambi yoima payokha.
  • Zitsanzo: Popeza ukuchita mwano pamene tinali kudya.

MITUNDU YA NTHAMBI YOSAIMA PAYOKHA

  1. Yadzina: Imagwira ntchito ngati dzina motere:
  • Zitsanzo: Zakuti wapita sindidamve.
  1. Yamfotokozi: Imakamba zambiri zadzina lomwe lili munthambi yoyima payokha.
  • Zitsanzo: Chuma chimene wabacho ufa nacho.
  1. Yamuonjezi: Imagwira ntchito ngati muonjezi ndipo ili ndi mitundu yotsatirayi:
  • Wanthawi: Imasonyeza nthawi yomwe ntchito yachitika.
  • Wamalo: Imaonetsa malo amenentchito ikuchitikira.
  • Wamchitidwe: Imakamba zamchitidwe wa momwe ntchito yachitikira.
  • Wachifukwa: Imasonyeza chifukwa chomwe ntchito yamneni wa munthambi yoima payokha yachitikira.
  • Wacholinga: Imasonyeza cholinga chomwe ntchito yamneni wa munthambi yoyima payokha idachitikira.
  • Wolabadira: Imasonyeza kulabadira.
  • Wapokhapokha: Imasonyeza kuti ntchito ichitika inzake ikakwaniritsidwa.
  • Wazotsatira: Imasonyeza zotsatira za ntchito yamneni wamunthambi yoyima payokha.

 

error: Content is protected !!
Scroll to Top