Atengambali: Mayi ake a Nthondo, azimayi a m’mudzi, atsibweni ake a Nthondo, mlongo wake wa Nthondo, ndi ena ambiri.
Malo: Kumudzi kwawo kwa mayi ake a Nthondo
NKHANI YA M’MUTUWU MWACHIDULE
- Nthondo adabadwa nthawi yozizira usiku.
- Nthondo adali mwana yekhayo wamwamuna pomwe ena onse anali aakazi.
- Anthu a m’mudziwo adapita kukayamikira kubadwa kwa mwana.
- Nthondo anali mwana amene anayembekezeka kutsatira makolo ake polowa bulangete akakula.
- Bambo ake a Nthondo anali atatengedwa ndi asilikali pamene iye anabadwa.
- Uthenga wa kubadwa kwa Nthondo unatumizidwa kwa bambo ake a Nthondo.
- A kwawo kwa bambo ake a Nthondo adalandira uthenga ndi chimwemwe chachikulu.
- Amayi ake a bambo ake a Nthondo adakonzekera ulendo wokawona Nthondo.
- Anthu a kwawo kwa bambo ake adayamikira kukongola kwa Nthondo ndipo adadziwitsidwa za kutengedwa kwa bambo ake ndi asilikali.
- A kwawo kwa bambo ake a Nthondo adakhala kwa mayi ake a Nthondo kwa kanthawi.
MFUNDO ZIKULUZIKULU ZA M’MUTUWU
- Chisangalaro
- Anthu a kumudzi kwa Nthondo adasangalala ndi kubadwa kwake.
- A kwawo kwa bambo ake a Nthondo nawonso adakondwera ndi uthenga wa kubadwa kwa Nthondo.
- Miyambo
- Bambo ake a Nthondo ankakhala chikamwini.
- A kwawo kwa mayi ake a Nthondo adalengeza za kubadwa kwa Nthondo kwa akuchimuna.
- Kuthandizana
- Anthu am’mudziwo adathandizana powafunira madzi mayi ake a Nthondo, popeza anali akadadwala.
MAPHUNZIRO AM’MUTUWU
- Ndibwino kuyamikira zinthu zabwino.
- Ndibwino kuthandiza anzathu pamene ali m’mavuto.