MSCE Chichewa Galamala Form 3 and 4

AGWIRIZANITSI

Mgwirizanitsi: Phatikizo limene limasonyeza mgwirizano pakati pa dzina kapena mlowam’amalo ndi mawu ena m’chiganizo.
Chitsanzo: Malani wataya mchere wathu.

MITUNDU YA AGWIRIZANITSI

  1. Wamwininkhani:

    • : Mphatikiram’mbuyo wamneni yemwe amasonyeza mgwirizano pakati pa yemwe wachita ntchito (mwininkhani) ndi mneniyo.

    • Zitsanzo:

      • Ntchentche zimafalitsa matenda akamwazi.

      • Agalu amawuwa zedi usiku.

  2. Wapamtherankhani:

    • : Mphatikiramkati wamneni yemwe amasonyeza mgwirizano pakati pa yemwe akuchitidwa/akuchitiridwa ntchito (pamtherankhani) ndi mneniyo m’chiganizo.

    • Zitsanzo:

      • Amayi adatifunsa mafunso ovuta zedi.

      • Tawona amandikonda ndithu.

    • Kumbutso: Mgwirizanitsiyu amatha kukhala mphatikiram’mbuyo ngati mneni ali m’kachitidwe kawochitidwa.

    • Chitsanzo: Mitengo yadulidwa ndi Akimu.

  3. Waumwini:

    • : Mphatikiram’mbuyo kutsinde la umwini yemwe amaonetsa mgwirizano pakati pa dzina ndi mawu amene akusonyeza umwini wachinthu chomwe chikutchulidwa ndi dzinalo.

    • Zitsanzo:

      • Mwana wanu wavuula nyama yathu.

      • Chovala chanu chilibe lamba.

  4. Wowerengera:

    • : Mphatikiram’mbuyo kutsinde lowerengera yemwe amagwirizanitsa mawu owerengerawo ndi dzina lomwe likutchula zinthu zomwe zikuwerengedwazo.

    • Zitsanzo:

      • Ana atatu athawa sabata yatha.

      • Mundipatseko mphangala ziwiri.

  5. Woloza:

    • : Mphatikiram’mbuyo kutsinde loloza amene amasonyeza ubale pakati pa mawu olozawo ndi dzina la chinthu chomwe chikulozedwa m’chiganizomo.

    • Zitsanzo:

      • Mtsikana uyu ndi chilandamoyo.

      • Kamwana aka kamandisautsa.

      • Mutiphere nkhuku iyo.

  6. Waubale / wamgwirizano:

    • : Mphatikiram’mbuyo kutsinde lamgwirizano/ubale ndipo amadalira gulu ladzina pofuna kugwirizana ndi dzinalo.

    • Zitsanzo:

      • Mandala ndiye asankhe zipokolo zomwe ndikuzifuna.

      • Sukulu imene ndidaphunzira ndi yabwino.

  7. Wamfotokozi:

    • : Uyu ndi mphatikiram’mbuyo ku tsinde la mfotokozi ndi mawu ena, timapangira afotokozi kuchokera kumasinde a afotokozi ndi mawu ena ndipo amagwirizanitsa mfotokozi ndi dzina lomwe akulikamba.

    • Zitsanzo:

      • Usavale buluku lofiira.

      • Ndikwatira mkazi wokuda.

      • Watenga choko chachifupi.

  8. Wodzichitira:

    •  Mphatikiramkati wamneni yemwe amasonyeza kuti ntchito yabwerera kwa yemwe akuyichita.

    • Zitsanzo:

      • Zuze wadziphunzitsa.

      • Kazimire adadzikhapa.

MAFUNSO

  1. Kodi agwirizanitsi angagwiritsidwe ntchito bwanji mu masinda?

  2. Chimodzi mwa zitsanzo zomwe mungapereke pa wamwininkhani?

  3. Ndi mawu otani amene angagwirizane pa wapamtherankhani?

  4. Ndi mtundu wotani wa agwirizanitsi umene umakhalapo mu mawu owerengera?

  5. Kodi zimenezi zimathandiza bwanji mukamalankhula?

error: Content is protected !!
Scroll to Top