ANENI
-
Aneni ndi mawu amene amakamba za ntchito yochitika m’chiganizo komanso momwe chinthu chilili.
-
Aneni ena amaonetsa ntchito pamene ena saonetsa ntchito.
Zitsanzo:
-
(a) Dalitso wakumba dzenje lalitali. (mneni woonetsa ntchito)
-
(b) Mkango ndi chilombo cholusa. (mneni wosaonetsa ntchito)
MITUNDU YA ANENI
a. Woyambukira:
-
Amasonyeza yemwe wagwira ntchito komanso yemwe wachitidwa ntchito.
-
Aneniwa amanyamula zochitika kuchokera kwa mwininkhani kupita ku pamtherankhani.
-
Zitsanzo:
-
Kamba adapha bakha.
-
Amayi adya malalanje athu.
-
b. Wosayambukira:
-
Aneniwa sakhala ndi pamtherankhani, kotero kuti ntchito yake siyioneka kuti yachitika pa chinthu chilichonse.
-
Zitsanzo:
-
Fumulani wagwa lero.
-
Galu wafa.
-
c. Wodalira:
-
Amadalira mawu ena kuti apereke ganizo lomveka bwino.
-
Aneniwa alipo amitundu iwiri: amaphatikizo ndi amawu.
-
Zitsanzo:
-
Mandala ndi wabwino. (wamawu)
-
Hana anali ndi mwayi zedi. (“li” waphatikizo)
-
Akuti moni ambuyanu. (“ti” waphatikizo)
-
d. Wothandiza:
-
Amathandizira aneni ena poponga nthawi za aneni zosiyanasiyana.
-
Ntchitoyawo yeniyeni simaoneka, koma yomwe imaoneka ndi ya mneni wothandizidwayo.
-
Zitsanzo:
-
Nabanda wakhala akushashalika kwa zaka zambiri.
-
e. Wosintha nthawi:
-
Amasintha molingana ndi nthawi yakale, yatsopano, ngakhalenso yamtsogolo.
-
Zitsanzo:
-
Dimba adaphika maungu.
-
ANambewe ankaphika kale.
-
Mwana akuphika.
-
Mwayi adzaphika.
-
f. Wosasintha nthawi:
-
Awa sasintha molingana ndi nthawi ndipo amayamba ndi mphatikiram’mbuyo “ku”.
-
Zitsanzo:
-
Amakonda kupemphera.
-
Adazolowera kuyenda usiku.
-
Samatha kuphika.
-
Akufuna kukhala chitsiru.
-
MAGULU A ANENI
a. Mneni watsinde la phatikizo limodzi
-
Zitsanzo:
-
-ba, -psa, -swa, -fa, -mwa, -dya
-
Kagone waba nkhuku yanga.
-
Malinda wapsa ndi moto.
-
b. Mneni watsinde la maphatikizo awiri
-
Zitsanzo:
-
-lowa, -menya, -thyola, -zula
-
Talowa m’nyumba.
-
Adamenya mwana.
-
c. Mneni watsinde la maphatikizo atatu
-
Zitsanzo:
-
-khazika, -lalata, -lamula, -chepetsa
-
Khazikani mphika pamoto.
-
Tipita ndipo tikalalata.
-
d. Mneni wa tsinde la maphatikizo anayi kapena kuposera apo
-
Zitsanzo:
-
-piringiza, -changamutsa, -tsukuluza, -khulupirira
-
Amuchangamutsa anzake.
-
Ndimamukhulupirira Nambewe.
-
NTHAWI ZA ANENI
-
Izi zili ndi khalidwe la mneni poonetsa nthawi yomwe ntchito inachitikira, ikuchitikira, yachitikira ngakhalenso idzachitikira.
-
Nthawi za aneni zimapangidwa pogwiritsa ntchito aphatikiramkati osonyeza nthawi.
-
Zitsanzo:
-
Ankadya, timadya, tidzadya, tikudya.
-
MITUNDU YA NTHAWI ZA ANENI
-
Pali mitundu ikuluikulu itatu ya nthawi za aneni: nthawi yakale, yatsopano ndi yamtsogolo.
1. Nthawi yakale:
-
Yawamba:
-
Imakamba zinthu zomwe zinachitika ndipo zidatha.
-
Zitsanzo:
-
Ndidayamba uphunzitsi zaka zisanu zapitazo.
-
A Ngozo analedzera mowa kwambiri.
-
-
-
Yakawirikawiri:
-
Imasonyeza zinthu zomwe zimachitika kale kawirikawiri.
-
Zitsanzo:
-
Amadya zipokolo akadali ana.
-
Timatukwana tili kusekondale.
-
-
-
Yathayi:
-
Imasonyeza kuti pamene ncthito ina inkatha, ina idayamba kapena kuti pamene ntchito inkachitika inzake inali itatha.
-
Zitsanzo:
-
Ndidali nditakonzeka kale pamene ankanditenga.
-
M’mene ankawatema anali atadya kale.
-
-
-
Yopitirira:
-
Imasonyeza kuti ntchito inkachitika mopitirira kalero.
-
Zitsanzo:
-
Makolo athu ankavala nguwo.
-
Anali kudya usiku.
-
-
Kumbutso:
-
Nthawi yakale yopitirira imagwira ntchito izi:
-
i. kusonyeza chizolowezi komanso chikhulupiriro.
-
Zitsanzo:
-
Makolo ankayenda pangolo.
-
Anthu akale anali kupembedza mizimu.
-
-
-
ii. kusonyeza kuti ntchito inali kupitirira pamene inzake imachitika.
-
Zitsanzo:
-
Mphatso anali kuodzera ife tikupemphera.
-
Gandali ankadya iwo akuphunzira.
-
-
-
-
Yathayi yopitirira:
-
Imasonyeza kuti ntchito inkachitika m’mbuyomo mopitirira kufikira nthawi ina yake.
-
Zitsanzo:
-
Tidakhala tikudya mtoliro kwa sabata yathunthu.
-
Adakhala akutipondereza kwa zaka zisanu.
-
-
2. Nthawi yatsopano:
-
Imasonyeza zinthu zimene zikuchitika kapena zangochitika kumene.
-
Yawamba:
-
Imagwiritsa ntchito mphatikiramkati “-ma-”.
-
Zitsanzo:
-
Timadya zipokolo.
-
Angoni samasankha ndiwo.
-
-
-
Nthawi yatsopano yawamba imagwira ntchito zotsatirazi:
-
i. kusonyeza chizolowezi.
-
Zitsanzo:
-
Solobala amaseka mopusa.
-
Thokozani amayankhula mokuluwika.
-
-
-
ii. kusonyeza zikhulupiriro.
-
Zitsanzo:
-
Akhirisitu amakhulupirira Yesu.
-
Satana amamwa mwazi.
-
-
-
-
Yathayi:
-
Imasonyeza kuti ntchito yangotha kumene koma zotsatira zake zikadalipo.
-
Zitsanzo:
-
Tamenya nkhondo yabwino.
-
Ndalima ndime yayikulu.
-
-
-
Yopitirira:
-
Imasonyeza kuti ntchito ikuchika mopitirira.
-
Zitsanzo:
-
Ali kusonyeza zomwe akolola.
-
Ife tikusamba.
-
-
-
Yathayi yopitirira:
-
Imasonyeza kupitirira kwa ntchito ndi kutha kwa nthawi yonenedwayo.
-
Zitsanzo:
-
Takhala tikulandira malipiro ochepa kwa zambiri.
-
Wakhala akudwala kwa nthawi yayitali.
-
Anthuwa akhala ali kukupirirani.
-
-
3. Nthawi yamtsogolo:
-
Imakamba za ntchito zomwe zidzachitika mtsogolo.
-
Yawamba:
-
Imagwiritsa ntchito mphatikiramkati “-dza-”.
-
Zitsanzo:
-
Udzadya thukuta lako.
-
Tidzapuma sabata yamawa.
-
-
-
Yathayi:
-
Imaonetsa ntchito yomwe idzachitike mtsogolo itatha.
-
Zitsanzo:
-
Udzakhala utalambula bwaloli pofika pa 23 August 2010.
-
Tidzakhala titayala nkhata pokwirira dzenjelo.
-
-
-
Yopitirira:
-
Aneni ake amasonyeza kuti ntchito izidzachitika mopitirira kutsogolo.
-
Zitsanzo:
-
Nkhondo zidzachitika kwa masabata atatu.
-
Mafilimu adzachitika pa intaneti masiku angapo.
-
-
MAGULU A NTHAWI ZA ANENI
a. Mphatikiridwa
-
Pali mitundu iwiri:
-
Poyamba, akufotokozera mawu otero monga “ali” ndi “kudzalu.”
-
Pothandizidwa ndi mphatikiridwa.
-
b. Zinthu
-
Mofanana ndi mphatikiridwa, zinthu zimagawidwa mu zitsanzo ziwiri:
-
Zinthu zomwe zili ndi mphamvu yotsogolera, monga, “ndidayamba.”
-
Zinthu zopanda mphamvu, monga, “ndidya” yomwe ikukwaniritsidwa kuchokera m’nthawi yapitayi.
-
Zitsanzo Zopeza Aneni:
-
Aneni amasonyeza njira ziwiri kapena zingapo zovuta popanda mawu.
-
Malemba akuzungulira aneni akhala akuchitika ndi anthu asanayambe.
-
Ndiyenera kutchula akale, nthawi ya lero, komanso zinthu zatsopano.
MAFUNSO AKE
-
Kodi aneni anenetsa chiyani?
-
Ndizofunika bwanji kuti aneni akhalebe ndi zotsatira za malinga ndi nthawi?
-
Chifukwa chiyani ndi bwino kusonyeza mawu akale pofuna kutsatira aneni?
ZOFUNA KUYAMBA:
-
Onetsetsani kuti aneni akuchita zinthu zolemera, zambiri, komanso zolondola.
-
Kapenanso bwanji chindapusa chiyamba kukhala chapamwamba chomwe chingathandize kusonyeza aneni a m’mbuyomu?
KACHITIDWE KA ANENI
Ili ndi khalidwe lamneni losonyeza mgwirizano pakati pa mwininkhani, pamtherankhani ndi mneniyo.
MITUNDU YA KACHITIDWE KA ANENI
-
Kachitidwe kawochita: Mwininkhani amayamba chiganizo ndipo chidwi cha woyankhula chimakhala pa yemwe wachita ntchito m’chiganizo.
-
Zitsanzo:
-
Galu wanu waponda chimanga changa.
-
Mbuzi zabudula bonongwe.
-
-
Kachitidwe kawochitidwa: Pamtherankhani amayamba chiganizo kusonyeza kuti ntchito yamuchitikira ndipo chidwi cha woyankhula chimakhala pa yemwe wachitidwa ntchito.
-
Zitsanzo:
-
Chimanga changa chapondedwa ndi galu wanu.
-
Bonongwe wabudulidwa ndi mbuzi.
-
Kachitidwe Kawochitidwa Kali Ndi Mitundu Yake:
-
Kawochitidwa poyera: Aneni ake amathera ndi mphatikiramtsogolo “-idwa-” ndi “-edwa-”
-
Zitsanzo:
-
Ana alasidwa ndi zigawenga.
-
Nkhumba yabedwa dzulo.
-
-
Kawochitidwa m’chibisira: Aneni ake amathera ndi mphatikiramtsogolo “-ika-” komanso “-eka-”
-
Zitsanzo:
-
Nsima yadyeka.
-
Mtolo wamangika bwino.
-
III. Kawochitidwa monyazitsa: Aneni ake amathera ndi mphatikiramtsogolo “-iwa-”, “-ewa-” ndi “-wa-”.
-
Zitsanzo:
-
Galu waphewa.
-
Kamoto watengwa.
-
Ndipsi yamangwa.
-
Joza wapezwa ndi mkazi uja.
-
MISINTHO YA ANENI
Msintho wamneni ndi kusintha komwe kumachitika pamneni pamene tayika mphatikiramtsogolo wosinthira mneniyo.
|
Msintho wamneni |
Mtundu wa msintho wamneni |
Mphatikiramtsogolo |
|
matidwa |
Wochitidwa poyera |
-idwa, -edwa |
|
matika |
Wochitidwa m’chibisira |
-ika, -eka |
|
matiwana |
Wochitidwa monyazitsa |
-iwa, -ewa, -wa |
|
matamata |
Wachibwereza |
– |
|
matula |
Wamtsutso/wotsutsa |
-ula |
|
matana |
Wochitirana |
-ana |
|
mobwezerana |
Womchitira |
– |
|
matira |
||
|
matitsa |
||
|
matitsitsa |
Wochititsa |
-ira, -era |
|
Wokitzitsa |
-itsa, -etsa |
|
|
Wochititsitsa |
-itsitsa, -etsetsa |
KANENEDWE KA ANENI
Iyi ndi ntchito yomwe aneni amagwira m’chiganizo molingana ndi m’mene akumvekera, monga: kufotokoza, kufunsa, kulamula, kusonyeza cholinga ndi zina.
MITUNDU YA KANENEDWE KA ANENI
-
Kofotokoza: Aneni ake amangouza anthu (amangofotokoza) zomwe zachitika kuti adziwe chabe.
-
Zitsanzo:
-
Mvula imagwa yochepa kuchipalamba.
-
Masika sadayende bwino.
-
-
Kofunsa: Kawirikawiri aneni ake amatchulidwa mofunsa koma satsatana ndi mawu ofunsira monga: “kodi”, “bwanji” ndi ena.
-
Zitsanzo:
-
Mwadya kale?
-
KuMalawi mumafunsira amuna?
-
-
Kolamula: Aneni amkanenedweka amapereka lamulo ndipo kanenedweka kalipo kamitundu itatu:
-
Kolamula wamba/mwachindunji: Aneni ake amapangidwa ndi tsinde lamneni kapenanso tsinde ndi mphatikiramtsogolo wolemekeza kapena kuchulukitsa (“-ni”)
-
Zitsanzo:
-
Pita uko.
-
Pitani uko.
-
Yala apa.
-
Yalani apa.
-
-
-
Kolamula mopempha/molangiza:
-
Zitsanzo:
-
Baalemba nthawi siyinathe.
-
Kathamanga sunamalize.
-
-
-
Kolamula mokakamiza: Lamulo limagwa kwa aliyense wonyozera ntchito yomwe wauzidwa. Aneni ake amakhala ndi mphatikiramkati “-zi-”.
-
Zitsanzo:
-
Kazilemba mwachangu.
-
Kazilimani ndingakuthamangitseni.
-
-
-
Kachifuniro: Kamasonyeza kuti zoyankhulazo ndi maganizo a woyankhulayo osati ndi choncho nthawi zonse. Kanenedweka kamasonyeza izi:
-
Kupempha chilolezo (kanenedwe kopempha chilolezo)
-
Zitsanzo:
-
Ndingapite nawo ku Zomba lero?
-
Timati titenge nawo mwanayu.
-
-
-
Kusonyeza mafuno (kanenedwe ka mafuno):
-
Zitsanzo:
-
Muuse mumtendere.
-
Uziona kutali ndi moto.
-
Mulembe bwino mayeso anu.
-
-
-
Kusonyeza kutheka kwa chinthu (kanenedwe kosonyeza kutheka ndi kusatheka kwa ntchito):
-
Zitsanzo:
-
Ndingawuluke patsache.
-
Uyu angapapire bibida.
-
Iwe wekha sungandimenye.
-
Sangasenze mtolo wankhuni.
-
-
-
Kusonyeza cholinga (kanenedwe kacholinga): Aneni ake amasonyeza kuti ntchito yachitika ndi cholinga chake.
-
Zitsanzo:
-
Adavina mosangalatsa kuti alandire mphatso.
-
Tidakhamukira ku malo ogona kuti tikapulumutse mabuku athu.
-
Adamulemba pamsana kuti asadzamuyiwale.
-
-
-
Kapokhapokha: Aneni ake amapereka muyeso wachinachake kuti ufikitsidwe ndipo amasonyeza kuti ntchito ichitika inzake ikakwaniritsidwa. Aneni akakhala ndi mphatikiramkati wapokhapokha “-ka-”.
-
Zitsanzo:
-
Mukasankha Kamanuyu tidzavutika zedi.
-
Mukadafuna mukadalenga galu.
-
Mukadandipempha chilichonse ndikadakupatsani.
-
-
Kazotsatira: Aneni ake amasonyeza kuti ntchito idachitika/idakwanitsidwa motsatiridwa ndi inzake (ntchito itachitika, inzake idatsatira).
-
Zitsanzo:
-
Atawerenga kwambiri adapambana mayeso.
-
Ndidalira kwambiri mwakuti ndidatupa maso.
-
Atamuchotsa sukulu adadzimangirira.
-