APEREKEZI
Awa ndi mawu amene amaperekeza dzina kapena mlowam’malo. Zitsanzo:
- Bwerani kwa ine nonse olemba ndi ovutika.
- Ndagula fanta chifukwa cha iwe.
MAGULU A APEREKEZI
- Mperekezi wamawu amodzi
Zitsanzo:
- Tikupita ku Nsaka.
- Wakhala pa chitsa.
- Ndidzakumenya ndi ichi.
- Mperekezi wamawu awiri
Zitsanzo:
- Mukabisale pansi pa bedi.
- Tidampeza kuseri kwa chigayo.
- Tinkayenda mphepete mwa msewu.
- Wamwalira kamba ka malungo.
NTCHITO ZA APEREKEZI
- Kusonyeza chipangizo/chida
Zitsanzo:
- Adamukwapula ndi tsatsa.
- Ndikugwaza ndi chisongole.
- Adabwera pa galimoto.
- Tinkauluka pa tsache.
- Kusonyeza mbali yomwe chinthu chili (malo)
Zitsanzo:
- Mwana wapita ku Matawale.
- Atate ali pa phiri.
- Akuyenda pakati pa msewu.
- Ndidamuona m’mbali mwa khola.
- Kusonyeza umwini
Zitsanzo:
- Musadye mapapaya a Nagwede.
- Ng’ombe izi ndi za amalume.
- Kusonyeza nthawi
Zitsanzo:
- Tilemba mayeso mkati mwa Juni.
- Kodi udabadwa pakati pa mwezi?
- Ndidzapitako pa chisanu.
- Kusonyeza kuchita ntchito ndi wina kapena chinthu china
Zitsanzo:
- Mukadya ndi alendo.
- Apita ndi atsibweni.
- Ndayenda ndi ndalama.
- Mugule ndi ndalama zanu.
- Kusonyeza chifukwa
Zitsanzo:
- Mwabwera kuno kumudzi chifukwa cha matendawa.
- Mwanayu afa kamba ka uhule.
- Kodi mwagulitsa Malaya chifukwa cha mtsikanayu?