MALAMULO ACHIYANKHULO MITUNDU YAMAWU M’CHICHEWA
M’chichewa, pali mitundu isanu ndi inayi yamawu, yomwe ndi:
-
Mayina
-
Alowam’malo
-
Afotokozi
-
Aonjezi
-
Aneni
-
Aperekezi
-
Alumikizi
-
Mifuwu
-
Mvekero
MITUNDU INA YAMAWU M’CHICHEWA
-
a) A phatikizo limodzi
Zitsanzo: ndi, za, kwa, pa, cha, la, mwa, wa, ku, mu -
b) A maphatikizo awiri
Zitsanzo: munthu, bala, mwala, ntchito, gwira, komba, pita -
c) A maphatikizo atatu
Zitsanzo: lalata, wakunda, chinangwa, monyada, ngakhale -
d) A maphatikizo anayi kapena kupitirira apo
Zitsanzo: khululuka, mpulumutsi, malimidwe, bongololo, muyang’anadzuwa, chilimampunga, chigwirizano
NTCHITO ZA MAWU APHATIKIZO LIMODZI
-
a) Kukhala aperekezi
Zitsanzo: Amayi apita ndi atate. Adadya phala la mwana. Tikupita ku Masasa. -
b) Kukhala aneni
Zitsanzo: Kapoloma ndi mphunzitsi. Akoma Akagonera si bukhu lovuta. -
c) Kukhala alumikizi
Zitsanzo: Mukagule masache ndi makungwa. -
d) Kukhala mvekero
Zitsanzo: Tikufuna kansima ka ndi. Adali mbu. Chitsulo chidali psu pamoto.
MAGWERO A MAWU
M’Chichewa, magwero aakulu amawu ndi tsinde ndi muzu. Tsinde ndi gawo lamawu lomwe silisintha, ndipo ili ndi phata lomwe timatha kupangira mawu. Kusiyana kwa tsinde ndi muzu ndi uku:
-
a) Tsinde limamalizira ndi lembo laliwu, ndipo limatchulika palokha.
Zitsanzo: -nthu, -dya, -pita, -fa -
b) Muzu umamalizira ndi lembo lopanda liwu, ndipo sumatchulika pawokha makamaka chifukwa cha mathero ake.
Zitsanzo: -nth, -dy, -mw ndi bwer
MITUNDU YA MASINDE
-
Tsinde la dzina: Limathandiza popanga mayina.
Zitsanzo: anthu, munthu, chinthu -
Tsinde lamfotokozi: Timaligwiritsa ntchito popangira afotokozi ndi mawu ena.
Zitsanzo: -tali, -fupi, -kulu, -ng’ono, -muna, -kazi, -wisi -
Tsinde lamneni: Timapanga nalo aneni osiyanasiyana.
Zitsanzo: wadya, tadya, akutola, mutola, kumwa, timwa, walemera, tilemera -
Tsinde lolozera: Timapangira alozi (mawu olozera).
Zitsanzo: uja, kaja, zija, ilo, icho, aka, ako, uyu -
Tsinde lofunsira: Timaligwiritsa ntchito popanga mawu ofunsira.
Zitsanzo: otani, zotani, anji, yanji, zayani, kayani, tingati, zingati -
Tsinde losonyeza kuchuluka kwa zinthu:
Zitsanzo: ambiri, zambiri, zingapo, angapo, zingapo, ochepa, zochepa -
Tsinde laumwini: Timapangira mawu osonyeza umwini.
Zitsanzo: anga, panga, kwathu, zathu, pawo, chawo, tanu, kanu, wake, zake -
Tsinde losonyeza malo: Timaligwiritsa ntchito popanga mawu osonyeza malo.
Zitsanzo: kuno, pano, muno, paseri, kuseri, mseri, kunsi, pansi, m’munsi -
Tsinde lamgwirizano:
Zitsanzo: amene, kumene, pamene, komwe, yemwe, zomwe
Mawu m’Chichewa amapangidwa pophatikiza aphatikiram’mbuyo ndi masinde komanso maphatikizo molondola.
MAPHATIKIZO
Phatikizo ndi gawo lamawu lomwe limapangidwa pophatikiza zilembo zaliwu ndi zopanda liwu. Phatikizo timalitchula kamodzi ndi kamodzi.
Zitsanzo: ba, ka, kwa, nkhwa, mphwe, chu, the, psu, tswa, mwe, nyo.
KUMBUTSO: Zilembo za liwu zimayima pazokha ngati phatikizo.
Zitsanzo: a, e, i, o ndi u
MITUNDU YA MAPHATIKIZO
-
a) A lembo laliwu
Zitsanzo: ana, ena, ina, ona, una -
b) A lembo limodzi lopanda liwu ndi limodzi laliwu
Zitsanzo: longa, to, sa, menya, te, ma, ka, li, pa, la, manga -
c) A malembo awiri opanda liwu ndi limodzi laliwu
Zitsanzo: phala, dyera, khasu, pwayi, thawa, bwato -
d) A malembo atatu opanda liwu ndi limodzi laliwu
Zitsanzo: nthawi, nkhanu, tchire, khwerero, phwera -
e) A malembo anayi opanda liwu ndi limodzi laliwu
Zitsanzo: nkhwere, ntchito, nthyamba, mphwayi
MPHATIKIRI
Mphatikiri ili ndi phatikizo limene limayikidwa (limaphatikizidwa) kutsinde la mawu.
MITUNDU YA APHATIKIRI
-
MPHATIKIRAM’MBUYO: Amakhala / amayikidwa kumbuyo kwa tsinde lamawu.
Zitsanzo: mu- (munthu), chi- (chinthu)
NTCHITO ZA APHATIKIRAM’MBUYO
-
a) Kupangira mayina.
Zitsanzo: u- (Ukapolo), chi- (Chimunthu) -
b) Kukulitsa kapena kunyoza
Zitsanzo: chi- (chinyumba), chi- (chimphunzitsi) -
c) Kuchepetsa kapena kunyozetsa
Zitsanzo: ka- (kamphunzitsi), ka- (kanyumba) -
d) Kulamula
Zitsanzo: u- (Upite msanga), zi- (Zitenge zimenezi) -
e) Kutsutsa kapena kukana
Zitsanzo: si- (sindipita), su- (sudya), sa- (sapita) -
f) Kusonyeza malo
Zitsanzo: ku- (kumudzi), pa- (pamudzi), mu- (muno) -
g) Kukhala mgwirizanitsi wamwininkhani
Zitsanzo: Aphunzitsi abweretsa mabukhu asanu.
Chiswamphika chapana kangaude. -
h) Kuchulukitsa
Zitsanzo: anthu, mitengo, zingwe, minda, matabwa -
i) Kusonyeza nthawi za aneni
Zitsanzo: -ku- (akupita), -dza- (adzapita), -zidza- (ndizidzakudyetsa), -nka- (tinkamuuza) -
j) Kulamula
Zitsanzo: -zi- (kazipita, kwada), -zi- (uzidya mwachangu) -
k) Kusonyeza kuti ntchito yachitika popanda chifukwa
Zitsanzo: -ngo- (wangobwera sadayitanidwe), (angolira) -
l) Kusonyeza kuti ntchito ichitika ina ikakwaniritsidwa
Zitsanzo: -ka- (Ndidzakondwa ukandivomera), -ta- (Ndingapite utandiuza) -
m) Kusonyeza kutheka kwa ntchito
Zitsanzo: -ka- (kanakhozolo), -ku- (kwathu), -zi- (zomwezo), -pa- (panthawiyi) -
n) Kusonyeza kuzama
Zitsanzo: -ndu- (pofika), -muna- (pokhuzanamo)
MPHATIKIRAMTSOGOLO
Amalembedwa kutsogolo kwa tsinde lamawu
-
Zitsanzo: -li, -nso, -di, -ku, -yu, -ti, -nji, -ka, -wa, -wo, -wu
NTCHITO ZA APHATIKIRAMTSOGOLO
-
a) Kuloza
-
Zitsanzo: -chi(chimangachi)-yu (mwanayu), -li (phalali)
-
b) Kufunsa
-
Zitsanzo: -nji (Mwatenganji lero?), (Kodi kulinji kunjako?)
-
c) Kusonyeza malo
-
Zitsanzo: -ku (Kusukuluku kuli uve.), -mu (M’chitinimu muli kudya.)
-
d) Kusonyeza chipangizo chomwe chagwiritsidwa ntchito
-
Zitsanzo: -ira (Aphikira mthikowu.), -era (Agendera mwala wolimba.)
-
e) Kupangira misintho ya aneni / Kusinthira aneni
-
Zitsanzo: -ula (matula), -idwa (matidwa), -itsa (matitsa), -ana (matana)
-
f) Kusonyeza kuphatikiza chinthu
-
Zitsanzo: -nso (Kapitonso wasewera kwambiri.), (Iwenso undisamale.)
-
g) Kusonyeza kubwereza ntchito
-
Zitsanzo: -nso (Abwenzi adyanso lero.), -nso (Mukabenso mabuku.)
-
h) Kuchenjeza
-
Zitsanzo: -tu (Akubweratu Matakoakanapansi), (Kulitu Edzi kunja kuno.)
-
i) Kusonyeza kuchitiratu ntchito ina isanachitike
-
Zitsanzo: -tu (Mulimiretu mvula isanagwe.), (Anayankhuliratu tisanadye.)
-
j) Kusonyeza kuchita ntchito kwathunthu
-
Zitsanzo: -tu (Wadyeratu ndi kwamawa komwe), (Utengeretu ndithu katunduyu.)
-
k) Kusonyeza kuchita ntchito mopitirira muyeso
-
Zitsanzo: -tu (Aledzeleratu sangayankhulenso.), (Wagoneratu sangadzukenso.)
-
l) Kutsimikiza kuchitika kwa ntchito
-
Zitsanzo: -di (Ife tachimwadi), (Kodi unapitadi kuchipatala?)
-
m) Kusonyeza kupitirira kwa ntchito
-
Zitsanzo: -be (Akulirabe), (Tikusambabe.)
-
n) Kusonyeza kuti ntchito ichitika mtsogolo
-
Zitsanzo: -be (Tibwerabe tikadya.), (Ndigonabe ndikamaliza kuwerenga.)
-
o) Kusonyeza kukakamira kuchita ntchito
-
Zitsanzo: -be (Ngakhale ndife ndidyabe nsimayi), (Ndikwatirabe Malitayu ngakhale ndi chindalandala.)
-
p) Kuchulukitsa kapena kulemekeza
-
Zitsanzo: -ni (Gonani apa, agogo), (Khalani pansi ana nonsenu.)