MLOWAM’MALO
Mlowam’malo ndi mawu amene amagwira ntchito m’malo mwa dzina. Awa ndi mitundu ya mlowam’malo ndi zitsanzo zake:
A. Wadzina lakelake
Wam’mawa ukugwira ntchito m’malo mwa dzina la munthu, ndipo alipo wamitundu itatu:
-
Wakalozamwini
-
Amalowa m’malo mwa dzina la munthu yemwe akuyankhulayo.
-
Zitsanzo:
-
Ine ndikwatira mwana wa a Phiri.
-
Ife sitikufuna kudya masambawo.
-
-
-
Wakalozamzako
-
Amaloza mzako amene ukumuona panthawi yoyankhulayo.
-
Zitsanzo:
-
Akufuna iwe mtsikanayu.
-
Inu mulibe chilungamo.
-
-
-
Wakalozawina
-
Amaloza munthu amene panthawi yoyankhulayo palibe.
-
Zitsanzo:
-
Iye anali mphunzitsi wathu.
-
Iwo ankapita kutheba.
-
-
B. Woloza
-
Amathandiza poloza, amagwiritsa ntchito masinde oloza.
-
Zitsanzo:
-
Uyu ndi mnzanga.
-
Adamupha ndi ichi.
-
C. Wofunsa
-
Amathandiza pofunsa, amagwiritsa ntchito masinde ofunsira.
-
Zitsanzo:
-
Zingati mwazionazo?
-
Wotani wabera mayeso?
-
D. Wamgwirizano
-
Amagwiritsa ntchito masinde amgwirizano monga -tere, -mene, ndi -mwe.
-
Zitsanzo:
-
Zotere zimayambitsa chinyengo.
-
Amene wabwera adye.
-
E. Wogawa
-
Amagwiritsa ntchito masinde ogawa monga –li ndi –nse.
-
Zitsanzo:
-
Aliyense wadwala.
-
Tidya chilichonse.
-
F. Waumwini
-
Amasonyeza umwini, amagwiritsa ntchito masinde aumwini.
-
Zitsanzo:
-
Zako zili m’khola lino.
-
Wathu siwochita naye masewera.
-
G. Wowerenga
-
Amathandiza kusonyeza chiwerengero cha zinthu, amagwiritsa ntchito masinde owerengera.
-
Zitsanzo:
-
Mutipatse zisanu zokha.
-
Adatitengera zitatu.
-
H. Wopatula
-
Amasonyeza kuti zinthu zikupatulidwa kuchokera pazinzake.
-
Zitsanzo:
-
Ochepa apita ku Zambo.
-
Ena athawa.
-
I. Wotsimikiza/Otsindika
-
Amatsindika kapena kutsimikiza.
-
Zitsanzo:
-
Iye yemwe adandipereka kwa adani anga.
-
Inu nomwe mwatentha nyumba.
-
J. Wodzichitira
-
Amasonyeza kuti ntchito yabwerera kwa yemwe amayichita.
-
Zitsanzo:
-
Wadzikola wekha.
-
Adadzibaya yekha.
-
NTCHITO ZA ALOWAM’MALO
A. Kukhala mwininkhani
-
Apa ndi pamene mlowam’malo amachita ntchito m’chiganizo.
-
Zitsanzo:
-
Zitatu zadya mfutso wathu.
-
Wanu wapha mbuzi.
-
B. Kukhala pamtherankhani
-
Wachindunji
-
Amachitidwa ntchito m’chiganizo.
-
Zitsanzo:
-
Alinafe waba chochepa.
-
Mbalangwe wapha zonse.
-
-
-
Wopanda chindunji
-
Amachitiridwa ntchito m’chiganizo.
-
Zitsanzo:
-
Kachitsa wagulira awirife mtedza.
-
Gamaliyele wachapira ife zovala.
-
-
-
Wamperekezi
-
Amatsana ndi mperekeziyo.
-
Zitsanzo:
-
Amauluka pa aka.
-
Adabwera ndi zinayi.
-
-
C. Kuyitanira
-
Zitsanzo:
-
Inu, thawani moto.
-
Tenga njingayi, iwe.
-
D. Kukhala mtsirizitsi
-
Amatsirizitsa ganizo la aneni odalira monga –li, si, komanso ndi.
-
Zitsanzo:
-
Chapha nkhuku ndi ichi.
-
Amadwala adali wathu. Makokoto si iwe.
-
Chidule
-
Mlowam’malo umagwira ntchito m’malo mwa dzina, kugwira ntchito zosiyanasiyana monga kulankhulana, kupempha, ndikuwonetsa umwini.