ZIGANIZO
Chiganizo ndi gulu lamawu lokhala ndi mneni ndipo limapereka ganizo lomveka bwino.
Zitsanzo:
- Ali kulandira mankhwala otalikitsa moyo.
- Timakhala ku Blantyre.
MITUNDU YA ZIGANIZO
- Chiganizo chopanda nthambi: Chimakhala ndi mneni m’modzi ndiponso chimakhala ndi ganizo limodzi.
- Zitsanzo: Timadya bwino.
- Chiganizo chanthambi: Chimakhala ndi nthambi yoyima payokha komanso ina yosaima payokha.
- Zitsanzo: Ndizoona kuti ndili ndi pakati.
- Chiganizo chaziganizo: Chimakhala ndi ziganizo zopanda nthambi zingapo zomwe zimalumikizidwa ndi mlumikizi m’modzi.
- Zitsanzo: Adasewera, adavina komanso adachitako ndewu.
- Chiganizo chaziganizo zanthambi: Chimapangidwa ndi ziganizo zanthambi zingapo.
- Zitsanzo: Tagwirizana kuti tikwatirane ngakhale tilibe podalira.
NTHAMBI ZA CHIGANIZO
Nthambi ndi gulu la mawu lomwe limakhala ndi mneni wakewake.
Zitsanzo:
- Popeza ukuchita mwano.
- Tipitako madzulo.
MITUNDU YA NTHAMBI ZACHIGANIZO
- Nthambi yoima payokha: Imapereka ganizo lomveka bwino.
- Zitsanzo: Tipitako madzulo.
- Nthambi yosaima payokha: Simapereka ganizo lomveka ndipo imadalira nthambi yoima payokha.
- Zitsanzo: Popeza ukuchita mwano pamene tinali kudya.
MITUNDU YA NTHAMBI YOSAIMA PAYOKHA
- Yadzina: Imagwira ntchito ngati dzina motere:
- Zitsanzo: Zakuti wapita sindidamve.
- Yamfotokozi: Imakamba zambiri zadzina lomwe lili munthambi yoyima payokha.
- Zitsanzo: Chuma chimene wabacho ufa nacho.
- Yamuonjezi: Imagwira ntchito ngati muonjezi ndipo ili ndi mitundu yotsatirayi:
- Wanthawi: Imasonyeza nthawi yomwe ntchito yachitika.
- Wamalo: Imaonetsa malo amenentchito ikuchitikira.
- Wamchitidwe: Imakamba zamchitidwe wa momwe ntchito yachitikira.
- Wachifukwa: Imasonyeza chifukwa chomwe ntchito yamneni wa munthambi yoima payokha yachitikira.
- Wacholinga: Imasonyeza cholinga chomwe ntchito yamneni wa munthambi yoyima payokha idachitikira.
- Wolabadira: Imasonyeza kulabadira.
- Wapokhapokha: Imasonyeza kuti ntchito ichitika inzake ikakwaniritsidwa.
- Wazotsatira: Imasonyeza zotsatira za ntchito yamneni wamunthambi yoyima payokha.