Malo: Kumudzi kwawo kwa Nthondo, Kwa a Mnjondo
Atengambali:
- Nthondo
- Atsibweni ake a Nthondo
- Amnzake a Nthondo
- Mkazi wa Nthondo
- Apongozi ake a Nthondo
- Mlamu wa Nthondo
- A Mzingwa
- A Chikunje
- A Dzeya
- Mzungu wa Mishoni
- M’phunzitsi
- Ena ambiri
NKHANI YA M’MUTUWU MWACHIDULE
- Anyamata a Nthondo adafika kumudzi kuchokera ku Kabula ndipo anafotokozera anthu zonse zomwe anakumana nazo pa ulendo wawo.
- Nthondo adayamba kukhala kubwalo la akuluakulu kumene ankalangizidwa kuti adzilimbikira ntchito kuti akhale wokhumbirika kwambiri ndi mbeta.
- Chifukwa cha khalidwe labwino, Nthondo adakhoza kusoka mphasa, kusema mipini, kumanga masindwi, ndinso kugamula milandu ing’onoing’ono.
- Atsibweni ake a Nthondo adafuna kumpatsa mkazi Nthondo, koma iyeyo adakana chifukwa mkaziyo adali wamng’ono.
- Nthondo ndi mnzake wina adagwirizana zolekana ndi amnzake chifukwa adali ndi makhalidwe oipa ndinso nsanje.
- Nthondo ndi amnzake adakambirana nkhani zofunsa mbeta mu mphala yawo ndipo adalongosolerana njira zosankhira mkazi wabwino.
- Nthondo ndi amnzake adapita kukafuna mbeta pa mudzi wa a Mnjondo, ndipo Nthondo adapempha madzi kwa mtsikana yemwe adamukondayo.
- Ngakhale atsibweni ake ankafuna kumukaniza, adavomereza atadandawula za umasiye wake.
- Nthondo adalonjeza atsibweni ake kuti akakhalakhala kwawo kwa mkazi, adzatenga chitengwa kuti adzasunge mudzi popeza iyeyo adali m’phwawo yekhayo wa atsibweni ake.
- Atafotokozera amnzake mu mphala, Nthondo adapita kwa alamu ake kukawawuza kuti akamufunsirire mbeta ndipo adagwirizana zoti apiteko tsiku linalo.
- Atafika kwa Mnjondoko, adalandiridwa ndipo adawuzidwa kuti abwerere kaye kuti uthengawo upite kaye kwa amayi ake a mtsikanayo.
- Nthondo ndi alamu ake anabwerera kumudzi kuti akafotokozere anthu, ndipo usiku, Nthondo sadagone chifukwa amangolota mkazi wakeyo.
- Atapitanso adayankhidwa kuti mtsikanayo walola ndi kuti Nthondo apite naye mawa lakelo.
- Pamene amapita tsiku linalo, mlamu wake wa Nthondo adamulangiza Nthondo kuti akakhale ndi makhalidwe abwino ku chikamwiniko.
- Atafika anapereka malonjeza ndipo Nthondoyo adalandiridwa pamudzi wa a Mnjondopo.
- Nthondo adaperekeza alamu akewo kunjira komwe adabwereza kumulangiza, ndipo iye anamva ndi kuwauza kuti akamperekereko moni kwa Mdzitula.
- Atamulozera nyumba yoti azigona, Nthondo ndi mkazi wake anasonkha moto, ndipo mkazi wake wa Nthondo anakatenga nsima ya ndiwo ya nyama ya nkhuku onse ndikudya nyamayo.
- Nthondo adatsanzika kuti apite kwawo ndiwo anampatsa mkanda ndicholinga choti asakakhale kwawo komweko.
- Atafika kumudzi kwawo, Nthondo adapempha nkhuku yoti akawaphere apongozi ake, ndipo mnyamata wina adampatsa nkhukuyo namlangiza kuti aphike.
- Anthu aja anadya ndiwo ija mogawana bwinobwino, ngakhale kuti apongozi ake a Nthondo anapereka nyama yonse poyamba, zinthu zomwe Nthondo sadagwirizane nazo.
- Mkazi wake wa Nthondo atakula chinamwali, anthu am’mudzimo adakonza mwambo wa chinamwali, ndipo anayitana anthu akumudzi kwawo kwa Nthondo pa mwambowo.
- Nthondo adasoka mphasa nazipereka kwa a Mnjondo pokonzekera mwambo wa chinamwaliwo.
- Pamwambowo, anthu adalanga Nthondo ndi mkazi wake, ndipo adawameta.
- Nthondo adayamba kutcha misampha kuti azipha nyama, popeza ndiwo zamasamba zidakola, kotero adayamba kupha nyama zambiri moti anthu ankamukhumbira kamba ka khama lakelo.
- Nthondo ankayambirira kugwira zintchito pokonzekera ulimi, pomwe amnzake ena amamuseka, koma anadzawoneka wa nzeru nthawi yamvula itafika pomwe amnzakewo amatanganidwa.
- Nthondo adayamba kuswa mphanje kamba ka njala, ndipo atalima adakolola zakudya zambiri, choncho apongozi ake adamkonda, ndipo Nthondo adakhala mwa mtendere ndi mkazi wake chifukwa samapsetsana mtima.
- Tsiku lina, Nthondo adafunsa mkazi wake za chitengwa, ndipo mkaziyo adalola mosavuta, choncho Nthondo adapita kwawo nakafotokozera atsibweni ake kuti abwera kudzakhala kwawoko ndi mkazi wake.
- Atsibweni ake a Nthondo adatumiza nkhoswe ya Nthondo kwa a Mnjondo kukapempha chitengwa, ndipo adawalola ngakhale kuti apongozi ake anadandawula kwambiri.
- Nthondo adapita kukakonza kanyumba kwawo, ndipo kenaka adanyamuka limodzi ndi mkazi wake kukakhala kwawo.
- Nthondo adalima mphanje, ndipo chimanga chake chinabereka kwambiri koti anthu amayesa kuti iyeyo adali ndi mankhwala amfumba.
- Nthondo ndi mnzake adagwirizana zokaswa mphanje tsiku linalo, ndipo anapitadi nagawana malowo.
- Akulima adamva phokoso kumudzi, ndipo iwo anapita kumudziko komwe adamvetsedwa kuti kunabwera mzungu.
- Anthu onse am’mudzimo adakondwera powona mzunguyo, ndipo atsibweni ake a Nthondo adapita kukalonjera mzunguyo atanyamula mbuzi yomwe ankayikoka ndi Nthondo.
- Mfumuyo idauzidwa kuti nkhani ayimva madzulo kuchokera kwa Mzunguyo, koma mzunguyo adaitanitsa madzi ndi nkhuni zosinthanitsana ndi mchere.
- A mfumu, A Mzingwa, a chikunja ndi a Dzeye adauzidwa ndi Mzungu kuti iyeyo amafuna kuti abweretse sukulu m’mudzimo, kotero anthuwa adati ayankha mawa lake.
- Atapita pa upo, a Mfumu ndi amnzawo aja adakana sukulu, koma Nthondo adamuwumiriza kuti aivomere sukuluyo, kotero adakavomeradi atapita kwa mzunguyo.
- Atatero, mzunguyo adakondwera, nathokoza, ndipo anatsanzika napita kwawo atasiya kalata yoti akaipereke kwa mzungu wa ku Boma. Anasiyanso thumba la mchere komanso adagawira mabulangeti mfumuzo.
- Tsiku lina, amfumu adasonkhanitsa anthu kuti awafotokozere zolinga za mzunguyo ndi kalata ija, ndipo anthu onse adawalola kuti apititse kalatayo ku Boma kuja.
- Amfumu ndi nduna zawo zija limodzinso ndi Nthondo adapita ndi kalatayo ku Boma, ndipo mzungu wa ku Boma adawafunsa ngati sukuluyo sadzaikana, ndipo atatero adawalamula kuti akamange nyumba yabwino ya sukulu.
- M’mawa lake, mfumuzo zidasonkhanitsa anthu ndi kuwadziwitsa zomwe adawauza mzungu wa ku Boma, kotero anthuwo adayamba kuthandizana pa zintchito zomanga nyumba ya sukulu.
- Tsiku lina, mzunguyo adabwera napeza Nthondo yekha popeza atsibweni ake amakamwa mowa, ndipo adasiya uthenga woti amadzangowona nyumba ija, komanso kuti adzawatumizira m’phunzitsi kenako adakwera pabulu napita.
- Nthondo adawafotokozera zonse atsibweni ake atachoka kumowa kuja.
- Tsiku lina, m’phunzitsi adafika m’mudzimo atavala nsalu zoyera, ndipo anakafikira ku nyumba ya amfumu.
- Anthuwo adakalonjera m’phunzitsiyo, adalandira nawo, ndipo atsibweni ake adakhalabe mu nthawi yopemphera kwa mzunguyo.
- Amfumu adakonda kumva zatsopano zotheka, ndipo Nthondo adachitapo tsopano kuti akhazikitse nyumba ya sukulu.
- Kuthamanga kwa mzungu wa ku Boma kunali ndi zikhumbuzo za akuluakulu a mukapita kumamili alimi, ndiye mwana wamkulu wa a Nthondo akukamanganabe ndi a Mzungu kuwadziwa bwanji.
- M’tsiku lawo, Nthondo adapita ku sukulu poyamba ndipo adangokhala ku makalata a akuluakulu, adalankhula bwanji, ndipo kumapeto kwake anali ndi zithunzi za ubale.
- Akakonda komanso ngati nthawi yotsiriza, akukuonetsani, adakuonekera kuti akukwaniritsa kupambana.
- Pambuyo pake, Nthondo akupanga zopanga, akupanga mfundo pa malangizo omwe ayankha.
- Ndipo panali chisankho chapamwamba kuti akudziwa komanso akuthandiza bwino.
- Nthondo adakula bwino m’masiku akale, pomwe adakanidwa komanso kuthandizidwa.
Nkhani Zofotokozedwa
- Anthu onse akukhala mu chipinda cha akuluakulu a a Mnjondo, ndipo akugawana mawu abwino omwe akufotokozera Nthondo.
- Akaphunzira nthawi ya udindo, atapeza zitsanzo zawo, ndipo ankakhazikika bwino.
- A Mnjondo adakhalapo kuti adzalamulire ngati akukhala kumeneko, ndipo akufunafuna munthu wabwino kuchokera m’chigawo cha a Mnjondo.
- Nthondo akukamba zinthu, akuzizira, pamene adachita mawu akulu a nthawi yanu.
- Kumbukirani kutchuka kwa zitsanzo zovuta mu mzindawu, m’lina pofikira mwa zina.
- Atsibweni ake adakhalabe kugwila gulu ndipo ankafuna kukwaniritsa.
MFUNDO ZIKULUZIKULU ZA M’MUTUWU
a. Zikhulupirilo ndi Miyambo
- Atsibweni a Nthondo adafuna kumupatsa mkazi Nthondo.
- Nthondo ndi alamu ake adakafunsa mbeta kwa a Mnjondo.
- Anthu anachita mwambo wa chinamwali mkazi wake wa Nthondo atatha msinkhu.
- Nthondo anakakhala chikamwini kwa a Mnjondo.
- Nkhoswe ya Nthondo idakapempha chitengwa kwa Mnjondo.
b. Kudalirana
- Nthondo ndi mkazi wake amadalirana pa zintchito m’nyumba mwawo.
- Anthu am’mudzi anadalirana popanga upo wopereka yankho kwa mzungu.
c. Kudalira
- Apongozi a Nthondo ankamudalira mkamwini wawo, Nthondo.
- Mfumu inadalira mfumu zing’onozing’ono pa chiganizo chovomera kapena kukana sukulu.
- Mfumu inadalira anthu ake kuti apereke chivomerezo choti akapereke kalata kwa mzungu wa ku Boma.
- Atsibweni a Nthondo anadalira Nthondo pomuwuza kuti adzasunge mudzi kutsogolo.
d. Kuthandizana
- Anthu am’mudzi anathandizana kumanga nyumba ya sukulu.
- Nthondo ndi mnzake anathandizana maganizo oti akalime mphanje.
- Amfumu ndi mfumu zing’onozing’ono zinathandizana pa nkhani ya kutsegula sukulu m’mudzi mwawo.
e. Chikondi
- Mzungu wa Mishoni adakonda anthu am’mudzi mwa kwawo kwa Nthondo powabweretsera sukulu.
- Mzungu anapereka mabulangete kwa mfumu kusonyeza chikondi.
- Mzungu anapereka thumba la mchere kwa mafumu ndi anthu am’mudzi.
- Mzungu wa mishoni anawabweretsera m’phunzitsi anthu a m’mudzi mwa kwawo kwa Nthondo.
- Anthu am’mudzi anamufunira nyumba ndi chakudya m’phunzitsi wawo.
f. Kulemekeza ufulu wa achinyamata
- Mafumu adalemekeza maganizo a Nthondo oti avomere kutsegula sukulu m’mudzi mwawo.
g. Kulimbikira ntchito
- Nthondo ankatcha misampha kuti apeze ndiwo.
- Nthondo ankalima mphanje kuti athetse njala pakhomo pawo.
- Nthondo ankayambirira kukonzekera ulimi kuti asavutike Nthawi ya dzinja ikafika.
h. Njira zopezera mkazi wabwino
- Mkazi azikhala wantchito osati wosambasamba.
- Mkazi asamakhale mwana wa mtsibweni wako.
- Mkazi azikhala wodziwa kuphika.
MAPHUNZIRO A M’MUTUWU
- Maganizo a achinyamata nawonso amakhala aphindu pobweretsa chitukuko m’dera.
- Kulimbikira ntchito kumapindulitsa.
- Nsanje siyipindula kalikonse.
- Mutu umodzi susenza denga.