Malo
-
Kwawo kwa Nthondo, kwa mfumu yaikulu
Atengambali
-
Nthondo
-
A Dzeya
-
A Chembe
-
A Mzingwa
-
Anthu am’mudzi
-
Anthu a kwa mfumu yaikulu
NKHANI YA M’MUTUWU MWACHIDULE
-
Atsibweni a Nthondo anadwala, ndipo Nthondo anatumidwa kukanena uthenga kwa mfumu yaikulu, koma asanapite, atsibweni akewo anamwalira.
-
Nthondo anatumidwa kukanena uthenga wa malirowo kuchokera kwa mfumu yayikulu, adapeza malirowo ataika kale.
-
Anthu am’mudzimo atasonkhanitsana, akazi (mbumba) adasankha Nthondo kukhala woyenera ufumu.
-
Anaphika mowa ndi kutumiza uthenga kwa mfumu yayikulu kuti adzakhale nawo pa mwambowo.
-
Patapita masiku angapo, mwambowo unachitika, ndipo Nthondo analowa ufumu, anampatsa malangizo osungira mudzi, ndipo anthu onse anamwazikana.
-
A Mzingwa ndi a Dzeya adafuna kumuwuza Nthondo kuti asathetse Mzinda chifukwa choti iyeyo ndi Mkhristu, podabwa kuti maliro akamachitika m’mudzimo, Nthondo samachita Mzinda.
-
Nthondo anakana maganizo a nduna zija, ndipo anaziuza kuti amene sankafuna sukulu achoke m’mudzimo.
-
A Dzeya ndi a Mzingwa anamuyesa Nthondo ngati wachibwana, ndipo anachoka pamalopo mokwiya.
-
Nthondo analimbikitsa anthu am’mudzimo kupita ku sukulu pamodzi ndi ana ake omwe ankawakalipira akajomba kusukulu.
-
Anthu ambiri adayamba kupeza phindu mu sukulu, ndipo ambiri amasandulika a Khristu chifukwa chodziwa za chikondi cha Ambuye Yesu.
-
Nthondo adakhalabe mfumu kwa zaka zingapo, ndipo anjala amawathandiza ndi kuwapatsa chakudya, ndinso otetana (amikangano, ofooka) adawaletsa ndi kuwakhazika mu mtendere.
-
Tsiku lina, Nthondo anadwala chibayo (chilaso), ndipo anthu ambiri anabwera ndi mankhwala awo, koma analephera Nthondo ndi kumwalira.
-
Anthu ambiri anamva chisoni ndi maliro a Nthondo chifukwa cha ntchito zake zabwino.
-
M’phunzitsi adatsiriza ndi pemphero pa mwambo wa malirowo, ndipo anthu ambiri adamuyesa Nthondo ngati mtsogoleri amene adawatengera chokoma m’mudzi mwawo.
MFUNDO ZIKULUZIKULU ZA M’MUTUWU
a. Kudalira
-
A kwawo kwa Nthondo anadalira anthu a kwa mfumu yaikulu pa maliro a atsibweni ake a Nthondo.
-
Anthu am’mudzi anadalira akazi kuti asankhe munthu woyenera kukhala mfumu.
-
Anthu am’mudzi anadalira anthu a kwa Mfumu yaikulu pa mwambo wolonga Nthondo ufumu.
-
A Dzeya ndi a Mzingwa anadalira Nthondo kuti asathetse Mzinda m’mudzimo.
-
Nduna zinadalira Nthondo kukanena uthenga wa maliro kwa mfumu yaikulu.
b. Kudalirana
-
A Dzeya ndi a Mzingwa anadalirana pokamuwuza Nthondo kuti asathetse Mzinda.
c. Miyambo
-
Mwambo wa maliro a atsibweni ake a Nthondo ndinso wa maliro a Nthondo.
-
Mwambo wolonga ufumu Nthondo.
d. Chisoni
-
Anthu anali ndi chisoni pa maliro a atsibweni ake a Nthondo.
-
Anthu anali ndi chisoni pa maliro a Nthondo.
e. Udindo ndi Kuthandiza
-
Nthondo ankathandiza anthu anjala pamene iye adali mfumu.
-
Nthondo ankathandiza anthu otetana.
-
Nthondo ankalimbikitsa anthu kupita ku sukulu.
f. Kudzidalira
-
Nthondo anadzidalira yekha poyankha nduna kuti amene ankafuna mzinda achoke pamudzipo.
g. Malangizo
-
Nthondo adamulangiza za kasungidwe ka mudzi pamene ankamulonga ufumu.
h. Kuthandizana
-
Anthu am’mudzi anathandizana pa matenda ndi maliro a atsibweni ake a Nthondo.
-
Anthu am’mudzi anathandizana pa matenda ndi maliro a Nthondo.
i. Ukhrisitu
-
Anthu ambiri amaphunzira sukulu ndi kusandulika a Khristu.